1 Samueli 30 – The Word of God in Contemporary Chichewa CCL

The Word of God in Contemporary Chichewa

1 Samueli 30:1-31

Davide Amenyana ndi Aamaleki

1Pa tsiku lachitatu, Davide ndi anthu ake anakafika ku Zikilagi. Tsono anapeza Aamaleki atawononga kale dera la Negevi ndi Zikilagi. Anathira nkhondo mzinda wa Zikilagi ndi kuwutentha ndi moto. 2Anatenga akazi ndi onse amene anali mʼmenemo akuluakulu ndi angʼono omwe kuti akakhale akapolo. Sanaphe aliyense koma anawatenga amoyo napita nawo.

3Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo. 4Kotero Davide ndi anthu ake analira mofuwula mpaka analibenso mphamvu zolirira. 5Akazi awiri a Davide, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli anatengedwanso. 6Davide anavutika kwambiri mu mtima mwake chifukwa anthu amakamba zoti amuponye miyala popeza aliyense anali ndi chisoni pokumbukira ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anapeza mphamvu mwa Yehova Mulungu wake.

7Kenaka Davide anawuza wansembe Abiatara, mwana wa Ahimeleki kuti, “Ndipatse efodi ija.” Abiatara anabwera nayo efodiyo. 8Tsono Davide anapempha nzeru kwa Yehova nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondoli? Kodi ndidzawapambana?”

Yehova anayankha kuti, “Litsatire, iwe udzawapambana ndithu ndipo udzapulumutsa anthu ako.”

9Davide pamodzi ndi anthu ake 600 aja ananyamuka nafika ku mtsinje wa Besori. Kumeneko anasiyako anthu ena. 10Davide ndi anthu ake 400 anapitirira kuwalondola Aamaleki aja. Koma anthu ena 200 anatsala popeza anatopa moti sakanatha kuwoloka mtsinje wa Besori uja.

11Anthu amene anali ndi Davide anapeza Mwigupto mʼmunda wina ndipo anabwera naye kwa Davide. Iwo anamupatsa madzi kuti amwe ndi chakudya kuti adye. 12Anamupatsanso chidutswa cha keke yankhuyu ndi makeke awiri a mphesa zowumika kuti adye. Atadya anapezanso mphamvu popeza anakhala masiku atatu wosadya kapena kumwa kanthu kalikonse.

13Davide anafunsa kuti, “Kodi ndiwe yani, ndipo ukuchokera kuti?”

Iye anayankha kuti, “Ine ndine Mwigupto, kapolo wa Mwamaleki. Mbuye wanga anandisiya nditayamba kudwala masiku atatu apitawo. 14Ife tinathira nkhondo dera la kummwera kwa mayiko a Akereti, dera la Yuda, ndi dera la kummwera kwa mayiko a Kalebe. Mzinda wa Zikilagi tinawutentha ndi moto.”

15Davide anamupempha kuti, “Kodi unganditsogolere kumene kuli gulu lankhondoli?”

Iye anayankha kuti, “Mukandilonjeza molumbira kuti simudzandipha kapena kundipereka kwa mbuye wanga, ine ndikulondolerani kumene kuli gululo.”

16Mwigupto uja anaperekeza Davide. Tsono Aamaleki anali atamwazikana ponseponse. Iwo ankadya, kumwa ndi kuvina chifukwa cha zofunkha zambiri zimene anatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Ayuda. 17Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa. 18Choncho Davide analanditsa zinthu zonse zimene Aamaleki aja anatenga. Anapulumutsanso akazi ake awiri aja. 19Palibe chimene chinasowa anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, mnyamata mpaka mtsikana anapulumutsidwa. Davide anapulumutsa chilichonse chimene anafunkha Aamaleki aja. 20Anapulumutsanso nkhosa ndi ngʼombe zonse. Tsono anthu ankakusa ziwetozo namati, “Izi ndizo zofunkha za Davide.”

21Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera. 22Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.”

23Koma Davide anawayankha kuti, “Ayi, abale anga, musachite zimenezi ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watisunga ndi kupereka mʼmanja mwathu gulu la ankhondo limene linabwera kudzalimbana nafe. 24Ndani angakumvereni zimene mukunenazi? Gawo la munthu amene anapita kukamenya nkhondo likhale lofanana ndi la munthu amene anatsala pano kuyangʼanira katundu wathu. Pasakhale kusiyana kulikonse.” 25Choncho Davide anakhazikitsa ngati lamulo mʼchitidwe woterewu pakati pa Aisraeli kuyambira tsiku limenelo mpaka lero.

26Davide atafika ku Zikilagi, anatumiza zina mwa zofunkhazo kwa akuluakulu a Yuda, amene anali abwenzi ake. Anati, “Nayi mphatso yanu yochokera pa zofunkha za adani a Yehova.”

27Iye anatumiza mphatsozo kwa anthu a ku Beteli, Ramoti-Negavi, Yatiri, 28Aroeri, Sifimoti, Esitemowa 29Rakala, mizinda ya fuko la Ayerahimeeli, mizinda ya fuko la Akeni, 30a ku Horima, Borasani, Ataki, 31Hebroni pamodzi ndi onse a kumalo kumene Davide ndi anthu ake anakhala akuyendayendako.