2 Mbiri 34 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 34:1-33

Yosiya Akonzanso Chipembedzo

1Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 31. 2Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndi kutsata makhalidwe a Davide abambo ake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.

3Mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ulamuliro wake, iye akanalibe wamngʼono, anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide abambo ake. Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri iye anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu kuchotsa malo azipembedzo, mafano a Asera, milungu yosema ndi mafano owumbidwa. 4Maguwa ansembe a Baala anagwetsedwa iye atalamulira. Anadula zidutswazidutswa maguwa ofukizira lubani amene anali pamwamba pake, ndipo anaphwanya mafano a Asera, milungu ndi zifaniziro zake. Anaziperapera ndipo anaziwaza pamwamba pa manda a amene ankapereka nsembe kwa mafanowo. 5Iye anatentha mafupa a ansembe pa maguwa awo, kotero iye anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu. 6Ku mizinda ya Manase, Efereimu ndi Simeoni mpaka kufika ku Nafutali, ndiponso malo a mabanja owazungulira, 7iye anagwetsa maguwa ansembe ndi mafano a Asera ndi kuphwanyaphwanya milungu yawo kukhala fumbi ndi kuduladula maguwa ofukizapo lubani mʼdziko lonse la Israeli. Atatero, anabwerera ku Yerusalemu.

8Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya, atayeretsa dziko ndi Yerusalemu, Yosiya anatuma Safani mwana wa Azariya ndi Maaseya, wolamulira mzinda pamodzi ndi Yowa mwana wa Yowahazi mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Yehova Mulungu wake.

9Iwo anapita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe ndipo anamupatsa ndalama zimene zinaperekedwa mʼNyumba ya Mulungu, zimene Alevi amene anali alonda apakhomo analandira kuchokera kwa anthu a ku Manase, Efereimu ndi onse otsala a ku Israeli ndiponso anthu onse ochokera ku Yuda ndi Benjamini ndi okhala mu Yerusalemu. 10Ndipo anazipereka mʼmanja mwa anthu amene anasankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Anthu amenewa ankalipira antchito amene ankakonzanso Nyumba ya Mulungu. 11Iwo anaperekanso ndalama kwa amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba kuti agule miyala yosema ndi matabwa a phaso la nyumba ndi nsichi zomangira zomwe mfumu ya Yuda inalekerera kuti zigwe ndi kuwonongeka.

12Anthuwa anagwira ntchitoyi mokhulupirika. Amene ankawayangʼanira anali Yahati ndi Obadiya, Alevi ochokera ku banja la Merari, ndi Zekariya ndi Mesulamu ochokera ku banja la Kohati. Alevi onse amene anali aluso loyimbira zida za nyimbo 13ankayangʼanira anthu onyamula katundu, namatsogolera anthu onse amene ankagwira ntchito iliyonse yotumikira. Alevi ena anali alembi, akapitawo ndiponso alonda apamakomo.

Buku la Malamulo Lipezeka

14Pa nthawi imene ankatulutsa ndalama zimene anabwera nazo ku Nyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya anapeza Buku la Malamulo limene linaperekedwa kudzera mwa Mose. 15Hilikiya anati kwa Safani, mlembi wa zochitika, “Ine ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Iye analipereka kwa Safani.

16Ndipo Safani anapita nalo bukulo kwa mfumu ndi kumufotokozera kuti: “Akuluakulu anu akuchita zonse zimene zinapatsidwa kwa iwo. 17Iwo alipira ndalama zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo azipereka kwa akapitawo ndi anthu antchito.” 18Kenaka Safani, mlembi wa zochitika anawuza mfumu, “Wansembe, Hilikiya wandipatsa ine buku ili.” Ndipo Safani anawerenga bukulo pamaso pa mfumu.

19Mfumu itamva mawu a Buku la Malamulo, inangʼamba mkanjo wake. 20Iye analamula izi kwa Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi wa zochitika ndi Asaya mtumiki wa mfumu: 21“Pitani ndipo mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa otsala a Israeli ndi Yuda za zimene zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu umene watsanulidwa pa ife chifukwa makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite motsatira zonse zimene zalembedwa mʼbuku ili.”

22Hilikiya pamodzi ndi anthu amene anawatuma aja, anapita kukayankhula ndi mneneri wamkazi Hulida, amene anali mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira, wosunga zovala zaufumu. Hulida ankakhala mu Yerusalemu, mʼdera lachiwiri la mzindawo.

23Iye anati kwa anthuwo, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, muwuzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti, 24‘Yehova akunena kuti, Ine ndidzabweretsa mavuto pamalo pano ndi pa anthu ake, matemberero onse amene alembedwa mʼbukuli amene awerengedwa pamaso pa mfumu ya Yuda. 25Chifukwa iwo anasiya Ine ndi kufukiza lubani kwa milungu ina ndi kuwutsa mkwiyo wanga ndi zonse zimene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzatsanulidwa pamalo pano ndipo sudzazimitsidwa.’ 26Uzani mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova Mulungu wa Israeli, ‘Chimene Yehova, Mulungu wa Israeli akunena mokhudzana ndi mawu amene mwamva ndi ichi: 27Pakuti mtima wako walapa, ndipo wadzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu pamene unamva zimene Iye ananena motsutsa malo ano ndi anthu ake, ndipo chifukwa iwe unadzichepetsa wekha pamaso pa Ine ndi kungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, atero Yehova. 28Tsono Ine ndidzakutengera kwa makolo ako, ndipo udzayikidwa mʼmanda mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene Ine ndidzabweretsa pa malo ano ndi pa iwo amene amakhala pano.’ ”

Choncho iwo anatenga yankho lakelo ndi kubwerera kwa mfumu.

29Ndipo mfumu inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu. 30Iye anapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu a Yuda, anthu a mu Yerusalemu, ansembe ndi Alevi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Iye anawerenga pamaso pawo mawu onse a Buku la Chipangano, limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova. 31Mfumu inayimirira pa chipilala chake ndipo inachitanso pangano pamaso pa Yehova: kutsatira Yehova, ndi kusunga malamulo ake, machitidwe ake ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndi kumvera mawu a pangano olembedwa mʼbukulo.

32Tsono Yosiya anawuza aliyense amene anali mu Yerusalemu ndi Benjamini kuti azisunga panganoli. Anthu a mu Yerusalemu anachita izi motsata pangano la Mulungu, Mulungu wa makolo awo.

33Yosiya anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse limene linali la Aisraeli ndipo anawuza onse amene anali mu Israeli kutumikira Yehova Mulungu wawo. Pa masiku onse a moyo wake, iye sanaleke kutsatira Yehova, Mulungu wa makolo awo.

Slovo na cestu

2 Letopisu 34:1-33

1V osmi letech byl Joziáš, když kralovati počal, a kraloval jedno a třidceti let v Jeruzalémě. 2Ten činil to, což jest pravého před očima Hospodinovýma, chodě po cestách Davida otce svého, a neuchýlil se na pravo ani na levo. 3Léta zajisté osmého kralování svého, když ještě mládenček byl, počal hledati Boha Davida otce svého, dvanáctého pak léta počal vyčišťovati Judy a Jeruzaléma od výsostí, hájů, rytin a slitin. 4Nebo u přítomnosti jeho rozbořili oltáře Bálů, i obrazy slunečné, kteříž byli na nich, zpodtínal. Též i háje a rytiny, i slitiny zdrobil a setřel, a rozsypal po hrobích těch, kteříž jim obětovávali. 5Kosti pak kněží popálil na oltářích jejich, a vyčistil Judu a Jeruzalém, 6Též i města v pokolení Manasses, Efraim a Simeon, až i Neftalím i pustiny jejich vůkol. 7A tak zkazil oltáře a háje, a rytiny stroskotal na kusy, a všecky obrazy slunečné vysekal po vší zemi Izraelské. Potom navrátil se do Jeruzaléma. 8Léta pak osmnáctého kralování svého, když vyčistil zemi a dům Boží, poslal Safana syna Azaliášova, a Maaseiáše úředníka města, aJoacha syna Joachazova kanclíře, aby opraven byl dům Hospodina Boha jeho. 9Kteříž přišedše k Helkiášovi knězi nejvyššímu, dali peníze snesené do domu Božího, kteréž byli Levítové vrátní vybrali od Manassesa a Efraima, i ode všech ostatků Izraelských, i od všeho Judy a Beniamina, a navrátili se do Jeruzaléma. 10Dali je pak v ruce správců toho díla, kteříž představeni byli nad domem Hospodinovým, a ti vydávali je dělníkům, jenž dělali v domě Hospodinově, opravujíce a utvrzujíce jej. 11I dali tesařům a stavitelům, aby najednali kamení tesaného, a dříví k vazbám i k trámům domů, kteréž byli zbořili králové Judští. 12Muži pak ti věrně se měli při té práci, nad nimiž ustanoveni Jachat a Abdiáš Levítové z synů Merari, Zachariáš a Mesullam z synů Kahat, aby s pilností přídrželi k práci. A z těch Levítů každý uměl hráti na nástroje muzické. 13Ale nad nosiči, i kteříž přídrželi dělníky ke všeliké práci, byli z Levítů písaři, úředníci a vrátní. 14A když vynášeli peníze, kteréž byli sneseny do domu Hospodinova, našel Helkiáš kněz knihu zákona Hospodinova vydaného skrze Mojžíše. 15I řekl Helkiáš k Safanovi písaři: Knihu zákona nalezl jsem v domě Hospodinově. I dal Helkiáš tu knihu Safanovi. 16Safan pak přinesl tu knihu králi, a při tom jemu oznámil, řka: Všecko, cožkoli bylo poručeno služebníkům tvým, dělají. 17Nebo sebravše peníze, což se jich koli nalezlo v domě Hospodinově, vydali je v ruce úředníkům a dělníkům. 18Oznámil také Safan písař králi, řka: Knihu mi dal Helkiáš kněz. I četl v ní Safan před králem. 19Pročež když slyšel král slova zákona, roztrhl roucho své. 20A rozkázal král Helkiášovi, též Achikamovi synu Safanovu, a Abdonovi synu Míchovu, a Safanovi písaři, a Asaiášovi služebníku královskému, řka: 21Jděte, poraďte se s Hospodinem o mne i o pozůstalý lid Izraelský a Judský, z strany slov knihy této, kteráž jest nalezena; nebo veliký jest hněv Hospodinův, kterýž jest vylit na nás, proto že neostříhali otcové naši slova Hospodinova, aby činili všecko, což psáno jest v knize této. 22Tedy šli, Helkiáš a kteříž byli při králi, k Chuldě prorokyni, manželce Salluma syna Tekue, syna Chasrova, strážného nad rouchem, nebo bydlila v Jeruzalémě na druhé straně, a mluvili k ní ty věci. 23Kteráž řekla jim: Toto praví Hospodin Bůh Izraelský: Povězte muži tomu, kterýž poslal vás ke mně, 24Takto praví Hospodin: Aj, já uvedu zlé věci na toto místo a na obyvatele jeho, všecka zlořečení napsaná v knize té, kterouž čtli před králem Judským, 25Proto že opustili mne a kadili bohům cizím, aby mne popouzeli všemi skutky rukou svých. Z té příčiny vylita bude prchlivost má na toto místo, aniž bude uhašena. 26Králi pak Judskému, kterýž poslal vás, abyste se tázali Hospodina, takto povíte: Toto praví Hospodin Bůh Izraelský o slovích těch, kteráž jsi slyšel: 27Poněvadž obměkčeno jest srdce tvé, a ponížil jsi se před tváří Boží, kdyžs slyšel slova jeho proti místu tomuto a proti obyvatelům jeho, a ponižuje se přede mnou, roztrhl jsi roucho své, a plakals přede mnou, i já vyslyšel jsem tě, praví Hospodin. 28Aj, já připojím tě k otcům tvým, a pochován budeš v hrobích svých v pokoji, aby neviděly oči tvé ničeho z toho zlého, kteréž já uvedu na místo toto a na obyvatele jeho. I oznámili králi tu řeč. 29Tedy poslav král, shromáždil všecky starší Judské a Jeruzalémské. 30A vstoupil král do domu Hospodinova, a všickni muži Judští i obyvatelé Jeruzalémští, kněží, Levítové a všecken lid od velikého až do malého, i četl, aby všickni slyšeli všecka slova knihy smlouvy, kteráž byla nalezena v domě Hospodinově. 31Potom stoje král na místě svém, učinil smlouvu před Hospodinem, že bude následovati Hospodina, a ostříhati přikázaní jeho i svědectví jeho a ustanovení jeho z celého srdce svého a ze vší duše své, a plniti slova smlouvy té, kteráž jsou v té knize zapsána. 32I rozkázal, aby k témuž každý stál, kdož by koli nalezen byl v Jeruzalémě a v Beniaminovi. I činili obyvatelé Jeruzalémští podlé smlouvy Boží, Boha otců svých. 33Tehdáž také vyprázdnil Joziáš všecky ohavnosti ze všech zemí synů Izraelských, a přídržel všecky, kteřížkoli byli v Izraeli, k tomu, aby sloužili Hospodinu Bohu svému. Po všecky dny jeho neodstoupili od následování Hospodina Boha otců svých.