Mawu a Moyo
1Tikukulalikirani za Mawu a moyo amene analipo kuyambira pachiyambi, amene tinawamva, amene tinawaona ndi maso athu, amene tinawapenyetsetsa, ndipo tinawakhudza ndi manja athu. 2Moyowo unaoneka, tinawuona ndipo tikuchitira umboni. Tikukulalikirani za moyo wosatha umene unali ndi Atate ndipo unaonekera kwa ife. 3Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu. 4Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu.
Kuyenda mu Kuwunika
5Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse. 6Tikanena kuti timayanjana naye, koma nʼkumayendabe mu mdima, tikunama ndipo sitikuchita choonadi. 7Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Kuwulula Machimo ndi Kukhululukidwa
8Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi. 9Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse. 10Ife tikanena kuti sitinachimwe, tikumutenga Mulungu kukhala wonama, ndipo Mawu ake sali mwa ife.