1 Akorinto 4 – CCL & JCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 4:1-21

Atumiki a Khristu

1Choncho tsono anthu atione ife monga atumiki a Khristu, ndiponso ngati osunga zinsinsi za Mulungu. 2Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika. 3Ine ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu kapena khothi lina lililonse. Ndithu, inenso sindidziweruza ndekha. 4Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, koma sikuti ndine wolungama. Wondiweruza ine ndi Ambuye. 5Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.

6Tsono abale, ndapereka chitsanzo cha ine mwini ndi Apolo kuti mupindule. Phunzirani kwa ife tanthauzo la mawu akuti, “Musamapitirire zimene Malemba akunena,” kuti musamanyade pamene wina aposa mnzake. 7Pakuti ndani amakusiyanitsani ndi wina aliyense? Nʼchiyani muli nacho chimene simunalandire? Ndipo ngati munalandira, bwanji mumadzitukumula ngati kuti simunalandire?

8Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu. 9Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu. 10Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu! Ife ndife ofowoka koma inu ndinu amphamvu! Inu ndinu olemekezeka koma ife ndife opeputsidwa! 11Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. 12Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. 13Pamene atilalatira timayankha mwachifundo. Mpaka pano takhala ngati zinyalala za dziko, monga zakudzala za dziko lapansi.

Pempho ndi Chenjezo

14Sindikulemba izi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kukuchenjezani monga ana anga okondedwa. 15Ngakhale muli ndi anthu 10,000 okutsogolerani mwa Khristu, mulibe abambo ambiri, popeza mwa Khristu Yesu, ine ndakhala abambo anu kudzera mu Uthenga Wabwino. 16Chifukwa chake ndikukupemphani kuti munditsanze ine. 17Chifukwa cha ichi ndikutumiza kwa inu Timoteyo, mwana wanga amene ndimamukonda, amene ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Adzakukumbutsani inuyo za moyo wanga mwa Khristu Yesu, umene ukugwirizana ndi zimene ndimaphunzitsa paliponse mu mpingo uliwonse.

18Ena mwa inu mukudzitukumula, ngati kuti sindingabwere kwanu. 19Koma ndibwera kwanuko posachedwapa, ngati Ambuye alola, ndipo ndi pamene ndidzadziwe osati zimene anthu odzitukumulawa akuyankhula, koma kuti mphamvu zawo nʼzotani. 20Pakuti ufumu wa Mulungu si mawu chabe koma mphamvu. 21Kodi musankha chiyani? Kodi ndidzabwere ndi chikwapu, kapena mu chikondi ndiponso mwa mzimu wofatsa?

Japanese Contemporary Bible

コリント人への手紙Ⅰ 4:1-21

4

1こういうわけでアポロや私を、神の深い御心を説明し、その祝福を配って回る、キリストの福音を預かる管理者と考えてください。 2家臣にとって一番大切なのは、主人の命令に従うことです。 3では私の場合はどうでしょう。良い管理者だったでしょうか。この点に関してあなたがたがどう考えようと、また、ほかの人がどう思おうと、私は少しも気にしません。この件については、私は自分の判断さえ信用していないのです。 4良心にやましいところはさらさらありませんが、だからといって、安心しきっているわけでもありません。調べた上で判定をお下しになるのは、主ご自身だからです。 5ですから、主がまだここにお帰りにならないうちから、何についても性急に結論を下すことがないように注意しなさい。主が来られる時、すべては明るみに出されます。一人一人の心の奥底までが見通され、ありのままの姿がはっきり見えるようになります。その時、一人一人が、ふさわしい賞賛を神から受けるのです。

特別扱いはやめなさい

6これまで私は、アポロと自分を例にあげて説明してきました。ある人だけを特別扱いしてはならないことを教えたかったのです。神様がお立てになった教師の一人を、他の教師以上に誇ってはなりません。 7いったい何について、そんなに得意になるのですか。あなたの持ちもので、神からいただかなかったものがありますか。その全部が神からいただいたものなら、どうして、さも偉そうにふるまうのですか。また、どうして自力で何かを成し遂げたような態度をとるのですか。 8あなたがたは、自分に必要な霊の食べ物はみな、すでに手にしたと思っているようです。十分に満ち足り、霊的に満足しています。私たちを差し置いて、裕福な王様のようになり、王座にふんぞり返っています。ああ、あなたがたはほんとうに王様になっていたらよかったのです。そうすれば、いつか私たちも、あなたがたと共に君臨できたでしょうに。

9こんなイメージが浮かびます。神様は私たち使徒を、死罪の判決が下された捕虜のように凱旋行列の最後に引き出し、人々や天使の前で見せ物にされたのだ、と。 10信仰のために私たちが愚か者になったと、あなたがたは言います。そういうあなたがたは、もちろん、たいそう賢いクリスチャンなのでしょう。私たちは弱くて、あなたがたは強いのです。人受けのよいあなたがたと違って、私たちは笑いものにされています。 11今の今まで、私たちは飢えと渇きに悩まされ、寒さをしのぐ着物さえありませんでした。自分の家もなく、どこへ行っても冷たくあしらわれるばかりでした。 12また、生活のために、自ら汗水流して働きました。私たちをのろう人たちを、かえって祝福し、危害を加えられても耐え忍び、 13ののしられても、おだやかに答えるのが常でした。それなのに、今でも私たちは、足もとのちりやごみのように扱われています。

14このように書いたのは、あなたがたに恥をかかせるためではありません。愛する子どもとして戒め、さとすためです。 15たとえ、キリストについて教えてくれる人が一万人いたとしても、あなたがたの父はこの私だけであることを忘れないでください。福音を伝えてキリストの救いに導いたのは、この私一人なのですから。 16ですから、お願いがあります。どうか私の模範にならい、同じ行いをしてください。 17その点であなたがたの助けになればと思い、テモテを遣わします。彼は、私がキリストに導いた一人で、主にあって愛し、信頼できる息子だからです。彼は、私自身が実践している信仰者の生き方を、私が行く先々の教会で教えているとおりに、あなたがたに思い出させてくれるでしょう。 18「パウロはこちらへ来て話をつけるのがこわいのだ」と、思い上がっている人たちがいるそうですね。 19しかし、もし主のお許しがあれば、私はすぐにでも行くつもりです。そうすれば、その高慢な人たちが、ただ大きなことを言っているだけか、それとも、ほんとうに神の力を持っているのかがわかるでしょう。 20神の国は、ことばだけのものではありません。神の力によって生きることなのです。 21さあ、あなたがたはどちらを選びますか。私が罰と叱責を持って行くほうですか。それとも、愛とやさしい心とを持って行くほうですか。