1 Samueli 14 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 14:1-52

1Tsiku lina Yonatani mwana wa Sauli anawuza mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka Afilisti tsidya ilo.” Koma iye sanawuze abambo ake.

2Sauli ankakhala mʼmalire a Gibeya pa tsinde pa mtengo wamakangadza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600. 3Pakati pawo panalinso Ahiya amene ankavala efodi. Iye anali mwana wa Ahitubi, mʼbale wake wa Ikabodi mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo. Koma palibe amene anadziwa kuti Yonatani wachoka.

4Pa mpata pamene Yonatani ankafuna kudutsa kukafika ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti kunali thanthwe lotsetsereka mbali ina ndi lina lotsetsereka mbali inayo. Thanthwe limodzi linkatchedwa Bozezi ndipo linalo linkatchedwa Seni. 5Thanthwe limodzi linali chakumpoto kuyangʼanana ndi Mikimasi, ndipo thanthwe linalo linali chakummwera kuyangʼanana ndi Geba.

6Yonatani anawuza mnyamata wake womunyamulira zida uja kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka anthu osachita mdulidwewo. Mwina Yehova adzatigwirira ntchito. Palibe chomuletsa Yehova kutipulumutsa, ngakhale tikhale ambiri kapena ochepa.”

7Mnyamata uja anati, “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukhumba. Ine ndili nanu pamodzi. Chimene mtima wanu ukhumba ndi chomwenso ine ndikhumba.”

8Yonatani anati, “Tiye tsono tiwoloke kupita kumene kuli anthuwo ndi kukadzionetsa kwa iwo. 9Akatiwuza kuti, ‘Imani pomwepo mpaka tikupezeni,’ ife tikangoyima pomwepo osapita kumene kuli iwoko. 10Koma akadzati, ‘Bwerani kuno,’ ndiye ife tikapitedi, chifukwa ichi chidzakhala chizindikiro chakuti Yehova wapereka mʼmanja mwathu.”

11Choncho awiriwa anadzionetsa ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti. Tsono Afilistiwo anati, “Taonani! Aheberi akutuluka mʼmaenje mʼmene anabisala.” 12Anthu a ku kaboma kaja anafuwula kwa Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Bwerani kuno ndipo tikuphunzitsani phunziro.”

Ndipo Yonatani anati kwa mnyamata wake. “Nditsate pakuti Yehova wapereka Afilistiwa mʼmanja mwa Aisraeli.”

13Choncho Yonatani anakwera mokwawa, ndipo mnyamata wake uja ankamutsata. Tsono Yonatani anathira nkhondo Afilisti aja namawagwetsa, ndipo mnyamata wake uja ankawapha pambuyo pa iyeyo. 14Nthawi yoyambayo Yonatani ndi mnyamata wake uja anapha anthu makumi awiri ndipo anawaphera pa malo ochepa okwanira ngati theka la ekala.

Aisraeli Agonjetsa Afilisti

15Tsono gulu lonse la ankhondo, ndiye kuti iwo amene anali mʼmisasa ndi mʼminda ndiponso iwo amene anali ku kaboma ka ankhondo kaja, onse anagwidwa ndi mantha aakulu. Dzikonso linagwedezeka, choncho anthu anachita mantha koopsa.

16Alonda a Sauli a ku Gibeya dziko la Benjamini atangomwaza maso anangoona chigulu cha asilikali chikumwazikana uku ndi uku. 17Kenaka Sauli anawawuza anthu amene anali naye kuti, “Awerengeni asilikali kuti muona amene wachoka.” Atawawerenga anapeza kuti Yonatani ndi mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo palibe.

18Tsono Sauli anawuza Ahiya kuti, “Bwera nalo Bokosi la Mulungulo.” (Nthawi imeneyo nʼkuti efodiyo ili ndi Ahiya pamaso pa Aisraeli). 19Pamene Sauli amayankhula ndi wansembe, phokoso limanka likulirakulira mu msasa wa Afilisti, Kotero Sauli anati kwa wansembe, “Leka kuwombeza.”

20Ndipo Sauli ndi asilikali onse amene anali naye anasonkhana kupita kukamenya nkhondo, ndipo anangoona chisokonezo chachikulu kwambiri. Afilisti akuphana okhaokha. 21Aheberi ena amene kale anali ndi Afilisti mpaka kukakhala ku misasa yawo, iwonso anatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraeli amene ankatsata Sauli ndi Yonatani. 22Ngakhale Aisraeli amene ankabisala ku dziko lamapiri la Efereimu atamva kuti Afilisti akuthawa, nawonso anawathamangitsa Afilistiwo nawathira nkhondo. 23Nkhondo inapitirira mpaka kufika ku Beti-Aveni. Choncho Yehova anapulumutsa Aisraeli tsiku limenelo.

Yonatani Adya Uchi

24Koma asilikali a Israeli anavutika tsiku limenelo, chifukwa Sauli anawalumbirira Aisraeli kuti, “Wotembereredwa munthu aliyense amene adzadya kusanade, ine ndisanalipsire adani anga!” Kotero palibe wankhondo aliyense amene analawa chakudya.

25Gulu lonse la ankhondo linalowa mʼnkhalango mmene munali uchi. 26Atalowa mʼnkhalango, anaona uchi ukukha, koma palibe amene anadya, pakuti ankaopa lumbiro lija. 27Koma Yonatani sanamve kuti abambo ake anawalumbirira anthu aja choncho anatenga ndodo yake imene inali mʼdzanja lake ndipo anayipisa mu chisa cha njuchi. Choncho iye anadya uchiwo ndipo mʼmaso mwake munayera. 28Kenaka mmodzi mwa Asilikali anamuwuza kuti, “Abambo ako alumbirira anthu nati, ‘Wotembereredwa munthu aliyense amene adye chakudya lero.’ Nʼchifukwa chake anthu alefuka.”

29Yonatani anati, “Abambo anga achita chinthu choyipira dziko. Taonani mʼmaso mwanga mwayera chifukwa ndalawa uchiwu pangʼono. 30Zikanakhala zabwino kwambiri anthuwa akanadya lero zofunkha za adani awo. Zikanatero tikanapha Afilisti ochuluka.”

31Tsiku limenelo Aisraeli anapha Afilisti kuchokera ku Mikimasi mpaka ku Ayaloni. Koma Aisraeliwo analefuka kwambiri ndi njala. 32Choncho iwo anathamangira pa zofunkha ndipo anatenga nkhosa, ngʼombe ndi ana angʼombe. Iwo anazipha zonsezi nazidya pamodzi ndi magazi omwe. 33Koma anthu ena anawuza Sauli kuti, “Taona anthu akuchimwira Yehova pakudya nyama yomwe ili ndi magazi.”

Ndipo Sauli anati, “Mwaonetsa kusakhulupirika. Tsopano gubuduzirani mwala waukulu pano.” 34Kenaka Sauli anati, “Mwazikanani pakati pa anthu ndi kukawawuza kuti aliyense abwere ndi ngʼombe yake kapena nkhosa yake, ndipo adzayiphe pomwe pano ndi kuyidya. Musachimwire Yehova pakudya nyama imene ili ndi magazi.”

Kotero aliyense anabwera ndi ngʼombe yake usiku womwewo ndi kuyipha pomwepo. 35Ndipo Sauli anamangira Yehova guwa. Ili linali guwa loyamba limene Sauli anamangira Yehova.

36Sauli anati, “Tiyeni titsatire Afilisti usikuwu ndi kulanda zinthu zawo mpaka mmawa. Tisasiyepo wamoyo ndi mmodzi yemwe.”

Ankhondowo anayankha kuti, “Chitani chilichonse chimene chikukomerani.”

Koma wansembe anati, “Tipemphe uphungu kwa Mulungu poyamba.”

37Choncho Sauli anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndiwatsatire Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwathu?” Koma Mulungu sanamuyankhe tsiku limenelo.

38Choncho Sauli anati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu, ndipo tiyeni tione kuti kodi tchimo limeneli lachitika bwanji lero? 39Pali Yehova amene amapulumutsa Israeli, ngakhale tchimolo litapezeka ndi mwana wanga Yonatani, iye afe ndithu.” Koma palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthuwo amene anamuyankha.

40Tsono Sauli anawuza Aisraeli onse kuti, “Inu mukhale mbali imodzi. Ine ndi mwana wanga Yonatani tikhala mbali inayo.”

“Chitani chilichonse chimene chikukomerani.”

41Ndipo Sauli anapemphera kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, “Chifukwa chiyani simunandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati tchimoli lipezeka ndi ine kapena ndi Yonatani mwana wanga, Inu Mulungu wa Israeli, aoneke ndi Urimu. Koma ngati wochimwa ndi anthu anu, Aisraeli aoneke Tamimu.” Maere anagwera Sauli ndi Yonatani ndipo anthu anapezeka osalakwa. 42Sauli anati, “Chitani maere pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga.” Ndipo maere anagwera Yonatani.

43Kenaka Sauli anati kwa Yonatani, “Ndiwuze chimene wachita.”

Ndipo Yonatani anamuwuza kuti, “Ine ndinangolawa uchi pangʼono ndi ndodo yangayi. Ndiye ine ndili wokonzeka kufa.”

44Sauli anati, “Mulungu andilange ngakhale kufa kumene, ngati sufa iwe Yonatani.”

45Koma anthuwo anafunsa Saulo kuti, “Kodi Yonatani afe, iye amene wagwira ntchito iyi yayikulu yopulumutsa Aisraeli? Osatheka! Pali Yehova ngakhale tsitsi ndi limodzi lomwe lapamutu pake silidzathothoka, pakuti wachita zimenezi lero ndi thandizo la Mulungu.” Choncho anthuwo anamupulumutsa Yonatani, ndipo sanaphedwe.

46Pambuyo pake Sauli analeka kulondola Afilisti, kenaka anabwerera ku dziko lawo.

47Sauli ali mtsogoleri wa Israeli, anachita nkhondo ndi adani awa omuzungulira: Mowabu, Amoni, Edomu mafumu a ku Zoba ndi Afilisti. Kulikonse kumene ankapita ankawagonjetsa. 48Anachita nkhondo mwamphamvu ndi kugonjetsa Aamaleki. Choncho anapulumutsa Aisraeli mʼmanja mwa anthu amene ankawalanda zinthu zawo.

Banja la Sauli

49Ana aamuna a Sauli anali Yonatani, Isivi ndi Maliki-Suwa. Analinso ndi ana aakazi awiri, dzina la mwana wake wamkulu wamkazi linali Merabi ndipo la mwana wake wamngʼono wamkazi linali Mikala. 50Dzina la mkazi wake linali Ahinoamu. Iyeyu anali mwana wa Ahimaazi. Dzina la mkulu wa ankhondo a Sauli linali Abineri mwana wa Neri, mʼbale wa abambo a Sauli. 51Kisi abambo a Sauli ndi Neri abambo a Abineri anali ana a Abieli.

52Pa moyo wake wonse, Sauli ankakhalira kuchita nkhondo pakati pa Israeli ndi Afilisti. Ndipo Sauli ankati akaona munthu aliyense wamphamvu kapena wolimba mtima ankamulemba ntchito mu gulu lake lankhondo.

New International Version – UK

1 Samuel 14:1-52

1One day Jonathan son of Saul said to his young armour-bearer, ‘Come, let’s go over to the Philistine outpost on the other side.’ But he did not tell his father.

2Saul was staying on the outskirts of Gibeah under a pomegranate tree in Migron. With him were about six hundred men, 3among whom was Ahijah, who was wearing an ephod. He was a son of Ichabod’s brother Ahitub son of Phinehas, the son of Eli, the Lord’s priest in Shiloh. No-one was aware that Jonathan had left.

4On each side of the pass that Jonathan intended to cross to reach the Philistine outpost was a cliff; one was called Bozez and the other Seneh. 5One cliff stood to the north towards Michmash, the other to the south towards Geba.

6Jonathan said to his young armour-bearer, ‘Come, let’s go over to the outpost of those uncircumcised men. Perhaps the Lord will act on our behalf. Nothing can hinder the Lord from saving, whether by many or by few.’

7‘Do all that you have in mind,’ his armour-bearer said. ‘Go ahead; I am with you heart and soul.’

8Jonathan said, ‘Come on, then; we will cross over towards them and let them see us. 9If they say to us, “Wait there until we come to you,” we will stay where we are and not go up to them. 10But if they say, “Come up to us,” we will climb up, because that will be our sign that the Lord has given them into our hands.’

11So both of them showed themselves to the Philistine outpost. ‘Look!’ said the Philistines. ‘The Hebrews are crawling out of the holes they were hiding in.’ 12The men of the outpost shouted to Jonathan and his armour-bearer, ‘Come up to us and we’ll teach you a lesson.’

So Jonathan said to his armour-bearer, ‘Climb up after me; the Lord has given them into the hand of Israel.’

13Jonathan climbed up, using his hands and feet, with his armour-bearer right behind him. The Philistines fell before Jonathan, and his armour-bearer followed and killed behind him. 14In that first attack Jonathan and his armour-bearer killed some twenty men in an area of about half an acre.14:14 Or about 2,000 square metres

Israel routs the Philistines

15Then panic struck the whole army – those in the camp and field, and those in the outposts and raiding parties – and the ground shook. It was a panic sent by God.14:15 Or a terrible panic

16Saul’s lookouts at Gibeah in Benjamin saw the army melting away in all directions. 17Then Saul said to the men who were with him, ‘Muster the forces and see who has left us.’ When they did, it was Jonathan and his armour-bearer who were not there.

18Saul said to Ahijah, ‘Bring the ark of God.’ (At that time it was with the Israelites.)14:18 Hebrew; Septuagint ‘Bring the ephod.’ (At that time he wore the ephod before the Israelites.) 19While Saul was talking to the priest, the tumult in the Philistine camp increased more and more. So Saul said to the priest, ‘Withdraw your hand.’

20Then Saul and all his men assembled and went to the battle. They found the Philistines in total confusion, striking each other with their swords. 21Those Hebrews who had previously been with the Philistines and had gone up with them to their camp went over to the Israelites who were with Saul and Jonathan. 22When all the Israelites who had hidden in the hill country of Ephraim heard that the Philistines were on the run, they joined the battle in hot pursuit. 23So on that day the Lord saved Israel, and the battle moved on beyond Beth Aven.

Jonathan eats honey

24Now the Israelites were in distress that day, because Saul had bound the people under an oath, saying, ‘Cursed be anyone who eats food before evening comes, before I have avenged myself on my enemies!’ So none of the troops tasted food.

25The entire army entered the woods, and there was honey on the ground. 26When they went into the woods, they saw the honey oozing out; yet no-one put his hand to his mouth, because they feared the oath. 27But Jonathan had not heard that his father had bound the people with the oath, so he reached out the end of the staff that was in his hand and dipped it into the honeycomb. He raised his hand to his mouth, and his eyes brightened.14:27 Or his strength was renewed; similarly in verse 29 28Then one of the soldiers told him, ‘Your father bound the army under a strict oath, saying, “Cursed be anyone who eats food today!” That is why the men are faint.’

29Jonathan said, ‘My father has made trouble for the country. See how my eyes brightened when I tasted a little of this honey. 30How much better it would have been if the men had eaten today some of the plunder they took from their enemies. Would not the slaughter of the Philistines have been even greater?’

31That day, after the Israelites had struck down the Philistines from Michmash to Aijalon, they were exhausted. 32They pounced on the plunder and, taking sheep, cattle and calves, they butchered them on the ground and ate them, together with the blood. 33Then someone said to Saul, ‘Look, the men are sinning against the Lord by eating meat that has blood in it.’

‘You have broken faith,’ he said. ‘Roll a large stone over here at once.’ 34Then he said, ‘Go out among the men and tell them, “Each of you bring me your cattle and sheep, and slaughter them here and eat them. Do not sin against the Lord by eating meat with blood still in it.” ’

So everyone brought his ox that night and slaughtered it there. 35Then Saul built an altar to the Lord; it was the first time he had done this.

36Saul said, ‘Let us go down and pursue the Philistines by night and plunder them till dawn, and let us not leave one of them alive.’

‘Do whatever seems best to you,’ they replied.

But the priest said, ‘Let us enquire of God here.’

37So Saul asked God, ‘Shall I go down and pursue the Philistines? Will you give them into Israel’s hand?’ But God did not answer him that day.

38Saul therefore said, ‘Come here, all you who are leaders of the army, and let us find out what sin has been committed today. 39As surely as the Lord who rescues Israel lives, even if the guilt lies with my son Jonathan, he must die.’ But not one of them said a word.

40Saul then said to all the Israelites, ‘You stand over there; I and Jonathan my son will stand over here.’

‘Do what seems best to you,’ they replied.

41Then Saul prayed to the Lord, the God of Israel, ‘Why have you not answered your servant today? If the fault is in me or my son Jonathan, respond with Urim, but if the men of Israel are at fault,14:41 Septuagint; Hebrew does not have ‘Why… at fault. respond with Thummim.’ Jonathan and Saul were taken by lot, and the men were cleared. 42Saul said, ‘Cast the lot between me and Jonathan my son.’ And Jonathan was taken.

43Then Saul said to Jonathan, ‘Tell me what you have done.’

So Jonathan told him, ‘I tasted a little honey with the end of my staff. And now I must die!’

44Saul said, ‘May God deal with me, be it ever so severely, if you do not die, Jonathan.’

45But the men said to Saul, ‘Should Jonathan die – he who has brought about this great deliverance in Israel? Never! As surely as the Lord lives, not a hair of his head shall fall to the ground, for he did this today with God’s help.’ So the men rescued Jonathan, and he was not put to death.

46Then Saul stopped pursuing the Philistines, and they withdrew to their own land.

47After Saul had assumed rule over Israel, he fought against their enemies on every side: Moab, the Ammonites, Edom, the kings14:47 Masoretic Text; Dead Sea Scrolls and Septuagint king of Zobah, and the Philistines. Wherever he turned, he inflicted punishment on them.14:47 Hebrew; Septuagint he was victorious 48He fought valiantly and defeated the Amalekites, delivering Israel from the hands of those who had plundered them.

Saul’s family

49Saul’s sons were Jonathan, Ishvi and Malki-Shua. The name of his elder daughter was Merab, and that of the younger was Michal. 50His wife’s name was Ahinoam daughter of Ahimaaz. The name of the commander of Saul’s army was Abner son of Ner, and Ner was Saul’s uncle. 51Saul’s father Kish and Abner’s father Ner were sons of Abiel.

52All the days of Saul there was bitter war with the Philistines, and whenever Saul saw a mighty or brave man, he took him into his service.