Eliya Atengedwa Kupita Kumwamba
1Yehova ali pafupi kutenga Eliya kupita kumwamba mu kamvuluvulu, Eliya ndi Elisa anali pa ulendo wopita ku Giligala. 2Eliya anawuza Elisa kuti, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Beteli.”
Koma Elisa anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Beteli.
3Ana a aneneri a ku Beteli anabwera kwa Elisa namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”
Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma musakambe zimenezi.”
4Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yeriko.”
Koma Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Yeriko.
5Ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa, namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”
Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma inu musakambe zimenezi.”
6Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yorodani.”
Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapitirira ulendo wawo.
7Anthu makumi asanu mwa ana a aneneri anawatsatira nayima chapatali moyangʼanana nawo ndipo Eliya ndi Elisa anayima mʼmphepete mwa Yorodani. 8Eliya anatenga chovala chake nachipinda, napanda madzi ndi chovalacho. Madziwo anagawikana, ena kwina ena kwina, ndipo awiriwo anawoloka powuma.
9Atawoloka, Eliya anati kwa Elisa, “Ndifotokozere, ndikuchitire chiyani ndisanachotsedwe pamaso pako?”
Elisa anayankha kuti, “Ndikupemphani kuti mundipatse magawo awiri a mphamvu za mzimu wanu wa uneneri.”
10Eliya anati, “Wapempha chinthu chapatali, komabe ukandiona pamene ndikuchotsedwa pamaso pako, mphamvu wapemphayi idzakhala yako, koma ukapanda kundiona sizidzachitika.”
11Akuyenda ndi kumakambirana, mwadzidzidzi galeta lamoto ndi akavalo amoto anaonekera ndi kuwasiyanitsa awiriwo, ndipo Eliya anapita kumwamba mʼkamvuluvulu. 12Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati.
13Iye anatola chovala cha Eliya chomwe chinagwa nabwerera ndi kukayima mʼmphepete mwa Yorodani. 14Ndipo Elisa anatenga chovala chomwe chinagwa kuchokera kwa Eliya napanda nacho madzi. Iye anafunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wa Eliya?” Atapanda madzi, madziwo anagawika pakati, ena kwina ena kwina, ndipo iye anawoloka.
15Ndipo ana a aneneri ochokera ku Yeriko atamuona anati, “Mzimu wa Eliya wakhazikika pa Elisa.” Ndipo anapita kukakumana naye nagwada ndi kuweramitsa mitu yawo pansi pamaso pake. 16Ndipo anawuza Elisa kuti, “Ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Aloleni apite kuti akafunefune mbuye wanu. Mwina Mzimu wa Yehova wamutenga ndi kukamuponya ku phiri lina kapena ku chigwa china.”
Elisa anayankha kuti, “Ayi, musawatume.”
17Koma anamukakamizabe mpaka Elisayo anachita manyazi moti sakanatha kukana. Choncho iye anati, “Atumizeni.” Ndipo anatumiza anthu makumi asanu amene anakafunafuna Eliya kwa masiku atatu koma sanamupeze. 18Atabwerera kwa Elisa (chifukwa anali akanali ku Yeriko), iye anawawuza kuti, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musapite?”
Kuchiritsidwa kwa Madzi
19Anthu a mu mzindamo anati kwa Elisa, “Mbuye wathu, taonani mzinda uno uli pamalo pabwino, monga mukuoneramu, koma madzi ake ndi oyipa, nthaka yakenso ndi yosabereka.”
20Iye anati, “Patseni mbale yatsopano ndipo muyikemo mchere.” Ndipo anabweretsa mbaleyo kwa iye.
21Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, “Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ ” 22Kotero madziwo ndi abwino mpaka lero, molingana ndi mawu amene Elisa anayankhula.
Kusekedwa kwa Elisa
23Kuchokera kumeneko Elisa anapita ku Beteli. Ndipo pamene ankayenda mu msewu, anyamata ena achichepere anatuluka mu mzindamo nʼkumamuseka. Iwo ankanena kuti, “Choka iwe, wachidazi! Choka iwe wachidazi” 24Iye anatembenuka nawayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Nthawi yomweyo panatulukira zimbalangondo ziwiri kuchokera kuthengo, ndi kuphapo anyamata 42. 25Ndipo iye anapita ku phiri la Karimeli. Pochoka kumeneko anabwerera ku Samariya.