1 Timoteyo 2 – CCL & NVI

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Timoteyo 2:1-15

Malangizo Achipembedzo

1Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika. 2Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima. 3Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu, 4amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi. 5Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu. 6Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera. 7Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.

8Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.

9Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali. 10Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.

11Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu. 12Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete. 13Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava. 14Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa. 15Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.

Nueva Versión Internacional

1 Timoteo 2:1-15

Instrucciones sobre la adoración

1Así que recomiendo, ante todo, que se presenten ante Dios con peticiones, oraciones, súplicas y den gracias por todos. 2Hagan esto especialmente por los gobernantes y por todas las autoridades, para que tengamos paz y tranquilidad y llevemos una vida respetable y de obediencia a Dios. 3Para Dios nuestro Salvador esto es bueno y agradable, 4pues él quiere que todos sean salvos y lleguen a conocer la verdad. 5Porque hay un solo Dios y solo hay uno que puede ponernos en paz con Dios, y ese es Jesucristo. Él es el hombre 6que dio su vida para salvarnos a todos. Dios, a su debido tiempo, nos demostró que desea salvarnos. 7Por eso me nombró predicador y apóstol de ese mensaje. Digo la verdad y no miento: Dios me hizo maestro de los no judíos para enseñarles la verdadera fe.

8Quiero, pues, que en todas partes los hombres oren, levantando las manos al cielo con un corazón sincero, sin enojos ni peleas.

9En cuanto a las mujeres, quiero que ellas se vistan decentemente y con sencillez. Que no lo hagan para impresionar, con peinados exagerados, con oro, perlas y vestidos costosos. 10Que se adornen más bien con buenas obras, como corresponde a mujeres que dicen servir a Dios.

11La mujer debe aprender en silencio y ser obediente. 12No permito que la mujer enseñe al hombre y tenga autoridad sobre él. Debe mantenerse quieta y en silencio. 13Porque Dios primero creó a Adán, y luego a Eva. 14Además, Adán no fue el engañado por la serpiente, sino la mujer; y ella, una vez engañada, cometió pecado. 15Pero la mujer se salvará siendo madre y manteniendo su fe en Cristo, y si continúa mostrando amor y santidad.