尼希米记 11 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

尼希米记 11:1-36

住在耶路撒冷的人

1民众的首领住在耶路撒冷。其余的人用抽签的方式抽出十分之一的人口住在圣城耶路撒冷,剩下的人则住在其他城邑。 2众人为所有自愿住在耶路撒冷的人祝福。

3-4以色列人、祭司、利未人、殿役和所罗门仆人的子孙住在犹大各城自己的家中,有些来自犹大便雅悯的人住在耶路撒冷。以下是住在耶路撒冷犹大省首领:

犹大人中有法勒斯的子孙、乌西雅的儿子亚他雅乌西雅撒迦利雅的儿子,撒迦利雅亚玛利雅的儿子,亚玛利雅示法提雅的儿子,示法提雅玛勒列的儿子。 5此外还有巴录的儿子玛西雅巴录谷何西的儿子,谷何西哈赛雅的儿子,哈赛雅亚大雅的儿子,亚大雅约雅立的儿子,约雅立撒迦利雅的儿子,撒迦利雅示罗尼的儿子。 6住在耶路撒冷法勒斯的子孙共有四百六十八人,都是勇士。

7便雅悯人中有米书兰的儿子撒路米书兰约叶的儿子,约叶毗大雅的儿子,毗大雅歌赖雅的儿子,歌赖雅玛西雅的儿子,玛西雅以铁的儿子,以铁耶筛亚的儿子。 8此外还有迦拜撒来的子孙共九百二十八人。 9细基利的儿子约珥是他们的监督,哈西努亚的儿子犹大耶路撒冷的副官。

10祭司中有雅斤约雅立的儿子耶大雅11以及管理上帝殿的希勒迦的儿子西莱雅希勒迦米书兰的儿子,米书兰撒督的儿子,撒督米拉约的儿子,米拉约亚希突的儿子; 12还有他们在殿里供职的弟兄八百二十二人;还有耶罗罕的儿子亚大雅耶罗罕毗拉利的儿子,毗拉利暗洗的儿子,暗洗撒迦利亚的儿子,撒迦利亚巴施户珥的儿子,巴施户珥玛基雅的儿子; 13还有他们做族长的弟兄二百四十二人;还有亚萨列的儿子亚玛帅亚萨列亚哈赛的儿子,亚哈赛米实利末的儿子,米实利末音麦的儿子; 14还有他们英勇的弟兄一百二十八人。他们的监督是哈基多琳的儿子撒巴第业

15利未人中有哈述的儿子示玛雅哈述押利甘的儿子,押利甘哈沙比雅的儿子,哈沙比雅布尼的儿子。 16还有利未人的族长沙比太约撒拔,他们负责上帝殿外面的事务。 17还有米迦的儿子玛他尼,他是带领祷告和赞美的。米迦撒底的儿子,撒底亚萨的儿子。还有他的助手玛他尼的弟兄八布迦。此外,还有沙姆亚的儿子押大沙姆亚加拉的儿子,加拉耶杜顿的儿子。 18在圣城的利未人共有二百八十四名。

19殿门守卫有亚谷达们,还有他们做殿门守卫的弟兄一百七十二人。 20其他以色列人、祭司和利未人住在犹大各城自己的地方。 21殿役住在俄斐勒,他们的首领是西哈基斯帕

22耶路撒冷利未人的监督是巴尼的儿子乌西巴尼哈沙比雅的儿子,哈沙比雅玛他尼的儿子,玛他尼米迦的儿子,乌西亚萨的子孙,亚萨的子孙是负责圣殿事务的歌乐手。 23歌乐手每天应尽的责任由王决定。 24犹大的儿子谢拉的子孙、米示萨别的儿子毗他希雅帮助王处理民众的事务。

住在其他城邑的人

25至于村庄及其周围的田地,一些犹大人住在基列·亚巴底本叶甲薛和它们周围的村庄, 26耶书亚摩拉大伯·帕列27哈萨·书亚别示巴别示巴周围的村庄, 28洗革拉米哥拿米哥拿周围的村庄, 29音·临门琐拉耶末30撒挪亚亚杜兰和它们周围的村庄,拉吉及其周围的田地,亚西加及其周围的村庄。他们居住的地方从别示巴一直延伸到欣嫩谷。

31便雅悯人住的地方由迦巴起直到密抹亚雅伯特利伯特利周围的村庄, 32亚拿突挪伯亚南雅33夏琐拉玛基他音34哈迭洗编尼八拉35罗德阿挪和匠人之谷。 36一些原本住在犹大利未人被安顿在便雅悯

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nehemiya 11:1-36

Nzika Zatsopano za mu Yerusalemu

1Nthawi imeneyo atsogoleri a anthu ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse anachita maere kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse kuti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulika. Anthu asanu ndi anayi otsalawo ankakhala mʼmidzi yawo. 2Anthu anayamikira onse amene anadzipereka kuti azikhala mu Yerusalemu.

3Aisraeli wamba, ansembe, Alevi, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ndiponso zidzukulu za antchito a Solomoni ankakhala mʼmidzi yawo, aliyense mu dera lake. Koma atsogoleri a chigawo cha Yuda anali atakhazikika mu Yerusalemu. 4Ku Yerusalemu kunkakhalanso anthu ena a mafuko a Yuda ndi Benjamini.

Ena mwa zidzukulu za Yuda ndi awa:

Ataya, mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalaleli. Onsewa anali ana a Perezi. 5Ena ndi awa: Maaseya mwana wa Baruki, mwana wa Koli-Hoze mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yowaribu, Zekariya mwana wa Msiloni. 6Zidzukulu zonse za Perezi, anthu amphamvu zawo amene ankakhala ku Yerusalemu analipo anthu okwanira 468.

7Nazi zidzukulu za Benjamini:

Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yowedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itieli, mwana wa Yesaiya. 8Abale ake anali Gabayi ndi Salaya. Onse pamodzi anali 928. 9Yoweli mwana wa Zikiri ndiye anali mtsogoleri wawo, ndipo Yuda mwana wa Hasenuya ndiye amayangʼanira chigawo cha chiwiri cha mzinda.

10Ansembe anali awa:

Yedaya mwana wa Yowaribu; Yakini; 11Seraya mwana wa Hilikiya mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi amene anali woyangʼanira Nyumba ya Mulungu, 12ndi abale awo, amene ankagwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu. Onse pamodzi anali 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya, 13ndi abale ake, amene anali atsogoleri a mabanja. Onse pamodzi anali 242. Kuphatikiza apo panalinso Amasisai mwana wa Azaireli, mwana wa Ahazayi, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri 14ndi abale ake. Onse pamodzi anali 128 ndipo anali anthu olimba mtima kwambiri. Mtsogoleri wawo wamkulu anali Zabidieli mwana wa Hagedolimu.

15Alevi anali awa:

Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni. 16Sabetayi ndi Yozabadi anali atsogoleri amene ankayangʼanira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu. 17Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu ndiye anali wotsogolera pa mapemphero achiyamiko. Panalinso Bakibukiya amene anali wachiwiri pakati pa abale ake. Kuwonjezera apo panalinso Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni. 18Alevi onse amene anali mu mzinda woyera analipo 284.

19Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Akubu, Talimoni ndi abale awo. Onse pamodzi anali 172.

20Aisraeli ena onse pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ankakhala mʼmizinda ya Yuda, ndipo aliyense ankakhala mʼdera la makolo ake.

21Koma antchito a ku Nyumba ya Mulungu ankakhala pa phiri la Ofeli, ndipo Ziha ndi Gisipa ndiwo anali kuwayangʼanira.

22Wamkulu wa Alevi mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Uzi anali mmodzi wa zidzukulu za Asafu, amene anali oyimba nyimbo pa nthawi zachipembedzo mʼNyumba ya Mulungu. 23Pakuti mfumu inalamula kuti tsiku ndi tsiku pa nthawi zachipembedzo oyimba nyimbowo azikhalapo.

24Petahiya mwana wa Mesezabeli, mmodzi mwa zidzukulu za Zera mwana wa Yuda ndiye ankayimirira Aisraeli pa bwalo la mfumu ya Perisiya.

25Anthu ena a fuko la Yuda ankakhala ku Kiriyati-Ariba ndi midzi yake, ku Diboni ndi midzi yake, ku Yekabizeeli ndi midzi yake, 26ku Yesuwa, Molada, Beti-Peleti, 27Hazari-Suwali, Beeriseba ndi midzi yawo. 28Ku Zikilagi, Mekona ndi midzi yawo, 29ku Eni-Rimoni, Zora, Yarimuti, 30Zanowa, Adulamu ndi midzi yake, ku Lakisi ndi minda yake, ku Beeriseba mpaka ku chigwa cha Hinomu.

31Nazonso zidzukulu za Benjamini zinkakhala mʼdera lawo kuyambira ku Geba mpaka ku Mikimasi, Ayiya, Beteli ndi midzi yake, 32ku Anatoti, Nobu ndi Ananiya, 33ku Hazori, Rama ndi Gitaimu, 34ku Hadidi, Zeboimu ndi Nebalati, 35ku Lodi, Ono ndi ku chigwa cha Amisiri.

36Magulu ena a Alevi a ku Yuda ankakhala ku Benjamini.