Chinese Contemporary Bible (Simplified)

箴言 7:1-27

要远离淫妇

1孩子啊,你要遵从我的吩咐,

把我的诫命珍藏在心中。

2遵守我的诫命,你便存活。

要爱护我的训言,

如爱护眼中的瞳仁。

3要系在你的指头上,

刻在你的心版上。

4你要把智慧当作姊妹,

将悟性视为亲人。

5她们能使你远离淫妇,

远离妓女的甜言蜜语。

6我曾在家里的窗前,

透过窗棂往外观看,

7只见在愚昧的青年人中,

有个无知的青年,

8他穿过靠近淫妇的巷口,

朝她的家门走去,

9趁着日暮黄昏,

借着夜色昏暗。

10看啊!一个妓女打扮、

心术不正的女子出来迎接他。

11她喧嚷放荡,不安分守家,

12有时在街上,有时在广场,

或在各巷口守候。

13她缠着那青年,与他亲吻,

厚颜无耻地说:

14“我今天刚献祭还了愿,

家里有平安祭肉7:14 按犹太律法规定,还愿之后所得的祭肉要在第二天吃完。参考利未记7:16

15因此我出来四处寻找你,

终于找到了你!

16我已经铺好了床,

铺上了埃及的绣花布,

17又用没药、沉香、肉桂熏了床。

18来吧,让我们通宵畅饮爱情,

让我们尽情欢爱!

19因为我丈夫不在家,出远门了。

20他带着钱囊去了,月底才回来。”

21淫妇花言巧语勾引他,

用谄媚的话语诱惑他。

22那青年立刻随她而去,

像走向屠宰场的公牛,

又像掉入陷阱的雄鹿,

23直等到利箭射穿他的肝。

他像只自投网罗的飞鸟,

浑然不知要赔上性命!

24孩子们啊,你们要听从我的话,

留意我口中的训言,

25别让你的心偏向淫妇的道,

步入她的歧途。

26因为她使许多人丧命,

被她杀害的数目众多。

27她的家是通往阴间的路,

引人坠入死亡的殿。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 7:1-27

Za Mkazi Wachigololo

1Mwana wanga, mvera mawu anga;

usunge bwino malamulo angawa.

2Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo;

samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.

3Uchite ngati wawamangirira pa zala zako,

ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.

4Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,”

ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”

5Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo

ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.

6Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga

ndinasuzumira pa zenera.

7Ndinaona pakati pa anthu opusa,

pakati pa anyamata,

mnyamata wina wopanda nzeru.

8Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo,

kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.

9Inali nthawi yachisisira madzulo,

nthawi ya usiku, kuli mdima.

10Ndipo mkaziyo anadzakumana naye,

atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.

11(Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve,

iye ndi wosakhazikika pa khomo.

12Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika,

ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).

13Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona

ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,

14“Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.

Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.

15Choncho ndinabwera kudzakumana nawe;

ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!

16Pa bedi panga ndayalapo

nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.

17Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira

za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.

18Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa;

tiye tisangalatsane mwachikondi!

19Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako;

wapita ulendo wautali:

20Anatenga thumba la ndalama

ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”

21Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo;

amukopa ndi mawu ake oshashalika.

22Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo

ngati ngʼombe yopita kukaphedwa,

monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,

23mpaka muvi utalasa chiwindi chake,

chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe,

osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.

24Tsono ana inu, ndimvereni;

mvetsetsani zimene ndikunena.

25Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu;

musasochere potsata njira zake.

26Paja iye anagwetsa anthu ambiri;

wapha gulu lalikulu la anthu.

27Nyumba yake ndi njira yopita ku manda,

yotsikira ku malo a anthu akufa.