1 Mbiri 20 – CCL & TNCV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 20:1-8

Davide Alanda Raba

1Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Yowabu anatsogolera gulu la ankhondo. Iye anawononga Aamoni, kenaka anapita ku mzinda wa Raba ndipo anawuzungulira, koma Davide anatsala ku Yerusalemu. Yowabu anathira nkhondo mzinda wa Raba ndipo anawuwononga. 2Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Ndipo Davide anavala chipewacho. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, 3ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka Davide pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.

Davide Achita Nkhondo ndi Afilisti

4Patapita nthawi, nkhondo inayambika pakati pa Aisraeli ndi Afilisti ku Gezeri. Nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Sipai, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai, ndipo Afilisti anagonja.

5Pa nkhondo inanso ndi Afilisti, Elihanani mwana wa Yairi anapha Lahimi mʼbale wake wa Goliati Mgiti, amene mkondo wake unali ngati ndodo yowombera nsalu.

6Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati, panali munthu wina wamtali kwambiri, wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. 7Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha.

8Anthu amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.

Thai New Contemporary Bible

1พงศาวดาร 20:1-8

การยึดเมืองรับบาห์

(2ซมอ.11:1; 12:29-31)

1ในฤดูใบไม้ผลิอันเป็นช่วงที่กษัตริย์ทั้งหลายมักออกไปรบ โยอาบนำทัพอิสราเอลไปทำลายล้างดินแดนของชาวอัมโมน แล้วเขาก็ไปล้อมเมืองรับบาห์ แต่ดาวิดยังคงประทับอยู่ที่กรุงเยรูซาเล็ม โยอาบโจมตีรับบาห์และทิ้งให้เป็นซากปรักหักพัง 2ดาวิดทรงถอดมงกุฎจากพระเศียรของกษัตริย์20:2 หรือของพระมิลโคม(คือ พระโมเลค)ของพวกเขามาสวมบนพระเศียรของพระองค์ มงกุฎนั้นทำด้วยทองคำหนักประมาณ 34 กิโลกรัม20:2 ภาษาฮีบรูว่า1 ตะลันต์ประดับเพชรนิลจินดา ดาวิดทรงริบของเชลยได้มากมายจากเมืองนั้น 3และทรงเกณฑ์ชาวเมืองนั้นให้มาทำงานโดยใช้เลื่อย จอบ เสียมและขวาน ดาวิดทรงทำเช่นนี้กับทุกเมืองของอัมโมน แล้วดาวิดกับกองทัพทั้งหมดก็กลับกรุงเยรูซาเล็ม

สงครามกับชาวฟีลิสเตีย

(2ซมอ.21:15-22)

4ต่อมามีการสู้รบกับชาวฟีลิสเตียอีกที่เกเซอร์ ครั้งนั้นสิบเบคัยชาวหุชาห์ได้สังหารสิปปัยวงศ์วานของพวกมนุษย์ยักษ์เรฟาอิม และชาวฟีลิสเตียก็ยอมแพ้

5ในการรบกับฟีลิสเตียอีกครั้งหนึ่ง เอลฮานันบุตรยาอีร์ได้สังหารลามีน้องชายของโกลิอัทชาวกัท ผู้ซึ่งถือหอกด้ามใหญ่เหมือนไม้กระพั่นทอผ้า

6ในการรบอีกครั้งที่เมืองกัท คนร่างยักษ์ผู้หนึ่งมีนิ้วมือนิ้วเท้าข้างละ 6 นิ้วรวมเป็น 24 นิ้ว ซึ่งเป็นวงศ์วานราฟาเช่นกัน 7ได้มาข่มขู่อิสราเอล แต่ถูกโยนาธานบุตรชิเมอาพี่ชายของดาวิดสังหาร

8แล้วดาวิดและทหารปลิดชีพคนเหล่านี้ซึ่งเป็นวงศ์วานของราฟาแห่งเมืองกัท