马太福音 27:1-66
犹大的下场
1到了清晨,众祭司长和百姓的长老商定要处死耶稣。 2他们把祂绑起来,押送到总督彼拉多那里。
3出卖耶稣的犹大看见耶稣被定了罪,感到很后悔,就把那三十块银子还给祭司长和长老,说: 4“我出卖了清白无辜的人,我犯罪了!”
他们说:“那是你自己的事,跟我们有什么关系?”
5犹大把钱扔在圣殿里,出去上吊自尽了。
6祭司长们捡起银子,说:“这是血钱,不可收进圣殿的库房。” 7他们商议后,决定用这些钱买下陶匠的地作为埋葬异乡人的坟场。 8因此,那块地至今被称为“血田”。 9这就应验了耶利米先知的话:“他们用以色列人给祂估定的三十块银子, 10买了陶匠的一块田,正如主指示我的。”27:10 撒迦利亚书11:12、13;耶利米书19:1‑13;32:6‑9。
耶稣在彼拉多面前受审
11耶稣站在总督面前受审。总督问:“你是犹太人的王吗?”
耶稣说:“如你所言。”
12当祭司长和长老控告祂时,祂一句话也不说。 13彼拉多就问:“你没听见他们对你的诸多控告吗?” 14耶稣仍旧一言不发。彼拉多感到十分惊奇。
15每逢逾越节,总督都会照惯例按民众的意愿释放一个囚犯。 16那时,有一个恶名昭彰的囚犯名叫巴拉巴。 17百姓聚在一起的时候,彼拉多就问他们:“你们要我给你们释放谁?巴拉巴还是被称为基督的耶稣?” 18因为彼拉多知道他们把耶稣押来是出于嫉妒。
19彼拉多正坐堂断案时,他夫人派人来对他说:“你不要插手这个义人的事!我今天在梦中因为这个人受了许多苦。”
20祭司长和长老却怂恿百姓要求释放巴拉巴,处死耶稣。 21总督再次问百姓:“这两个人,你们要我释放哪一个?”他们说:“巴拉巴!”
22彼拉多问:“那么,我怎样处置被称为基督的耶稣呢?”
他们齐声说:“把祂钉在十字架上!”
23彼拉多问:“为什么?祂犯了什么罪?”
他们却更大声地喊叫:“把祂钉在十字架上!”
24彼拉多见再说也无济于事,反而会引起骚乱,于是取了一些水来,在众人面前洗手,说:“流这义人的血,罪不在我,你们自己负责。”
25众人都说:“流祂血的责任由我们和我们的子孙承担!”
26于是,彼拉多为他们释放了巴拉巴,下令将耶稣鞭打后交出去钉十字架。
耶稣受辱
27总督的士兵把耶稣押进总督府,把全营士兵都集合在祂周围。 28他们剥下耶稣的衣服,给祂披上一件朱红色长袍, 29用荆棘编成冠冕,戴在祂头上,又拿一根苇秆放在祂右手里,跪在祂跟前戏弄祂,说:“犹太人的王万岁!” 30然后向祂吐唾沫,拿过苇秆打祂的头。 31他们戏弄完了,就脱去祂的袍子,给祂穿上原来的衣服,把祂押出去钉十字架。
钉十字架
32他们出去的时候,遇见一个叫西门的古利奈人,就强迫他背耶稣的十字架。
33来到一个地方,名叫各各他——意思是“髑髅地”, 34士兵给耶稣喝掺了苦胆汁的酒,祂尝了一口,不肯喝。
35他们把耶稣钉在十字架上,还抽签分了祂的衣服, 36然后坐在那里看守。 37他们在祂头顶上挂了一个牌子,上面写着祂的罪状:“这是犹太人的王耶稣。” 38当时,有两个强盗也被钉在十字架上,一个在祂右边,一个在祂左边。 39过路的人都嘲笑祂,摇着头说: 40“你这要把圣殿拆毁又在三天内重建的人啊,救救自己吧!你要是上帝的儿子,就从十字架上下来吧!”
41祭司长、律法教师和长老也同样嘲讽说: 42“祂救了别人,却救不了自己!祂可是以色列的王啊!现在就从十字架上下来吧!我们就信祂。 43祂信靠上帝,如果上帝喜悦祂,就让上帝来救祂吧!因为祂自称是上帝的儿子。” 44跟祂一同被钉十字架的强盗也这样嘲笑祂。
耶稣之死
45从正午一直到下午三点,黑暗笼罩着整个大地。 46大约下午三点,耶稣大声呼喊:“以利,以利,拉马撒巴各大尼?”27:46 诗篇22:1。意思是:“我的上帝,我的上帝,你为什么离弃我?”
47有些站在旁边的人听见了,就说:“这人在呼叫以利亚。” 48其中一人连忙跑去拿了一块海绵,蘸满酸酒,绑在苇秆上送给祂喝。 49其他人却说:“等着吧,我们看看以利亚会不会来救祂。”
50耶稣又大喊了一声,就断了气。
51就在那时,圣殿里的幔子从上到下裂成两半,大地震动,岩石崩裂, 52坟墓打开,很多死去圣徒的身体复活过来。 53他们在耶稣复活后离开坟墓,进圣城向许多人显现。
54看守耶稣的百夫长和士兵看见地震及所发生的一切,都惊恐万状,说:“这人真是上帝的儿子啊!” 55有好些妇女在远处观看,她们从加利利就跟随了耶稣,服侍祂。 56其中有抹大拉的玛丽亚、雅各和约西的母亲玛丽亚以及西庇太两个儿子的母亲。
封石守墓
57傍晚,从亚利马太来了一位名叫约瑟的有钱人,他是耶稣的门徒。 58他去求见彼拉多,要求领取耶稣的遗体,彼拉多就下令把耶稣的遗体交给他。 59约瑟领了遗体,用干净的细麻布裹好, 60安放在他为自己在岩壁上凿出的新墓穴里,又滚来一块大石头堵住墓口,然后离去。 61那时,抹大拉的玛丽亚和另一个玛丽亚坐在坟墓的对面。
62第二天,就是预备日之后的那天,祭司长和法利赛人一起来见彼拉多,说: 63“总督大人,我们记得那个骗子生前曾说,‘三天之后,我必复活。’ 64所以请你命人看守坟墓三天,以防祂的门徒偷走祂的尸体,然后对百姓说祂已经从死里复活。这样的迷惑会比以前的更厉害!”
65彼拉多说:“你们带上卫兵,去那里严加看守。”
66他们就带着卫兵去了,在墓口的石头上贴上封条,派人看守墓穴。
Mateyu 27:1-66
Yudasi Adzimangirira
1Mmamawa, akulu a ansembe onse ndi akuluakulu anavomerezana kuti aphe Yesu. 2Anamumanga, napita naye kukamupereka kwa bwanamkubwa Pilato.
3Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu. 4Iye anati, “Ndachimwa pakuti ndapereka munthu wosalakwa.”
Iwo anayankha nati, “Ife tilibe nazo kanthu izo ndi zako.”
5Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira.
6Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.” 7Choncho anagwirizana kuti ndalamazo azigwiritse ntchito pogulira munda wa wowumba mbiya kuti ukhale manda alendo. 8Ndi chifukwa chake umatchedwa munda wamagazi mpaka lero lino. 9Pamenepo zimene anayankhula mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa kuti, “Anatenga ndalama zamasiliva makumi atatu mtengo umene anamuyikira Iye anthu a Israeli. 10Ndipo anazigwiritsa ntchito kugula munda wa wowumba mbiya monga mmene Ambuye anandilamulira ine.”
Yesu kwa Pilato
11Pa nthawi yomweyo Yesu anayimirira pamaso pa bwanamkubwa ndipo bwanamkubwayo anamufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?”
Koma Yesu anayankha kuti, “Mwanena ndinu.”
12Pamene akulu a ansembe ndi akuluakulu ankamuneneza, sanayankhe kanthu. 13Kenaka Pilato anamufunsa Iye kuti, “Kodi sukumva zinthu zimene akukunenerazi?” 14Koma Yesu sanayankhe ngakhale mawu amodzi mpaka bwanamkubwa anadabwa kwambiri.
15Pa nthawiyi chinali chizolowezi cha bwanamkubwa kuti pachikondwerero cha Paska amamasula wamʼndende wosankhidwa ndi anthu. 16Pa nthawiyo anali ndi wamʼndende woyipa kwambiri dzina lake Baraba. 17Gulu la anthu litasonkhana, Pilato anawafunsa kuti, “Ndi ndani amene mufuna kuti ndikumasulireni; Baraba kapena Yesu wotchedwa Khristu?” 18Pakuti anadziwa kuti anamupereka Yesu chifukwa cha kaduka.
19Pamene Pilato anakhala pa mpando woweruza, mkazi wake anamutumizira uthenga uwu, “Musachite kanthu ndi munthuyo, ndi wosalakwa pakuti ndavutika kwambiri lero mʼmaloto chifukwa cha munthuyo.”
20Koma akulu a ansembe ndi akuluakulu ananyengerera gulu la anthu kuti apemphe Baraba ndi kuti Yesu aphedwe.
21Bwanamkubwayo anafunsa kuti, “Ndi ndani mwa awiriwa amene mufuna ine ndikumasulireni?”
Iwo anayankha kuti, “Baraba.”
22Pilato anafunsa kuti, “Nanga ndichite chiyani ndi Yesu wotchedwa Khristu?”
Onse anayankha kuti “Mpachikeni!”
23Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wachita choyipa chotani?”
Koma anachita phokoso nafuwula kwambiri kuti, “Mpachikeni!”
24Pilato ataona kuti samaphulapo kanthu, koma mʼmalo mwake chiwawa chimayambika, anatenga madzi nasamba mʼmanja mwake pamaso pa gulu la anthu. Iye anati “Ine ndilibe chifukwa ndi magazi a munthu uyu, ndipo uwu ndi udindo wanu!”
25Anthu onse anayankha nati, “Magazi ake akhale pa ife ndi pa ana athu!”
26Pamenepo anawamasulira Baraba koma analamula kuti Yesu akakwapulidwe, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.
Asilikali Amuchita Chipongwe Yesu
27Pamenepo asilikali abwanamkubwayo anamutenga nalowa naye ku bwalo la milandu ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali namuzungulira Iye. 28Anamuvula malaya ake namuveka Iye malaya ofiira aufumu. 29Ndipo kenaka analuka chipewa chaminga nachiyika pa mutu pake. Anamugwiritsa ndodo mʼdzanja lake lamanja nagwada pamaso pake namuchitira chipongwe nati, “Tikulonjereni Mfumu ya Ayuda.” 30Anamuthira malovu ndipo anatenga ndodo namumenya nayo pa mutu mobwerezabwereza. 31Atamaliza kumuchitira chipongwe, anamuvula malaya aja namuveka malaya ake aja napita naye kokamupachika.
Amupachika Yesu
32Pamene gululi linkatuluka ndi Yesu, anakumana ndi munthu wochokera ku Kurene dzina lake Simoni ndipo anamuwumiriza kunyamula mtanda. 33Anafika ku malo wotchedwa Gologota amene atanthauza kuti malo a bade la mutu. 34Pamenepo anamupatsa vinyo wosakaniza ndi ndulu kuti amwe; koma atalawa anakana kumwa. 35Atamupachika Iye, anagawana zovala zake pochita maere. 36Ndipo anakhala pansi namulonda Iye. 37Pamwamba pa mutu wake analembapo mawu osonyeza mlandu wake akuti, “uyu ndi yesu, mfumu ya ayuda.” 38Achifwamba awiri anapachikidwa pamodzi ndi Iye, mmodzi kudzanja lamanja wina kudzanja lamanzere. 39Ndipo amene amadutsa anamunenera mawu a chipongwe, akupukusa mitu yawo. 40Ndipo anati, “Iwe amene ungapasule Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanga masiku atatu, dzipulumutse wekha! Tsika pa mtandapo ngati ndiwe Mwana wa Mulungu!”
41Chimodzimodzinso akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anamuchitira chipongwe. 42Iwo anati, “Anapulumutsa ena koma sangathe kudzipulumutsa yekha! Ndi mfumu ya Israeli! Mulekeni atsike pa mtanda ndipo tidzamukhulupirira Iye. 43Amadalira Mulungu, mulekeni Mulunguyo amupulumutse tsopano ngati akumufuna pakuti anati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’ ” 44Momwemonso mbala zimene zinapachikidwa naye pamodzi zinamuneneranso zachipongwe.
Kufa kwa Yesu
45Kuyambira 12 koloko masana mpaka 3 koloko, kunachita mdima pa dziko lonse. 46Ndipo nthawi ili ngati 3 koloko, Yesu analira mofuwula nati, “Eloi, Eloi, lama sabakitani!” Kutanthauza kuti, “Mulungu Wanga, Mulungu Wanga, mwandisiyiranji Ine?”
47Ena a oyimirira pamalopo atamva izi anati, “Akuyitana Eliya.”
48Mmodzi wa iwo anathamanga natenga chinkhupule. Anachidzaza ndi vinyo wosasa, nachizika ku mtengo namupatsa Yesu kuti amwe. 49Koma ena onse anati, “Mulekeni tiyeni tione ngati Eliyayo abwere kudzamupulutsa.”
50Ndipo pamene Yesu analiranso mofuwula, anapereka mzimu wake.
51Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika. 52Manda anatsekuka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera mtima amene anafa inaukitsidwa. 53Anatuluka mʼmanda mwawo, ndipo chitachitika chiukitso cha Yesu, anapita mu mzinda woyera naonekera kwa anthu ambiri.
54Mkulu wa asilikali ndi amene ankalondera Yesu ataona chivomerezi ndi zonse zinachitika, anachita mantha, ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu!”
55Amayi ambirimbiri amene ankasamalira Yesu ankaonerera ali patali. Iwo anamutsatira Yesu kuchokera ku Galileya. 56Pakati pawo panali Mariya wa ku Magadala, Mariya amayi ake Yakobo ndi Yosefe ndi amayi a ana a Zebedayo.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
57Pamene kumada, kunabwera munthu wolemera wa ku Arimateyu dzina lake Yosefe amene anali wophunzira wa Yesu. 58Anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu, ndipo Pilato analamula kuti uperekedwe kwa iye. 59Yosefe anatenga mtembowo, nawukulunga nsalu yabafuta. 60Ndipo anawuyika mʼmanda ake atsopano amene anasema mu thanthwe, natsekapo ndi mwala waukulu pa khomo la mandawo nachokapo. 61Mariya wa Magadala ndi Mariya wina anakhala pansi moyangʼanizana ndi mandawo.
Alonda a pa Manda
62Litapita tsiku lokonzekera Sabata, mmawa mwake, akulu a ansembe ndi Afarisi anapita kwa Pilato. 63Iwo anati, “Bwana takumbukira kuti munthu wonyenga uja akanali ndi moyo anati, ‘Pakatha masiku atatu ndidzauka.’ 64Choncho lamulirani kuti manda ake atetezedwe mpaka pa tsiku lachitatu. Chifukwa tikapanda kutero, ophunzira ake angabwere kudzaba mtembo wake ndipo angawuze anthu kuti waukitsidwa kwa akufa. Ndipo chinyengo chomalizachi chidzakhala choyipa kwambiri kusiyana ndi choyamba chija.”
65Pilato anayankha kuti, “Tengani mlonda kalondereni monga mudziwira.” 66Tsono anapita nakatseka manda kolimba ndi kuyikapo chizindikiro ndipo anayikapo mlonda.