2 Mbiri 28 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 28:1-27

Ahazi Mfumu ya Yuda

1Ahazi anali ndi zaka makumi awiri pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Iye sanachite zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide kholo lake. 2Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo anawumbanso mafano a chipembedzo cha Abaala. 3Iye amapsereza nsembe ku chigwa cha Hinomu, ndipo anaperekanso ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza kutsatira njira zonyansa za mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli. 4Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzerapo mafano, pamwamba pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu.

5Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wake anamupereka mʼmanja mwa mfumu ya Aramu. Aaramu anamugonjetsa ndipo anagwira ukapolo anthu ake ambiri napita nawo ku Damasiko.

Yehova anamuperekanso mʼmanja mwa mfumu ya Israeli, imene inamuzunza ndi kumuphera anthu ake ambiri. 6Pa tsiku limodzi, Peka mwana wa Remaliya anapha asilikali 120,000 mu Yuda chifukwa Yuda anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo. 7Zikiri msilikali wa ku Efereimu, anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu woyangʼanira nyumba yaufumu, ndi Elikana wachiwiri kwa mfumu. 8Aisraeli anagwira ukapolo abale awo, akazi, ana aamuna ndi ana aakazi okwanira 200,000. Iwo anafunkhanso katundu wambiri amene anapita naye ku Samariya.

9Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi, ndipo anapita kukakumana ndi gulu lankhondo pamene linabwerera ku Samariya. Iye anawawuza kuti, “Chifukwa Yehova, Mulungu wa makolo anu anakwiyira Ayuda, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Koma inu mwawapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba. 10Ndipo tsopano mukufuna kuti amuna ndi akazi a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akhale akapolo anu. 11Tsono mvereni! Abwezeni abale anu amene mwawagwira ukapolo, pakuti mkwiyo wa Yehova uli pa inu.”

12Tsono atsogoleri ena a ku Efereimu, Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilayi anatsutsana nawo amene ankachokera ku nkhondo kuja. 13Iwo anati, “Musabweretse akapolowo kuno, pakuti ife tidzakhala olakwa pamaso pa Yehova. Kodi mukufuna kuwonjezera pa machimo athu ndi kulakwa kwathu? Pakuti zolakwa zathu ndi zambiri kale ndipo mkwiyo wake woopsa uli pa Israeli.”

14Kotero asilikali aja anawasiya akapolowo pamodzi ndi katundu amene analanda ku nkhondo pamaso pa akuluakulu ndi gulu lonse la anthu. 15Anthu amene atchulidwa mayina aja anatenga akapolowo, ndipo kuchokera pa zolanda ku nkhondo, anawaveka onse amene anali maliseche. Anawapatsa zovala ndi nsapato, chakudya ndi chakumwa ndi mankhwala. Onse amene anali ofowoka anawakweza pa abulu. Choncho anabwera nawo kwa abale awo ku Yeriko, Mzinda wa Migwalangwa, ndipo kenaka anawabweza ku Samariya.

16Pa nthawi imeneyo mfumu Ahazi inatumiza mawu kwa mfumu ya ku Asiriya kupempha chithandizo. 17Ankhondo a ku Edomu anabweranso ndi kuthira nkhondo Yuda ndi kugwira akapolo. 18Pamenepo nʼkuti Afilisti atathira nkhondo mizinda ya mʼmbali mwa phiri ndi ku Negevi ku Yuda. Iwo analanda mizindayo nakhala ku Beti-Semesi, Ayaloni ndi Gederoti, komanso Soko, Timna ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. 19Yehova anapeputsa Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi ya Israeli, pakuti analimbikitsa zoyipa ku Yuda ndipo anali munthu wosakhulupirika kwambiri pamaso pa Yehova. 20Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera kwa iye, ndipo anabweretsa mavuto mʼmalo momuthandiza. 21Ahazi anatenga zinthu zochokera mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba yaufumu ndi kwa atsogoleri ndipo anazipereka kwa mfumu ya ku Asiriya, koma zimenezo sizinamuthandize.

22Pa nthawi yake yamavutoyi mfumu Ahazi inapitirira kukhalabe yosakhulupirika pamaso pa Yehova. 23Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse.

24Ahazi anasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse kuchokera mʼNyumba ya Mulungu ndipo anazitenga. Iye anatseka zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anayimika maguwa ansembe pa ngodya iliyonse ya msewu mu Yerusalemu. 25Mu mzinda uliwonse wa Yuda anamangamo malo achipembedzo, operekerapo nsembe zopsereza kwa milungu ina ndipo anaputa mkwiyo wa Yehova, Mulungu wa makolo ake.

26Zochitika zina pa ulamuliro wake ndi machitidwe ake onse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 27Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sanamuyike mʼmanda a mafumu a Israeli. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Slovo na cestu

2 Letopisu 28:1-27

1Ve dvadcíti letech byl Achas, když počal kralovati, a šestnácte let kraloval v Jeruzalémě, a nečinil toho, což pravého bylo před očima Hospodinovýma, jako David otec jeho. 2Ale chodil po cestách králů Izraelských, nýbrž nadělal také slitin modlářských. 3Přesto i sám kadíval v údolí Benhinnom, a pálil syny své ohněm podlé ohavností pohanů, kteréž vyhnal Hospodin před syny Izraelskými. 4A obětoval i kadíval na výsostech a na pahrbcích, i pod každým stromem zeleným. 5Protož dal jej Hospodin Bůh jeho v ruku krále Syrského. Kteříž porazivše jej, zajali odtud množství veliké, a přivedli je do Damašku. Nad to i v ruku krále Izraelského dán jest, kterýž porazil jej porážkou velikou. 6Nebo pomordoval Pekach syn Romeliášův v Judstvu sto a dvadcet tisíců dne jednoho, vše mužů udatných, proto že opustili Hospodina Boha otců svých. 7Zabil také Zichri, rytíř Efraimský Maaseiáše syna králova, a Azrikama, správce domu jeho, a Elkána, druhého po králi. 8Nadto zajali též synové Izraelští z bratří svých dvakrát sto tisíc žen, synů a dcer, ano i kořistí mnoho nabrali od nich, a vezli loupež do Samaří. 9Byl pak tu prorok Hospodinův, jménem Oded, kterýž vyšed proti vojsku přicházejícímu do Samaří, řekl jim: Hle, rozhněvav se Hospodin Bůh otců vašich na Judské, vydal je v ruku vaši, a vy jste je pomordovali v prchlivosti, kteráž až k nebi dosáhla. 10A ještě Judské a Jeruzalémské myslíte sobě podrobiti za pacholky a děvky. Zdaliž i vy, i vy, jste bez hříchů proti Hospodinu Bohu vašemu? 11A protož nyní poslechněte mne, a doveďte zase zajaté, kteréž jste zajali z bratří svých; nebo jinak hněv prchlivosti Hospodinovy bude proti vám. 12Tedy povstali někteří z předních synů Efraimových: Azariáš syn Jochananův, Berechiáš syn Mesillemotův, Ezechiáš syn Sallumův, a Amaza syn Chadlaiův proti těm, kteříž se vracovali z té vojny. 13A řekli jim: Nepřivedete sem těch zajatých; nebo vinu proti Hospodinu myslíte na nás uvesti, přivětšujíce hříchů našich a provinění našich. Veliký tě zajisté hřích náš a prchlivost hněvu proti Izraelovi. 14Takž nechali vojáci těch zajatých i kořistí svých před knížaty a vším shromážděním. 15A přičinivše se muži někteří ze jména znamenaní, vzali ty zajaté, a všecky, kteřížkoli z nich nebyli odění, přiodíli je z těch kořistí. A když je zobláčeli a zobouvali, nakrmili i napojili, ano i pomazali, a zprovodili na oslích, každého nemocného z nich, a dovedli ho do Jericha města palmového k bratřím jejich, potom navrátili se do Samaří. 16Toho času poslal král Achas k králům Assyrským, aby mu pomoc dali. 17Nebo ještě přitáhli i Idumejští, a zbili některé z Judských, a jiné zajali. 18Nadto i Filistinští učinili vpád do měst, na rovinách k straně polední Judstva, a vzali Betsemes a Aialon, a Gederot a Socho i vsi jeho, a Tamna i vsi jeho, a Gimzo i vsi jeho, a bydlili v nich. 19Tak zajisté ponižoval Hospodin Judy pro Achasa krále Izraelského, proto že odvrátil Judu, aby naprosto převráceně činil proti Hospodinu. 20A tak přitáhl k němu Tiglatfalazar král Assyrský, a více ho ssužoval, nežli mu pomáhal. 21A ačkoli Achas vzal z domu Hospodinova a domu královského, i od knížat, a dal králi Assyrskému, však nedal jemu pomoci. 22V který pak koli čas byl ssužován, tím větší převrácenost páchal proti Hospodinu. Takový byl král Achas. 23Nebo obětoval bohům Damašským, kteříž ho porazili, a řekl: Poněvadž bohové králů Syrských pomáhají jim, těm obětovati budu, aby mně pomáhali. Ale oni byli ku pádu jemu, ano i všemu Izraeli. 24Pročež shromáždiv Achas nádoby domu Božího, osekal je, a zamkl dvéře domu Hospodinova, a nadělal sobě oltářů při každém úhlu v Jeruzalémě. 25Ano i v každém městě Judském zdělal výsosti, aby kadil bohům cizím, a tak popouzel k hněvu Hospodina Boha otců svých. 26O jiných pak věcech jeho, a o všech cestách jeho, prvních i posledních zapsáno jest v knize králů Judských a Izraelských. 27I usnul Achas s otci svými, a pochovali jej v městě Jeruzalémě; nebo nevložili ho do hrobů králů Izraelských. I kraloval Ezechiáš syn jeho místo něho.