1 Mbiri 9 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 9:1-44

1Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli.

Anthu a ku Yerusalemu

Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. 2Tsono anthu oyamba kukhala mʼmadera awo anali Aisraeli wamba, ansembe, Alevi ndi otumikira ku Nyumba ya Yehova.

3Anthu a ku Yuda, Benjamini ndi Efereimu ndiponso Manase amene anakhala mu Yerusalemu anali awa:

4Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi mwana wa Yuda.

5A banja la Siloni:

Asaya mwana wake woyamba pamodzi ndi ana ake.

6A banja la Zera:

Yeueli.

Anthu ochokera ku Yuda analipo 690.

7A fuko la Benjamini:

Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuya;

8Ibineya mwana wa Yerohamu; Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri; ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli mwana wa Ibiniya.

9Anthu ochokera ku Benjamini monga analembedwera mwa mibado yawo, analipo 956. Anthu onsewa anali atsogoleri a mabanja awo.

10Ansembe:

Yedaya, Yehoyaribu; Yakini;

11Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi, wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu;

12Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya; ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yahizera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri.

13Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja awo analipo 1,760. Anali anthu amphamvu ndi odziwa kutumikira mʼnyumba ya Mulungu.

14Alevi:

Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa mʼbanja la Merari; 15Bakibakara, Heresi, Galali ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu; 16Obadiya mwana wa Semaya mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi ya Anetofati.

17Alonda a pa makomo:

Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani ndi abale awo. Mtsogoleri wawo anali Salumu. 18Amenewa amakhala pa chipata cha mfumu kummawa mpaka lero lino. Alonda a gulu la Alevi anali awa: 19Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova. 20Masiku oyamba Finehasi mwana wa Eliezara anali woyangʼanira alonda apakhomo ndipo Yehova anali naye. 21Zekariya mwana wa Meselemiya anali mlonda woyangʼanira pa chipata cha tenti ya msonkhano.

22Onse amene anasankhidwa kukhala alonda pa khonde analipo 212. Iwo analembedwa mwa mibado yawo ku midzi yawo. Davide ndi mneneri Samueli ndiwo anawayika mʼmalo awo antchito chifukwa cha kukhulupirika kwawo. 23Iwo ndi zidzukulu zawo anali oyangʼanira zipata za nyumba ya Yehova imene imatchedwa Tenti. 24Alonda apakhomowa anali mbali zonse zinayi: kummawa, kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. 25Abale awo a ku midzi yawo amabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito yawo kwa masiku asanu ndi awiri. 26Koma atsogoleri akuluakulu anayi a alonda, amene anali Alevi, anapatsidwa udindo woyangʼanira zipinda ndi chuma cha nyumba ya Mulungu. 27Iwo amakhala usiku wonse atayima mozungulira Nyumba ya Mulungu, chifukwa anayenera kuyilondera. Ndipo anali ndi kiyi wotsekulira mmawa uliwonse.

28Ena amayangʼanira zipangizo zimene amagwiritsa ntchito pa ntchito mʼNyumba ya Mulungu. Iwo amaziwerenga zikamalowetsedwa ndi potulutsidwa. 29Ena anapatsidwa udindo wosamalira zipangizo ndi zinthu zina zonse za ku malo opatulika, pamodzi ndi ufa, vinyo, mafuta, lubani ndi zonunkhira. 30Koma ansembe ena amasakaniza zonunkhirazo. 31Mlevi wotchedwa Matitiya mwana woyamba wa Salumu wa mʼbanja la Kora, anapatsidwa udindo woyangʼanira zophikidwa mʼziwaya. 32Abale ake ena a mʼbanja la Akohati amaphika buledi wa pa Sabata lililonse amene amayikidwa pa tebulo.

33Atsogoleri a mabanja a Alevi, amene anali ndi luso loyimba, amakhala mʼzipinda za Nyumba ya Mulungu ndipo samagwira ntchito zina chifukwa ankatumikira usana ndi usiku.

34Onsewa anali atsogoleri a mabanja a Alevi, akuluakulu monga analembedwera pa mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.

Mibado ya Sauli

35Yeiyeli abambo a Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni.

Dzina la akazi awo linali Maaka, 36ndipo mwana wawo woyamba kubadwa anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu, 37Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti. 38Mikiloti anabereka Simeamu. Iwonso ankakhala ndi abale awo ku Yerusalemu.

39Neri anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.

40Mwana wa Yonatani anali

Meri-Baala, amene anabereka Mika.

41Ana a Mika anali:

Pitoni, Meleki, Tahireya ndi Ahazi.

42Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimiri anabereka Moza. 43Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Refaya, Eleasa ndi Azeli.

44Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo mayina awo anali awa:

Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Awa anali ana a Azeli.

Священное Писание

1 Летопись 9:1-44

1Весь Исраил был внесён в родословия, записанные в «Книге царей Исраила».

Жители Иерусалима после Вавилонского пленения

(Неем. 11:3-19)

Народ Иудеи был уведён в плен в Вавилон за свою неверность. 2Первыми, кто вернулся к своим владениям в своих городах, были простые исраильтяне, священнослужители, левиты и служители при храме.

3Вот те из родов Иуды, Вениамина, Ефраима и Манассы, кто жил в Иерусалиме:

4Утай, сын Аммихуда, сына Омри, сына Имри, сына Бани, потомка Фареца, сына Иуды.

5Из шилонитян:

первенец Асая и его сыновья.

6Из потомков Зераха:

Иеуил.

От Иуды было шестьсот девяносто человек.

7Из потомков Вениамина:

Саллу, сын Мешуллама, внук Годавии, правнук Ассенуа; 8Ивнея, сын Иерохама; Ела, сын Уззия, внук Михри; и Мешуллам, сын Шефатии, внук Рагуила, правнук Ивнии.

9От Вениамина, по их родословиям, было девятьсот пятьдесят шесть человек. Все эти люди были главами своих семейств.

10Из священнослужителей:

Иедая, Иехоярив, Иахин 11и Азария, сын Хилкии, сына Мешуллама, сына Цадока, сына Мерайота, сына Ахитува, главы дома Всевышнего; 12Адая, сын Иерохама, сына Пашхура, сына Малхии; Маасай, сын Адиила, сына Иахзера, сына Мешуллама, сына Мешиллемита, сына Иммера.

13Священнослужителей, которые были главами своих семейств, было тысяча семьсот шестьдесят человек. Они были искусны в деле служения в доме Всевышнего.

14Из левитов:

Шемая, сын Хашува, сына Азрикама, сына Хашавии, потомка Мерари; 15Бакбаккар, Хереш, Галал и Маттания, сын Михи, сына Зихри, сына Асафа; 16Авдий, сын Шемаи, сына Галала, сына Иедутуна, и Берехия, сын Асы, сына Элканы, который жил в селениях нетофитян.

17Привратниками были:

Шаллум, Аккув, Талмон, Ахиман и их родичи. Шаллум был их главой. 18До сих пор его род стоит на страже у Царских ворот, что с восточной стороны. Это привратники, которые были из левитов. 19Шаллуму, сыну Коре, внуку Авиасафа, правнуку Кораха, и привратникам из его родства (корахитам), которые несли службу вместе с ним, было доверено охранять пороги Шатра9:19 То есть храма; также в ст. 21 и 23., как их отцы охраняли вход в святилище Вечного. 20В прежние времена Пинхас, сын Элеазара, был начальником над привратниками, и Вечный был с ним. 21Закария, сын Мешелемии, был привратником у входа в Шатёр Встречи.

22Всего в привратники было избрано двести двенадцать человек. Они были внесены в родословия по своим поселениям. На ответственные места привратников поставили Давуд и провидец Шемуил. 23Им самим и их потомкам было доверено охранять ворота дома Вечного (именуемого Шатром). 24Привратники стояли с четырёх сторон – на востоке, на западе, на севере и на юге. 25Их сородичи в поселениях должны были время от времени приходить, чтобы делить с ними обязанности в течение семи дней. 26Но четырём главным привратникам, которые были левитами, были доверены комнаты и сокровища дома Всевышнего. 27Они проводили ночь возле дома Всевышнего, потому что должны были охранять его и каждое утро отпирать двери.

28Некоторым из них были доверены вещи, которыми пользовались при храмовой службе. Левиты пересчитывали их, когда принимали их и когда выдавали. 29Другие были назначены заботиться об утвари и всех прочих вещах святилища, а также о лучшей муке и вине, масле, ароматах и благовониях. 30А некоторые из священнослужителей смешивали благовония. 31Левиту по имени Маттафия, первенцу корахита Шаллума, было доверено печь хлеб для приношений, 32а некоторым из их каафитских сородичей были вверены заботы о священном хлебе на каждую субботу.

33Музыканты, главы левитских семейств, жили в комнатах храма и были свободны от других обязанностей, потому что несли свою службу днём и ночью.

34Все они были главами левитских семейств, вождями по своим родословиям, и жили в Иерусалиме.

Родословие Шаула

(1 Лет. 8:29-38)

35Иеил, отец Гаваона, жил в Гаваоне. Его жену звали Мааха; 36а первенцем его был Авдон, после которого родились Цур, Киш, Баал, Нер, Надав, 37Гедор, Ахио, Закария и Миклот. 38Миклот был отцом Шимеама. Они тоже жили в Иерусалиме рядом со своими сородичами.

39Нер был отцом Киша; Киш – отцом Шаула; Шаул – отцом Ионафана, Малик-Шуа, Авинадава и Иш-Бошета.

40Сын Ионафана:

Мефи-Бошет, который был отцом Михи.

41Сыновья Михи:

Пифон, Малик, Тареа и Ахаз.

42Ахаз был отцом Иадды; Иадда – отцом Алемета, Азмавета и Зимри, а Зимри – отцом Моцы. 43Моца был отцом Бинеа, сыном которого был Рефая, сыном которого был Элеаса, сыном которого был Ацель.

44У Ацеля было шесть сыновей. Вот их имена:

Азрикам, Бохру, Исмаил, Шеария, Авдий и Ханан. Это сыновья Ацеля.