2 Petro 3 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Petro 3:1-18

Kubwera kwa Ambuye

1Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera. 2Ndikufuna kuti mukumbukire mawu amene anayankhulidwa kale ndi aneneri oyera mtima ndiponso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu analipereka kudzera mwa atumwi.

3Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa. 4Iwo adzati, “Kodi suja Ambuye analonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nʼkale anamwalira makolo athu, koma zinthu zonse zili monga anazilengera poyamba paja.” 5Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi. 6Ndi madzinso achigumula, dziko lapansi la masiku amenewo linawonongedwa. 7Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.

8Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! 9Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

10Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa.

11Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu 12pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. 13Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.

14Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye. 15Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. 16Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.

17Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. 18Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.

Persian Contemporary Bible

دوم پطرس 3:1‏-18

روز خداوند

1‏-2برادران عزيز، اين دومين نامه‌ای است كه به شما می‌نويسم. در هر دو نامه كوشيده‌ام مطالبی را كه از پيش می‌دانستيد، يادآوری نمايم تا فكر پاكتان را روشن سازم، يعنی همان مطالبی را كه از انبيای مقدس و از ما رسولان مسيح آموخته‌ايد، زيرا ما سخنان خداوند و نجات‌دهندهٔ‌مان را به گوش شما رسانديم.

3پيش از هر چيز می‌خواهم اين مطلب را يادآوری كنم كه در زمانهای آخر، اشخاصی پيدا خواهند شد كه به هر كار نادرستی كه به فكرشان می‌رسد، دست زده، حقيقت را به باد تمسخر خواهند گرفت، 4و خواهند گفت: «مگر مسيح وعده نداده كه باز خواهد گشت؟ پس او كجاست؟ اجداد ما نيز به همين اميد بودند، اما مردند و خبری نشد. دنيا از ابتدای پيدايش تا به حال هيچ فرقی نكرده است.» 5‏-6ايشان عمداً نمی‌خواهند اين حقيقت را به ياد آورند كه يک بار خدا جهان را با طوفانی عظيم نابود ساخت، آن هم مدتها بعد از آنكه به فرمان خود آسمانها و زمين را آفريد و از آب برای شكل دادن و احاطه زمين استفاده كرد. 7اكنون نيز به فرمان خدا، آسمان و زمين باقی هستند تا در روز داوری با آتش نابود شوند، يعنی در همان روزی كه بدكاران مجازات و هلاک خواهند شد.

8اما ای عزيزان، اين حقيقت را فراموش نكنيد كه برای خدا يک روز يا هزار سال تفاوتی ندارد. 9بنابراين، مسيح در وعدهٔ بازگشت خود تأخيری بوجود نياورده است، گرچه گاهی اين گونه به نظر می‌رسد. در واقع، او صبر می‌كند و فرصت بيشتری می‌دهد تا گناهكاران توبه كنند، چون نمی‌خواهد كسی هلاک شود. 10به هر حال بدانيد كه روز خداوند حتماً خواهد آمد، آن هم مثل دزدی كه همه را غافلگير می‌كند. در آن روز، آسمانها با صدايی هولناک از بين خواهند رفت، و اجرام آسمانی در آتش نابود شده، زمين و هر چه در آن است، خواهد سوخت.

11پس حال كه می‌دانيد هر چه در اطرافمان هست نابود خواهد شد، چقدر بايد زندگی‌تان پاک و خداپسندانه باشد. 12بايد چشم به راه آن روز باشيد و تلاش كنيد تا آن روز زودتر فرا رسد، روزی كه آسمانها خواهد سوخت و اجرام آسمانی در شعله‌های آتش ذوب شده، نابود خواهند گشت. 13ولی ما با اميد و اشتياق، در انتظار آسمانها و زمين جديد می‌باشيم كه در آنها فقط عدالت و راستی حكمفرما خواهد بود، زيرا اين وعدهٔ خداست.

14پس ای عزيزان، از آنجا كه منتظر اين رويدادها هستيد و چشم به راه بازگشت مسيح می‌باشيد، سخت بكوشيد تا بی‌گناه زندگی كنيد و با همه در صلح و صفا به سر بريد تا وقتی مسيح باز می‌گردد، از شما خشنود باشد.

15‏-16در ضمن بدانيد كه مسيح به اين دليل صبر می‌كند تا ما فرصت داشته باشيم پيام نجاتبخش او را به گوش همهٔ مردم برسانيم. برادر عزيز ما «پولس» نيز با آن حكمتی كه خدا به او داده است، در بسياری از نامه‌های خود دربارهٔ همين مطلب، سخن گفته است. درک برخی از نوشته‌های او دشوار است و بعضی كه اطلاع كافی از كتاب آسمانی ندارند و وضع روحانی‌شان نيز ناپايدار است، آنها را به غلط تفسير می‌كنند، همان كاری كه با بخشهای ديگر كتاب آسمانی نيز می‌كنند. اما با اين كار، نابودی خود را فراهم می‌سازند.

سخنان پايانی پطرس

17برادران عزيز، اين حقايق را از پيش به شما گوشزد می‌كنم تا مراقب خود باشيد و به سوی اشتباهات اين اشخاص بدكار كشيده نشويد، مبادا شما نيز از راه راست منحرف گرديد. 18در قدرت روحانی رشد كنيد و در شناخت خداوند و نجات دهنده‌مان عيسی مسيح ترقی نماييد، كه هر چه جلال و شكوه و عزت هست، تا ابد برازندهٔ اوست. آمين.