1 Mbiri 1 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 1:1-54

Mbiri ya Makolo Kuchokera pa Adamu Mpaka pa Abrahamu

Mpaka pa Ana a Nowa

1Adamu, Seti, Enosi 2Kenani, Mahalaleli, Yaredi, 3Enoki, Metusela, Lameki, Nowa.

4Ana a Nowa,

Semu, Hamu ndi Yafeti.

Fuko la Yafeti

5Ana aamuna a Yafeti anali:

Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.

6Ana aamuna a Gomeri anali:

Asikenazi, Rifati ndi Togarima

7Ana aamuna a Yavani anali:

Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.

Fuko la Hamu

8Ana aamuna a Hamu anali:

Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani

9Ana aamuna a Kusi anali:

Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka

Ana aamuna a Raama anali:

Seba ndi Dedani.

10Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu

kwambiri pa dziko lapansi.

11Igupto ndiye kholo la

Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, 12Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori.

13Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni,

ndipo anaberekanso Ahiti, 14Ayebusi, Aamori, Agirigasi 15Ahivi, Aariki, Asini 16Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.

Fuko la Semu

17Ana aamuna a Semu anali:

Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.

Ana aamuna a Aramu anali:

Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.

18Aripakisadi anabereka Sela

ndipo Selayo anabereka Eberi:

19Eberi anabereka ana aamuna awiri:

wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.

20Yokitani anabereka

Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, 21Hadoramu, Uzali, Dikila 22Obali, Abimaeli, Seba, 23Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.

24Semu, Aripakisadi, Sela

25Eberi, Pelegi, Reu

26Serugi, Nahori, Tera

27ndi Abramu (amene ndi Abrahamu).

Banja la Abrahamu

28Ana a Abrahamu ndi awa:

Isake ndi Ismaeli.

Zidzukulu za Hagara

29Zidzukulu zake zinali izi:

Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 30Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema, 31Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli.

Zidzukulu za Ketura

32Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa:

Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa.

Ana a Yokisani ndi awa:

Seba ndi Dedani

33Ana aamuna a Midiyani anali,

Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.

Onsewa anali zidzukulu za Ketura.

Zidzukulu za Sara

34Abrahamu anabereka Isake.

Ana a Isake anali awa:

Esau ndi Israeli.

Ana a Esau

35Ana aamuna a Esau anali awa:

Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora.

36Ana a Elifazi anali awa:

Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi:

Amene anabereka ndi Timna: Amaleki.

37Ana a Reueli anali awa:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza.

Anthu a ku Seiri ku Edomu

38Ana a Seiri anali awa:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.

39Ana aamuna a Lotani anali awa:

Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.

40Ana aamuna a Sobala anali awa:

Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

Ana aamuna a Zibeoni anali awa:

Ayiwa ndi Ana.

41Mwana wa Ana anali

Disoni.

Ana a Disoni anali awa:

Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani

42Ana aamuna a Ezeri anali awa:

Bilihani, Zaavani ndi Yaakani.

Ana aamuna a Disani anali awa:

Uzi ndi Arani.

Mafumu a ku Edomu

43Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:

Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.

44Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.

45Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake.

46Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.

47Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake.

48Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake.

49Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.

50Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. 51Hadadi anamwaliranso.

Mafumu a ku Edomu anali:

Timna, Aliva, Yeteti, 52Oholibama, Ela, Pinoni, 53Kenazi, Temani, Mibezari, 54Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu.