1 Mbiri 28 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 28:1-21

Ndondomeko ya Kamangidwe ka Nyumba ya Mulungu

1Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima.

2Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.” 3Koma Mulungu anati kwa ine, “Usandimangire nyumba chifukwa ndiwe munthu wankhondo ndipo wakhala ukukhetsa magazi.”

4“Komabe Yehova Mulungu wa Israeli anasankha ine pakati pa onse a banja langa kukhala mfumu ya Israeli kwamuyaya. Iye anasankha Yuda kukhala mtsogoleri, ndipo pa banja la Yuda anasankha banja langa. Pakati pa ana aamuna a abambo anga, kunamukomera Iye kundikhazika mfumu ya Aisraeli onse. 5Pa ana anga ambiri onse amene Yehova wandipatsa, Iye wasankha mwana wanga Solomoni kuti akhale pa mpando waufumu wa ufumu wa Yehova kuti alamulire Israeli.” 6Yehova anati kwa ine, “Solomoni mwana wako ndiye amene adzamanga nyumba yanga ndi mabwalo anga, pakuti Ine ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. 7Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya ngati iye saleka kutsatira malamulo ndi malangizo anga, monga momwe zikuchitikira leromu.”

8“Tsono lero ine ndikulamula inu pamaso pa Aisraeli onse ndi pa msonkhano wa Yehova, ndipo Mulungu wathu akumva: Mutsatire mosamala malamulo a Yehova Mulungu wathu, kuti dziko labwinoli likhale lanu ndi kuti mudzalipereke kwa zidzukulu zanu kukhala cholowa chawo kwamuyaya.”

9“Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya. 10Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.”

11Kotero Davide anapatsa Solomoni mwana wake mapulani a khonde la Nyumba ya Mulungu, nyumba zake, mosungiramo katundu, zipinda zake zamʼmwamba, zipinda zamʼkati ndi malo a nsembe zopepesera machimo. 12Iye anapatsa Solomoni mapulani a zonse zimene ankaziganizira za bwalo la Nyumba ya Yehova ndi zipinda zonse zozungulira, zipinda zosungiramo chuma cha Nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Yehova. 13Davide anamulangiza za magulu a ansembe ndi Alevi ndi ntchito yonse yotumikira mʼNyumba ya Yehova, komanso za zinthu zonse zogwirira ntchito potumikira. 14Iye anakonzeratu za kulemera kwa golide wopangira zida zonse zagolide zogwirira ntchito zosiyanasiyana, ndiponso kulemera kwa siliva wopangira zida zonse zasiliva zogwirira ntchito zosiyanasiyana: 15kulemera kwa golide wopangira choyikapo nyale chagolide ndi nyale zake; ndiponso kulemera kwa siliva wa choyikapo nyale chilichonse ndi nyale zake, molingana ndi kagwiritsidwe ka choyikapo nyale chilichonse; 16kulemera kwa golide wa tebulo iliyonse yoyikapo buledi wopatulika; kulemera kwa siliva wopangira matebulo asiliva; 17muyeso wa golide woyengeka bwino wopangira mafoloko, mbale ndi zotungira; muyeso wa golide wa beseni lililonse la siliva; 18ndiponso muyeso wa golide wabwino wopangira guwa la zofukiza. Davide anamupatsanso ndondomeko ya mapangidwe a galeta, akerubi agolide atatambasula mapiko awo kuphimba Bokosi la Chipangano la Yehova.

19Davide anati, “Zonsezi ndalemba kuchokera kwa Yehova, ndipo Iye wachita kuti ndimvetsetse zonse za mapulaniwa.”

20Davide anatinso kwa mwana wake Solomoni, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndipo uchite ntchitoyi. Usachite mantha kapena kutaya mtima pakuti Yehova Mulungu wanga ali nawe. Iye sadzakukhumudwitsa kapena kukusiya mpaka ntchito yonse ya Nyumba ya Mulungu itatha. 21Magulu a ansembe ndi Alevi ndi okonzeka kugwira ntchito ya Nyumba ya Mulungu, ndipo munthu waluso aliyense wodzipereka adzakuthandiza pa ntchito yonse. Akuluakulu ndi anthu onse adzamvera chilichonse chomwe udzalamula.”

Bibelen på hverdagsdansk

1. Krønikebog 28:1-21

David forbereder Salomon på tempelbyggeriet

1David sammenkaldte alle landets ledere til et møde i Jerusalem: Stammelederne, de 12 divisionschefer og mange andre officerer, alle der havde opsyn med kongens og hans sønners ejendom og besætning, hofmændene og en række heltemodige krigere. 2Da de var samlet, rejste kongen sig og sagde:

„Mine ledere og mit folk! Jeg havde på hjerte at bygge et tempel, hvor Herrens Ark kunne stå, og hvor Herren kunne bo. Jeg har tilvejebragt alt, hvad der er brug for til byggeriet, 3men Gud har sagt ligeud: ‚Fordi du har udgydt så meget blod i dine krige, bliver det ikke dig, der kommer til at bygge mit tempel.’

4Ikke desto mindre har Herren, Israels Gud, udvalgt mig til at begynde et dynasti, der skal regere over Israel til evig tid. Først udvalgte han Judas stamme til at være den, kongerne skulle komme fra. Dernæst udvalgte han af Judas stamme min familie, og endelig behagede det ham at udvælge mig blandt min fars sønner til at være konge over Israel. 5Og blandt de mange børn, Herren har givet mig, har han udvalgt Salomon til at efterfølge mig som konge over sit folk, Israel. 6Herren sagde nemlig til mig: ‚Din søn Salomon skal bygge mit tempel, for jeg har udvalgt ham som min søn, og jeg vil være hans far. 7Hvis han fortsætter med at følge mine befalinger og forskrifter, som han gør i dag, vil jeg grundfæste hans kongedømme for evigt.’

8Med Gud som vidne opfordrer jeg derfor jer alle, hele Israels folk, Herrens menighed, til at overholde alle Guds bud, så I kan beholde dette gode land og lade det gå i arv til jeres efterkommere til evig tid. 9Og du, min søn Salomon, hold fast ved din fars Gud! Tjen ham helhjertet og med et villigt sind, for Herren ser til hjertet, og han kender hver en tanke! Hvis du søger ham, vil han lade sig finde. Men hvis du vender dig fra ham, vil han forkaste dig for evigt. 10Du må forstå, at Herren har udvalgt dig til at bygge ham et hus, som skal være hans helligdom. Så vær blot frimodig og gå i gang med arbejdet.”

11Derpå overrakte David Salomon planerne over templet med forhallen og de øvrige bygninger, forrådskamrene, tagrummene, det hellige rum og det allerhelligste rum med forsoningsstedet, hvor Gud tilgiver folkets synder. 12Han gav ham også planerne for tempelforgården, de ydre kamre og rummene, hvor tempelredskaberne og alle gaverne til templet skulle opbevares. 13Kongen gav endvidere Salomon instrukser vedrørende præsternes og levitternes skiftehold, og forklarede ham brugen af samtlige redskaber, der hørte til tjenesten i Herrens Hus.

14David forklarede, hvor meget guld og sølv der skulle bruges til de forskellige tempelredskaber, 15hvor meget der skulle bruges til guld- og sølvlysestagerne og de tilhørende lamper af guld eller sølv, afhængig af deres funktion. 16Han forklarede, hvor meget guld der skulle bruges til bordet, hvor de hellige brød skulle lægges frem, og hvor meget sølv der skulle bruges til sølvbordene i templet. 17Derefter forklarede han, hvor meget guld der skulle bruges til kødgafler, stænkeskåle og kander, og hvor meget guld og sølv der skulle bruges til guld- og sølvbægrene. 18Endelig forklarede han, hvor meget rent guld der skulle bruges til røgelsesalteret og til keruberne, hvis vinger dækker over pagtens ark.

19„Hver eneste detalje i denne plan blev givet mig af Herren,” understregede David. 20„Gå derfor blot frimodigt i gang med arbejdet. Lad dig ikke overvælde af det store projekt, for Herren, min Gud, vil være med dig. Han vil ikke svigte dig. Han vil hjælpe dig til at fuldføre det hele, indtil alt arbejdet med Herrens Hus er færdigt. 21Alle præsterne og levitterne er parat til at udføre deres opgaver i templet. Du har mange folk til rådighed, som både er villige og kvalificerede til al slags arbejde. Alle lederne og hele folket vil gøre, hvad du befaler dem.”