1 Mafumu 7 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 7:1-51

Solomoni Amanga Nyumba Yake Yaufumu

1Solomoni anamanga nyumba yake yaufumu kwa zaka 13. 2Iye anamanga nyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni yomwe mulitali mwake inali mamita 44, mulifupi mwake mamita 22, msinkhu wake mamita 13 ndi theka; ndipo inakhazikika pa mizere inayi ya mapanda a mkungudza yokhala ndi mitanda ya mkungudza yotanthalika pa mapandawo. 3Pamwamba pa mitandapo panali matabwa a mkungudza amene anaphimba zipinda zimene zinamangidwa pa nsanamira 45, pa mzere uliwonse nsanamira 15. 4Mazenera a nyumbayo anali mmwamba mʼmizere itatu, zenera kuyangʼanana ndi zenera linzake. 5Zitseko zonse ndi mazenera omwe, maferemu ake anali ofanana mbali zonse. Mulitali mwake ndi mulifupi mwake, ndipo zenera linkapenyana ndi zenera linzake pa mizere itatu.

6Iye anapanga Chipinda cha Nsanamira. Mulitali mwake munali mamita 22, mulifupi mwake munali mamita 13 ndi theka. Patsogolo pake panali khonde ndi nsanamira zokhala ndi denga.

7Anamanga chipinda cha mpando waufumu, Chipinda cha Chilungamo, modzaweruziramo milandu ndipo anayikutira ndi matabwa a mkungudza kuchokera pansi mpaka ku denga. 8Ndipo nyumba yake yodzakhalamo anayimanga kumbuyo kwa chipindacho. Nyumbayo anayimanga mofanana ndi Chipindacho. Solomoni anamanga nyumba inanso yofanana ndi chipindachi, kumangira mkazi wake mwana wa Farao.

9Nyumba zonsezi, kuyambira kunja mpaka ku bwalo lalikulu ndiponso kuchokera pa maziko mpaka pamwamba pa khoma, zinapangidwa ndi miyala yabwino kwambiri imene anayisema potengera miyeso yake yoyenera ndipo anayisalaza ndi macheka mʼkati ndi kunja komwe. 10Maziko ake anali a miyala yabwino kwambiri, kutalika kwa miyala ina kunali mamita atatu ndi theka, inanso mamita anayi. 11Pamwamba pake panali pa miyala yabwino kwambiri, yosemedwa potengera miyeso yake. Pamwamba pa miyalayo panali matabwa a mkungudza. 12Bwalo lalikulu lozungulira nyumbayi linali ndi khoma la mizere itatu ya miyala yosemedwa ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza. Bwalo la mʼkati la Nyumba ya Yehova ndiponso khonde lake anazimanga mofanana.

Zipangizo za mʼNyumba ya Mulungu

13Mfumu Solomoni anatuma anthu ku Turo ndipo anakabwera ndi Hiramu, 14mwana wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali ndipo abambo ake anali a ku Turo, mʼmisiri wa mkuwa. Hiramu anali munthu wa luso lalikulu ndiponso wodziwa kupanga zinthu za mkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomoni ndi kugwira ntchito zonse zimene anamupatsa.

15Iye anawumba nsanamira ziwiri za mkuwa, nsanamira iliyonse msinkhu wake unali mamita asanu ndi atatu ndipo thunthu lake akazunguliza chingwe, linali mamita asanu ndi theka. 16Anapanganso mitu iwiri ya mkuwa ndi kuyiika pamwamba pa nsanamira zija; mutu uliwonse unali wotalika kupitirirapo mamita awiri. 17Pa mitu ya pa nsanamirazo anakolekapo maunyolo awiri olukanalukana ndi oyangayanga. Mutu uliwonse unali ndi maunyolo oterewa asanu ndi awiri. 18Anapanga mizere iwiri ya zinthu zonga makangadza mozungulira pamwamba pa maunyolo kukongoletsa mitu ya nsanamirazo. Anachita chimodzimodzi ndi mutu uliwonse. 19Mitu imene inali pamwamba pa nsanamira mʼkhonde inali yooneka ngati maluwa okongola kwambiri. Kutalika kwake kunali pafupifupi mamita awiri. 20Pa mitu yonse iwiri ya pamwamba pa nsanamira, pamwamba pa chigawo chonga mʼphika pafupi ndi cholukidwa ngati ukonde, panali makangadza 200 okhala mozungulira mʼmizere. 21Anayimika nsanamirazo pa khonde la Nyumba ya Mulungu. Nsanamira ya kumpoto anayitcha Yakini ndipo ya kummwera anayitcha Bowazi. 22Mitu ya pamwamba pa nsanamirazo inali yooneka ngati maluwa okongola kwambiri. Motero anamaliza ntchito ya nsanamirazo.

23Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13. 24Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo tizikho kuzungulira thunthu lonse la mbiyayo, tizikho khumi pa theka la mita. Tizikhoto tinali mʼmizere iwiri ndipo anatipangira kumodzi ndi mbiyayo.

25Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati. 26Mbiyayo inali yonenepa ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 40,000.

27Iye anapanganso maphaka khumi a mkuwa. Phaka lililonse mulitali mwake linali pafupifupi mamita awiri, mulifupi mwake linali pafupifupi mamita awiri, ndipo msinkhu wake unali kupitirirapo mita imodzi. 28Maphakawo anapangidwa motere: Anali ndi matabwa a mʼmbali amene ankalowa mʼmaferemu. 29Pakati pa matabwa a mʼmbali ndi maferemu panali zithunzi za mikango, ngʼombe zazimuna ndi akerubi. Pa maferemuwo, pamwamba ndi pansi pake pa mikangoyo ndi ngʼombe zazimunazo anajambulapo nkhata za maluwa. 30Phaka lililonse linali ndi mikombero ya mkuwa inayi ndi mitandanso ya mkuwa, ndipo phaka lililonse linali ndi zogwiriziza mbale zosambira pa ngodya zake zinayi, zopangidwa limodzi ndi nkhata za maluwa mbali zake zonse. 31Mʼkati mwa phakalo munali malo otsekuka amene anali ndi feremu yozungulira ndipo anali ozama theka la mita. Malo otsekukawa anali wozungulira, ndipo pamodzi ndi tsinde lake anali otalika masentimita 44. Kuzungulira pa malo otsekukawa panajambulidwa zokometsera. Matabwa oyimikira phakali anali ofanana mbali zonse, osati ozungulira. 32Pansi pa matabwawo panali mikombero inayi, ndipo mitanda ya mikomberoyo inalumikizidwa ku phakalo. Msinkhu wa mkombero uliwonse unali masentimita 66. 33Mikomberoyo inapangidwa ngati mikombero ya galeta; mitanda yake, marimu ake, sipokosi zake ndiponso mahabu ake, zonsezi zinali za chitsulo.

34Phaka lililonse linali ndi zogwirira zinayi; chogwirira chimodzi pa ngodya iliyonse, zolumikizidwa ku phakalo. 35Pamwamba pa phakalo panali mkombero wozungulira ndipo msinkhu wake unali masentimita 22. Pamwamba pa phakalo panali zogwiriziza ndi matabwa ake, zolumikizidwa ku phakalo. 36Paliponse pamene panali malo woti nʼkujambulapo, pa zogwiriziza ndi pa matabwa, anagobapo zithunzi za akerubi, mikango ndi mitengo ya mgwalangwa. Anajambulanso nkhata za maluwa mozungulira. 37Umu ndi mmene anapangira maphaka khumiwo. Onse anawapanga malo ofanana ndipo anali a miyeso yofanana ndiponso wooneka mofanana.

38Kenaka anapanga mabeseni akuluakulu khumi a mkuwa; beseni lililonse munkalowa madzi a malita 800, ndipo poyeza modutsa, pakamwa pake panali pafupifupi mamita awiri. Maphaka khumi aja, lililonse linali ndi beseni lake. 39Maphaka asanu anawayika mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu, asanu enawo anawayika mbali ya kumpoto. Mbiyayo anayiyika mbali yakummwera, pa ngodya yakummwera cha kummawa kwa Nyumba ya Mulungu. 40Iye anapanganso miphika ndi mafosholo ndi mabeseni owazira magazi.

Kotero Hiramu anatsiriza ntchito yonse ya ku Nyumba ya Yehova imene ankagwirira Mfumu Solomoni:

41nsanamira ziwiri;

mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;

maukonde awiri okongoletsera mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;

42makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);

43maphaka khumi pamodzi ndi mabeseni khumi pa maphakawo;

44mbiya pamodzi ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri zazimuna zosanjikapo mbiyayo;

45miphika, mafosholo ndi mbale zowazira magazi.

Ziwiya zonsezi za ku Nyumba ya Yehova, zimene Hiramu anapangira Mfumu Solomoni, zinali zamkuwa wonyezimira. 46Mfumu inapangitsa zimenezi mʼchigwa cha Yorodani, ku malo amtapo amene anali pakati pa Sukoti ndi Zaretani. 47Solomoni sanayeze ziwiya zonsezi chifukwa zinali zambiri ndipo kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.

48Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova:

guwa lansembe lagolide;

tebulo lagolide pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;

49zoyikapo nyale zagolide weniweni (dzanja lamanja zisanu ndipo zisanu zina ku dzanja lamanzere, mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika);

maluwa agolide, nyale ndi mbaniro;

50mbale zagolide weniweni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira;

ndiponso zomangira zitseko zagolide za chipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndiponso za zitseko za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu.

51Pamene ntchito yonse imene Mfumu Solomoni inagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka: siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Yehova.

Священное Писание

3 Царств 7:1-51

Дворец Сулеймана

1Но на то, чтобы завершить строительство своего дворца, у Сулеймана ушло тринадцать лет. 2Он построил дворец, который назывался дворцом Ливанского леса, – пятьдесят метров в длину, двадцать пять метров в ширину и пятнадцать метров7:2 Букв.: «сто… пятьдесят… тридцать локтей». в высоту, с четырьмя рядами кедровых колонн, поддерживающих кедровые балки. 3Его крыша была обшита кедром по балкам, которые располагались на колоннах, – сорок пять балок, по пятнадцать в каждом ряду. 4Окна его были поставлены высоко, по три окна в ряду, друг напротив друга. 5В дверных проёмах и в окнах7:5 Или: «косяках». были четырёхугольные рамы, и три ряда окон находились напротив трёх рядов на противоположной стене.

6Он сделал колонный зал – двадцать пять метров в длину и пятнадцать метров7:6 Букв.: «пятьдесят… тридцать локтей». в ширину. Там был притвор, крыша которого также поддерживалась колоннами.

7Он построил тронный зал для суда, называемый Зал правосудия, и покрыл его кедром от пола до потолка. 8А его дом, где он должен был жить, был в другом дворе, позади зала, такой же по замыслу. Ещё Сулейман сделал дворец, подобный этому залу, для дочери фараона, на которой женился.

9Все эти сооружения – от внешней стороны до большого двора и от основания до карнизов – были сделаны из дорогих камней, обтёсанных по размеру и обрезанных пилами с внешней и с внутренней стороны. 10В основания были заложены большие дорогие камни четырёх-пяти метров7:10 Букв.: «восьми-десяти локтей».. 11Сверху были дорогие камни, обтёсанные по размеру, и кедровые балки. 12Большой двор был обнесён стеной из трёх рядов обтёсанного камня и ряда кедровых брусьев, как внутренний двор храма Вечного с его притвором.

Хурам – бронзовых дел мастер

13Царь Сулейман пригласил и принял Хурама из Тира, 14сына вдовы из рода Неффалима. Его отцом был тирянин, бронзовых дел мастер. Хурам был очень искусен и имел большой навык во всех видах работы с бронзой. Он пришёл к царю Сулейману и сделал всю работу, которая была ему поручена.

Две бронзовые колонны

(2 Лет. 3:15-17)

15Хурам отлил две бронзовые колонны. Одна из них была девять метров высотой, и шнур длиной в шесть метров7:15 Букв.: «восемнадцать… двенадцать локтей». обвивал её по окружности. Вторая колонна была такой же. 16Ещё он сделал две капители колонн из литой бронзы, чтобы поставить их на колоннах. Капители на каждой из колонн были по два с половиной метра7:16 Букв.: «пять локтей». высотой. 17Верхние части колонн украшала сетка из переплетённых цепей, по семь на каждой колонне. 18Он сделал два ряда гранатовых плодов, окружавших каждую сетку, чтобы украсить капители колонн. Обе капители он сделал одинаковыми. 19На капителях колонн притвора были вырезаны лилии в два метра7:19 Букв.: «четыре локтя». высотой. 20На капителях обеих колонн, над чашеобразной частью рядом с сеткой, были сделаны кругом рядами двести гранатовых плодов.

21Хурам установил колонны у притвора храма. Ту колонну, что с южной стороны, он назвал Иахин («Он утвердит»), а ту, что с северной, – Боаз («в Нём сила»). 22Капители колонн были сделаны в виде лилий. На этом была завершена работа над колоннами.

Бронзовый бассейн

(2 Лет. 4:2-5)

23Хурам вылил из бронзы большой круглый бассейн, названный «морем», который был пяти метров в диаметре, двух с половиной метров высотой и пятнадцати метров7:23 Букв.: «десять… пять… тридцать локтей». в окружности. 24Снизу его окружали два ряда подобия тыкв – по десять на каждые полметра7:24 Букв.: «на локоть».. Тыквы были отлиты с бассейном одним литьём.

25Бассейн стоял на двенадцати быках, три из которых смотрели на север, три на запад, три на юг и три на восток. Бассейн покоился на них, а их зады были обращены внутрь, к центру. 26Его стенки были восемь сантиметров толщиной, а его край был как край чаши, как цветок лилии. Бассейн вмещал в себя сорок четыре тысячи литров7:26 Букв.: «одна ладонь… две тысячи батов». воды.

Бронзовые подставки

27Ещё Хурам сделал десять передвижных подставок из бронзы. Каждая была два метра длиной, два шириной и полтора метра7:27 Букв.: «четыре… четыре… три локтя». высотой. 28Вот как были устроены подставки: у них были боковые панели, находящиеся внутри рамок. 29На панелях внутри рамок, как и на самих рамках, были изображены львы, быки и херувимы. Над львами и быками и под ними были кованые венки. 30У каждой подставки было по четыре бронзовых колеса с бронзовыми осями, и у каждой была умывальница, которая покоилась на четырёх опорах, отлитых с венками на каждой стороне. 31На верху каждой подставки была круглая рама для умывальницы, служившая ей опорой. Эта рама была высотой в полметра, а её отверстие было семидесяти пяти сантиметров7:31 Букв.: «один… полтора локтя». шириной. Снаружи на ней были резные украшения. Панели подставок были квадратные, а не круглые. 32Под панелями находилось четыре колеса, и их оси крепились к подставке. Диаметр каждого колеса был равен семидесяти пяти сантиметрам7:32 Букв.: «полтора локтя».. 33Колёса были сделаны как для колесниц: оси, ободья, спицы и ступицы – все были литые.

34У каждой подставки было четыре рукоятки, по одной на каждом углу, которые выдавались из подставки. 35На верху подставки был круглый обод высотой в четверть метра7:35 Букв.: «пол-локтя».. Опоры и панели крепились к верхушке подставки. 36На подставках и панелях, где только было место, Хурам вырезал херувимов, львов и пальмы, а вокруг – венки. 37Так он сделал десять подставок. Все они были отлиты одинаково и были одного размера и формы.

38Затем Хурам сделал десять бронзовых умывальниц, каждая из которых вмещала восемьсот восемьдесят литров воды и была два метра7:38 Букв.: «сорок батов… четыре локтя». в диаметре, по одной умывальнице на каждую из десяти подставок. 39Он поставил пять подставок на южной стороне храма и пять на северной, а «море» поставил на юго-восточном углу храма.

40Ещё Хурам сделал горшки, лопатки и кропильные чаши.

Список утвари храма

(2 Лет. 4:11–5:1)

На этом Хурам завершил всю работу, которую выполнял для царя Сулеймана в храме Вечного. Он сделал

41две колонны,

две чашеобразные капители для колонн,

две сетки, украшавшие чашеобразные капители,

42четыреста плодов гранатового дерева для двух сеток (два ряда гранатов для каждой сетки, украшавшей чашеобразные капители),

43десять подставок с умывальницами,

44«море» и двенадцать быков под ним,

45горшки, лопатки и кропильные чаши.

Вся утварь, которую Хурам сделал царю Сулейману для храма Вечного, была из полированной бронзы. 46Царь велел отлить её в глиняных формах в долине Иордана между Суккотом и Цартаном. 47Сулейман не взвешивал всех этих вещей, потому что их было слишком много. Вес бронзы остался неизвестным.

48Ещё Сулейман сделал всю утварь для храма Вечного:

золотой жертвенник,

золотой стол для священного хлеба,

49подсвечники из чистого золота (пять на правую и пять на левую сторону перед внутренним святилищем),

золотые цветы, светильники и щипцы,

50кубки, ножницы для фитилей, кропильные чаши, блюда и сосуды для возжигания благовоний – всё из чистого золота,

золотые петли для дверей внутренней комнаты, Святая Святых, а также для внешних дверей храма.

51Когда вся работа, которую царь Сулейман делал для храма Вечного, была завершена, он принёс те вещи, которые посвятил Вечному его отец Давуд, – серебро, золото и утварь – и положил их в сокровищницы храма Вечного.