1 Yohane 5 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yohane 5:1-21

Chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu

1Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake. 2Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake. 3Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa, 4chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi. 5Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.

6Uyu ndiye anabwera mwa madzi ndi magazi, ndiye Yesu Khristu. Sanabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi magazi. Ndipo ndi Mzimu Woyera amene akuchitira umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndi choonadi. 7Pakuti pali atatu amene amachitira umboni. 8Mzimu Woyera, madzi ndi magazi; ndipo atatu amavomerezana. 9Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake. 10Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake. 11Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. 12Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.

Mawu Otsiriza

13Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha. 14Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera. 15Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.

16Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi. 17Chilichonse chosalungama ndi tchimo ndipo pali tchimo losadzetsa imfa.

18Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze. 19Tikudziwa kuti ndife ana a Mulungu ndi kuti dziko lonse lapansi lili pansi pa ulamuliro wa woyipayo. 20Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha.

21Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

New International Version

1 John 5:1-21

Faith in the Incarnate Son of God

1Everyone who believes that Jesus is the Christ is born of God, and everyone who loves the father loves his child as well. 2This is how we know that we love the children of God: by loving God and carrying out his commands. 3In fact, this is love for God: to keep his commands. And his commands are not burdensome, 4for everyone born of God overcomes the world. This is the victory that has overcome the world, even our faith. 5Who is it that overcomes the world? Only the one who believes that Jesus is the Son of God.

6This is the one who came by water and blood—Jesus Christ. He did not come by water only, but by water and blood. And it is the Spirit who testifies, because the Spirit is the truth. 7For there are three that testify: 8the5:7,8 Late manuscripts of the Vulgate testify in heaven: the Father, the Word and the Holy Spirit, and these three are one. 8 And there are three that testify on earth: the (not found in any Greek manuscript before the fourteenth century) Spirit, the water and the blood; and the three are in agreement. 9We accept human testimony, but God’s testimony is greater because it is the testimony of God, which he has given about his Son. 10Whoever believes in the Son of God accepts this testimony. Whoever does not believe God has made him out to be a liar, because they have not believed the testimony God has given about his Son. 11And this is the testimony: God has given us eternal life, and this life is in his Son. 12Whoever has the Son has life; whoever does not have the Son of God does not have life.

Concluding Affirmations

13I write these things to you who believe in the name of the Son of God so that you may know that you have eternal life. 14This is the confidence we have in approaching God: that if we ask anything according to his will, he hears us. 15And if we know that he hears us—whatever we ask—we know that we have what we asked of him.

16If you see any brother or sister commit a sin that does not lead to death, you should pray and God will give them life. I refer to those whose sin does not lead to death. There is a sin that leads to death. I am not saying that you should pray about that. 17All wrongdoing is sin, and there is sin that does not lead to death.

18We know that anyone born of God does not continue to sin; the One who was born of God keeps them safe, and the evil one cannot harm them. 19We know that we are children of God, and that the whole world is under the control of the evil one. 20We know also that the Son of God has come and has given us understanding, so that we may know him who is true. And we are in him who is true by being in his Son Jesus Christ. He is the true God and eternal life.

21Dear children, keep yourselves from idols.