1 Mafumu 2 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 2:1-46

Davide Alangiza Solomoni

1Davide ali pafupi kumwalira, analangiza mwana wake Solomoni kuti:

2“Ndatsala pangʼono kupita kumene munthu wina aliyense amayenera kupitako. Tsono khala wamphamvu, uvale zilimbe, 3ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite. 4Ndipo Yehova akwaniritse zimene anandilonjeza kuti, ‘Ngati zidzukulu zako zidzakhala mosamala, niziyenda mokhulupirika pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse, sudzasowa munthu wokhala pa mpando waufumu wa Israeli.’

5“Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake. 6Iwe uchite kwa iye molingana ndi nzeru zako, koma usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.

7“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.

8“Ndipo kumbukira kuti uli ndi Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wochokera ku Bahurimu, amene ananditemberera koopsa tsiku limene ndimapita ku Mahanaimu. Atabwera kudzakumana nane ku Yorodani, ine ndinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Sindidzakupha iwe ndi lupanga.’ 9Koma tsopano usamuyese ngati munthu wosalakwa. Iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziwa choti uchite naye. Ngakhale ndi wokalamba, aphedwe ndithu.”

10Tsono Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. 11Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33. 12Choncho Solomoni anakhala pa mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo ufumu wake unakhazikika kwambiri.

Kukhazikika kwa Ufumu wa Solomoni

13Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, anapita kwa Batiseba, amayi ake a Solomoni. Batiseba anamufunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere?”

Iye anayakha kuti, “Eya, ndi zamtendere.” 14Ndipo iye anawonjezera kunena kuti, “Ndili ndi mawu oti ndiyankhule nanu.”

Batiseba anayankha kuti, “Yankhula.”

15Tsono Adoniya anati, “Monga inu mukudziwa, ufumu unali wanga. Aisraeli onse ankayembekezera kuti ine ndidzakhala mfumu yawo. Koma zinthu zinasintha ndipo ufumu wapita kwa mʼbale wanga; pakuti wapatsa iye ufumuwu ndi Yehova. 16Tsono ndili ndi pempho limodzi kwa inu. Musandikanize ayi.”

Batiseba anati, “Nena.”

17Adoniya anapitiriza kunena kuti, “Chonde, inu mupemphe mfumu Solomoni kuti andipatse Abisagi wa ku Sunemu kuti akhale mkazi wanga pakuti mukapempha inu sadzakukanizani.”

18Batiseba anayankha kuti, “Chabwino. Ndidzakuyankhulira kwa mfumu.”

19Batiseba atapita kwa Mfumu Solomoni kukayankhula naye mʼmalo mwa Adoniya, mfumu inanyamuka kukumana naye, ndipo inaweramira amayi akewo, kenaka inakhala pa mpando wake waufumu. Iye anayitanitsa mpando wina kuti amayi ake akhalepo ndipo anakhala pansi ku dzanja lake lamanja.

20Amayi akewo anati, “Ndikufuna ndikupempheni kanthu kakangʼono. Chonde musandikanize.”

Mfumu inayankha kuti, “Pemphani amayi, ine sindikukanizani.”

21Ndipo amayiwo anati, “Mulole kuti Abisagi wa ku Sunemu akhale mkazi wa mʼbale wanu Adoniya.”

22Koma Mfumu Solomoni inayankha amayi ake aja kuti, “Chifukwa chiyani mukupemphera Adoniya Abisagi wa ku Sunemu? Mungathenso kumupemphera ufumu pakuti iyeyu ndi mkulu wanga ndipo mupemphereninso wansembe Abiatara ndi Yowabu mwana wa Zeruya!”

23Pamenepo Mfumu Solomoni inalumbira mʼdzina la Yehova kuti, “Mulungu andilange ine koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha pempho lakeli! 24Tsono pali Yehova wamoyo, amene anandikhazikitsa ine pa mpando waufumu wa abambo anga Davide ndi kundipatsa ufumu monga analonjezera, Adoniya aphedwa lero lomwe lino!” 25Choncho Mfumu Solomoni inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo anakantha Adoniyayo, nafa.

26Ndipo mfumu inati kwa Abiatara wansembe, “Pita ku Anatoti ku minda yako chifukwa ndiwe woyenera kufa, koma sindikupha tsopano, chifukwa unkanyamula Bokosi la Chipangano la Ambuye Yehova pamaso pa abambo anga Davide ndipo unazunzika limodzi ndi abambo angawo.” 27Kotero Solomoni anachotsa Abiatara pa udindo wokhala wansembe wa Yehova, kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula za nyumba ya Eli ku Silo.

28Yowabu atamva zimenezi anathawira ku tenti ya Yehova ndipo anakagwira msonga za guwa lansembe, popeza Yowabu ndiye anathandiza Adoniya kuwukira koma sanathandize Abisalomu. 29Mfumu Solomoni inawuzidwa kuti Yowabu wathawira ku tenti ya Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe. Tsono Solomoni analamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti, “Pita, kamukanthe!”

30Choncho Benaya analowa mʼtenti ya Yehova ndipo anati kwa Yowabu, “Mfumu ikuti ‘Tuluka!’ ”

Koma iye anayankha kuti, “Ayi, ine ndifera muno.”

Benaya anakafotokozera mfumu kuti, “Umu ndi mmene Yowabu wandiyankhira.”

31Pamenepo mfumu inalamula Benaya kuti, “Kachite monga iye wanenera. Ukamukanthe ndi kumuyika mʼmanda. Ukatero udzandichotsera ine pamodzi ndi nyumba ya abambo anga mlandu wa anthu osalakwa amene Yowabu anawapha. 32Yehova adzamubwezera zomwe anachita pokhetsa magazi, chifukwa iye anakantha ndi lupanga anthu awiri abwino ndi olungama kuposa iye, nawapha, abambo anga Davide osadziwa. Anthu awiriwo ndi Abineri mwana wa Neri, wolamulira gulu lankhondo la Israeli ndi Amasa mwana wa Yeteri, wolamulira gulu lankhondo la Yuda. 33Magazi amene Yowabu anakhetsa akhale pamutu pake ndi pa zidzukulu zake kwamuyaya. Koma pa Davide ndi zidzukulu zake, nyumba yake ndi mpando wake waufumu pakhale mtendere wochokera kwa Yehova kwamuyaya.”

34Choncho Benaya mwana wa Yehoyada anapita kukakantha Yowabu nʼkumupha ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yakeyake ya ku chipululu. 35Mfumu inayika Benaya mwana wa Yehoyada kuti akhale woyangʼanira gulu lankhondo mʼmalo mwa Yowabu ndipo inayika Zadoki kuti akhale wansembe mʼmalo mwa Abiatara.

36Kenaka mfumu inatuma anthu kukayitana Simei ndipo inamuwuza kuti, “Udzimangire nyumba mu Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko, koma usatuluke mu mzinda kupita kwina kulikonse. 37Tsiku lomwe udzatulukemo ndi kuwoloka Chigwa cha Kidroni, udziwiretu kuti udzafa ndipo magazi ako adzakhala pamutu pako.”

38Simei anayankha mfumu kuti, “Zimene mwanenazi nʼzabwino. Kapolo wanu adzachita monga mbuye wanga mfumu mwanenera.” Choncho Simei anakhala mu Yerusalemu nthawi yayitali.

39Koma patatha zaka zitatu, akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati, ndipo Simei anawuzidwa kuti, “Akapolo anu ali ku Gati.” 40Atamva zimenezi, anakwera bulu wake ndipo anapita kwa Akisi ku Gati kukafunafuna akapolo ake. Choncho Simei anapita ndi kukatenga akapolo ake ku Gati ndipo anabwera nawo.

41Solomoni atawuzidwa kuti Simei anatuluka mu Yerusalemu ndi kupita ku Gati ndipo kuti wabwerako, 42mfumu inamuyitanitsa Simei ndipo inamufunsa kuti, “Kodi sindinakulumbiritse mʼdzina la Yehova ndi kukuchenjeza kuti, ‘Tsiku limene udzatuluka kupita kwina kulikonse, udziwe kuti udzafa’? Nthawi imeneyo iwe unandiwuza kuti, ‘Zimene mwanena nʼzabwino. Ine ndidzamvera.’ 43Chifukwa chiyani tsono sunasunge lumbiro lako kwa Yehova? Bwanji nanga sunamvere lamulo limene ndinakuwuza?”

44Mfumuyo inawuzanso Simei kuti, “Ukudziwa mu mtima mwakomo zoyipa zonse zimene unachitira abambo anga Davide. Tsopano Yehova akubwezera zoyipa zakozo. 45Koma Mfumu Solomoni idzadalitsidwa ndipo mpando waufumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova kwamuyaya.”

46Pamenepo mfumu inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo iye anapita kukakantha Simei ndi kumupha.

Tsono ufumu unakhazikika mʼdzanja la Solomoni.

New Serbian Translation

1. Књига о царевима 2:1-46

Давид саветује Соломона

1Кад се приближио час Давидове смрти, заповедио је своме сину Соломону:

2„Ја одлазим на пут којим сва земља иде. Стога буди јак и држи се мушки. 3Пази на сва упутства Господа, Бога свога, следећи његове путеве и држећи његове прописе, његове заповеди, његове правила и његова сведочанства, како је записано у Закону Мојсијевом, да би био успешан у свему што предузимаш, куда год се окренеш. 4Тада ће Господ испунити обећање које ми је дао, рекавши: ’Ако твоји синови буду пазили како живе, и буду ходили преда мном у верности свим својим срцем и свом својом душом, никада ти неће понестати наследника на Израиљевом престолу.’

5Такође знаш шта ми је учинио Јоав, син Серујин, и шта је учинио с двојицом израиљских војних заповедника, Авениром, сином Неровим, и Амасом, сином Јетеровим. Он их је убио проливши крв у миру као у рату, окаљавши опасач око својих бокова и сандале на својим ногама крвљу проливеном у рату. 6Поступи како ти мудрост налаже, али не дозволи да му седа глава с миром сиђе у Свет мртвих2,6 У изворном тексту Шеол, или подземље, где пребивају душе умрлих..

7А синовима Варзелаја Галађана искажи благонаклоност, јер су били уз мене кад сам бежао пред твојим братом Авесаломом. Зато нека једу за твојим столом.

8Код тебе је и Семај, син Гирин, Венијаминовац из Ваурима. Он ме је љуто проклињао оног дана кад сам ишао за Маханајим. Ипак, дошао је да ме дочека на Јордану. Тада сам му се заклео Господом: ’Нећу те погубити мачем.’ 9Зато му не опраштај кривицу, јер ти си мудар човек, и знаш како да поступиш с њим, да пошаљеш његову седу главу с крвљу у Свет мртвих.“

10Затим се Давид упокојио са својим прецима; сахранили су га у Давидовом граду. 11Давид је владао над Израиљем четрдесет година. У Хеврону је владао седам година, а у Јерусалиму је владао тридесет три године.

Соломон учвршћује своју власт

12Соломон је сео на Давидов престо, и његово царство се веома учврстило.

13А Адонија, син Агитин, дође Витсавеји, мајци Соломоновој. Она упита: „Долазиш ли с миром?“

Он рече: „С миром.“

14Он рече: „Имам нешто да ти кажем.“ Она рече: „Кажи.“

15Он рече: „Ти знаш да је царство било моје, и да је сав Израиљ очекивао да будем цар. Али испало је другачије, па је припало моме брату, јер га је добио од Господа. 16А сад имам нешто што бих те замолио. Немој ме одбити.“

Она рече: „Говори.“

17„Питај, молим те, цара Соломона – он те неће одбити – да ми да Ависагу Сунамку за жену.“

18„У реду – рече Витсавеја – разговараћу с царем о теби.“

19Витсавеја дође цару Соломону да с њим разговара о Адонији. Цар је устао да је поздрави; поклонио јој се, па је сео на престо. Тада су поставили столицу за цареву мајку, те је она села њему с десне стране.

20Она рече: „Тражила бих од тебе једну малу ствар, немој ме одбити.“

Цар јој рече: „Тражи, мајко, јер те нећу одбити.“

21Она рече: „Нека се да Ависага Сунамка твоме брату Адонији за жену.“

22Цар Соломон одговори својој мајци: „Зашто тражиш Ависагу Сунамку за Адонију? Што не тражиш и царство за њега, пошто је он мој старији брат?! А још су и свештеник Авијатар и Јоав, син Серујин, уз њега.“

23Тада се цар Соломон закле: „Нека ми Господ тако учини, и још више, ако Адонија не плати главом за ове речи! 24Стога, живога ми Господа, који ме је поставио на престо Давида, оца мога, и подигао ми дом, како је обећао, данас ће Адонија бити погубљен!“ 25Тада цар Соломон посла Венају, сина Јодајевог, који удари Адонију, те он умре.

26Затим је цар рекао свештенику Авијатару: „Иди у Анатот на свој посед. Заслужио си да умреш, али те нећу погубити данас, јер си носио Ковчег Господа Бога пред мојим оцем, и јер си поднео све невоље које је мој отац поднео.“ 27Тако је Соломон искључио Авијатара из свештенства Господњег, да се испуни реч Господња изречена у Силому за дом Илијев.

28Кад је ова вест дошла до Јоава, побегао је у Шатор Господњи, и ухватио се за рогове жртвеника, пошто се Јоав приклонио Адонији, иако се није приклонио Авесалому. 29Тада су јавили цару Соломону: „Јоав је побегао у Шатор Господњи и ено га код жртвеника.“ Цар посла Венају, сина Јодајевог и рече му: „Иди и убиј га.“

30Венаја уђе у Шатор Господњи и рече Јоаву: „Цар заповеда да изађеш.“

Али он одговори: „Нећу, нека умрем овде!“

Венаја се врати цару с одговором: „Јоав је рекао тако и тако; то је одговор који ми је дао.“

31Цар му рече: „Уради како је рекао. Убиј га, па га сахрани. Тако ће се с мене и с дома мога оца уклонити кривица за невину крв коју је Јоав пролио. 32Тако ће Господ вратити његово крваво дело на његову главу, јер је убио два праведна човека и то боља од њега; он је, без знања мога оца Давида, убио мачем Авенира, сина Неровог, војводу Израиљевог, и Амасу, сина Јетеровог, војводу Јудиног. 33Нека кривица за њихову крв падне на главу Јоаву и његовом семену заувек. А Давиду и његовом семену, његовом дому и његовом престолу, нека довека буде мир од Господа.“

34Венаја, син Јодајев, оде и удари Јоава, те он умре. Сахранили су га код његове куће у пустињи. 35Цар Соломон је уместо њега поставио Јодајевог сина Венају над војском, а свештеника Садока је цар поставио уместо Авијатара.

36Потом цар посла по Семаја и рече му: „Сагради себи кућу у Јерусалиму и остани тамо; никуд не излази оданде. 37Оног дана кад изађеш и пређеш преко потока Кидрона, знај да ћеш свакако умрети, па ће твоја крв пасти на твоју главу.“

38Семај одговори цару: „Повољна је реч коју је рекао мој господар цар. Твој слуга ће урадити тако.“ Семај је дуго времена остао у Јерусалиму.

39На крају треће године, два Семајева роба одбегну к Ахису, сину Махином, цару гатском. Семају су јавили: „Твоји робови су у Гату.“ 40Семај устане, оседла магаре и оде у Гат, к цару Ахису, да тражи своје робове. Семај оде и доведе своје робове из Гата.

41Но, Соломону су јавили да је Семај отишао из Јерусалима у Гат и да се вратио. 42Цар посла по Семаја и рече му: „Нисам ли те заклео Господом и упозорио те: ’Оног дана кад изађеш било где, знај да ћеш свакако умрети?’ Зар ми ниси одговорио: ’Повољна је реч; послушаћу’? 43Зашто ниси одржао заклетву Господу и заповест коју сам ти дао?“

44Цар је још рекао Семају: „Ти знаш у свом срцу све зло које си учинио моме оцу Давиду. Нека Господ врати твоје зло на твоју главу. 45Нека Соломон буде благословен, а престо Давидов нека заувек буде утврђен пред Господом.“

46Тада је цар дао наредбу Венаји, сину Јодајевом, па је отишао и ударио Семаја, те је овај умро.

Тако се царство утврдило у Соломоновим рукама.