祭司和利未人的名单
1以下是与撒拉铁的儿子所罗巴伯和耶书亚一起回来的祭司和利未人:
祭司有西莱雅、耶利米、以斯拉、 2亚玛利雅、玛鹿、哈突、 3示迦尼、利宏、米利末、 4易多、近顿、亚比雅、 5米雅民、玛底雅、璧迦、 6示玛雅、约雅立、耶大雅、 7撒路、亚木、希勒迦和耶大雅。这些人在耶书亚的时代是祭司和他们弟兄的首领。
8利未人有耶书亚、宾内、甲篾、示利比、犹大和玛他尼。玛他尼及其弟兄负责感恩诗歌。 9他们的弟兄八布迦和乌尼站在他们对面供职。
耶书亚大祭司的后代
10耶书亚生约雅金,约雅金生以利亚实,以利亚实生耶何耶大, 11耶何耶大生约拿单,约拿单生押杜亚。
做族长的祭司
12在约雅金时代,祭司家族的族长有西莱雅家族的米拉雅,耶利米家族的哈拿尼雅, 13以斯拉家族的米书兰,亚玛利雅家族的约哈难, 14米利古家族的约拿单,示巴尼家族的约瑟, 15哈琳家族的押拿,米拉约家族的希勒恺, 16易多家族的撒迦利亚,近顿家族的米书兰, 17亚比雅家族的细基利,米拿民家族的无名氏,摩亚底家族的毗勒太, 18璧迦家族的沙姆亚,示玛雅家族的约拿单, 19约雅立家族的玛特乃,耶大雅家族的乌西, 20撒来家族的加莱,亚木家族的希伯, 21希勒迦家族的哈沙比雅,耶大雅家族的拿坦业。
祭司和利未家族的记录
22在以利亚实、耶何耶大、约哈难和押杜亚的时代,利未人的族长都列入名册;在波斯王大流士执政期间,祭司的族长也都列入名册。 23做族长的利未子孙的名字都记录在历代志上,直到以利亚实的儿子约哈难的时代。
圣殿供职的班次
24哈沙比雅、示利比和甲篾的儿子耶书亚是利未人的首领。他们的弟兄站在他们对面,照上帝仆人大卫的吩咐一班一班地赞美、称颂上帝。 25负责守卫库房的是玛他尼、八布迦、俄巴底亚、米书兰、达们和亚谷。 26他们任职时正值约萨达的孙子、耶书亚的儿子约雅金,尼希米省长和律法教师以斯拉祭司的时代。
尼希米奉献新城墙
27在耶路撒冷的城墙典礼之际,民众把各处的利未人请到耶路撒冷,来称颂、歌唱、敲钹、鼓瑟、弹琴,欢庆典礼。 28歌乐手的子孙从耶路撒冷周围地区、尼陀法人的村庄、 29伯·吉甲,以及迦巴和亚斯玛弗地区被招聚起来,因为歌乐手已在耶路撒冷周围为自己建立了村庄。 30祭司和利未人自洁,然后洁净民众、城门和城墙。
31我率犹大的首领上到城墙上,使称颂的歌乐手分成两大队,一队从城墙上向右前往粪厂门, 32跟在他们后面的有何沙雅和半数的犹大首领, 33还有亚撒利雅、以斯拉、米书兰、 34犹大、便雅悯、示玛雅和耶利米, 35还有一些吹号的祭司,包括约拿单的儿子撒迦利亚,约拿单是示玛雅的儿子,示玛雅是玛他尼的儿子,玛他尼是米该亚的儿子,米该亚是撒刻的儿子,撒刻是亚萨的儿子; 36还有撒迦利亚的弟兄示玛雅、亚撒利、米拉莱、基拉莱、玛艾、拿坦业、犹大、哈拿尼,他们都拿着上帝仆人大卫的乐器。队伍由律法教师以斯拉带领。 37他们经过泉门,沿大卫城的台阶,顺城墙的地势而上,经过大卫的宫殿,走到东面的水门。
38第二队称颂的歌乐手向左走,我和半数的民众在城墙上跟着他们,经过炉楼一直走到宽墙, 39然后又经过以法莲门、古门、鱼门、哈楠业楼、哈米亚楼,远至羊门,之后停在护卫门。 40这两队称颂的歌乐手站在上帝的殿里,我和半数的首领也站在那里, 41同时还有吹号的祭司以利亚金、玛西雅、米拿民、米该亚、以利约乃、撒迦利亚和哈楠尼亚, 42以及玛西雅、示玛雅、以利亚撒、乌西、约哈难、玛基雅、以拦和以谢。歌乐手在伊斯拉希雅的领导下高声歌唱。 43那天,众人献上许多祭物,满心欢喜,因为上帝赐给他们极大的喜乐,连妇孺也都欢喜,耶路撒冷的欢声远处可闻。
预备圣殿的需要
44那天,有人被委派管理库房,把举祭、初熟之物和十一奉献收集在库房里。他们要照律法的规定从各城田地收集祭司和利未人当得的份,因为犹大人对祭司和利未人的供职很满意。 45祭司和利未人遵行上帝的吩咐,遵守洁净的礼。歌乐手和殿门守卫也遵照大卫和他儿子所罗门的命令行事。 46远在大卫和亚萨的时代就有歌乐手,并有赞美、称颂上帝的诗歌。 47在所罗巴伯和尼希米的时代,全体以色列人供应歌乐手和殿门守卫的日常需用,并分出一份给利未人,利未人又分出一份给亚伦的子孙。
Ansembe ndi Alevi
1Ansembe ndi Alevi amene anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa anali awa:
Seraya, Yeremiya, Ezara,
2Amariya, Maluki, Hatusi,
3Sekaniya, Rehumu, Meremoti,
4Ido, Ginetoyi, Abiya
5Miyamini, Maadiya, Biliga,
6Semaya, Yowaribu, Yedaya,
7Salu, Amoki, Hilikiya ndi Yedaya.
Awa ndiye anali atsogoleri a ansembe ndi abale awo pa nthawi ya Yesuwa.
8Alevi anali Yesuwa, Binuyi, Kadimieli, Serebiya, Yuda, ndiponso Mataniya, amene pamodzi ndi abale ake ankatsogolera nyimbo za mayamiko. 9Abale awo, Bakibukiya ndi Uri, ankayimba nyimbo molandizana.
10Yesuwa anabereka Yowakimu, Yowakimu anabereka Eliyasibu, Eliyasibu anabereka Yoyada. 11Yoyada anabereka Yonatani, ndipo Yonatani anabereka Yaduwa.
12Pa nthawi ya Yowakimu, awa ndiwo anali atsogoleri a mabanja a ansembe:
Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya;
wa fuko la Yeremiya anali Hananiya;
13wa fuko la Ezara anali Mesulamu;
wa fuko la Amariya anali Yehohanani;
14wa fuko la Maluki anali Yonatani;
wa fuko la Sebaniya anali Yosefe;
15wa fuko la Harimu anali Adina;
wa fuko la Merayoti anali Helikayi;
16wa fuko la Ido anali Zekariya;
wa fuko la Ginetoni anali Mesulamu;
17wa fuko la Abiya anali Zikiri;
wa fuko la Miniyamini ndi banja la Maadiya anali Pilitayi;
18wa fuko la Biliga anali Samuwa;
wa fuko la Semaya anali Yonatani;
19wa fuko la Yowaribu anali Matenayi;
wa fuko la Yedaya anali Uzi;
20wa fuko la Salai anali Kalai;
wa fuko la Amoki anali Eberi;
21wa fuko la Hilikiya anali Hasabiya;
wa fuko la Yedaya anali Netaneli.
22Pa nthawi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa panalembedwa atsogolera a mabanja a Alevi ndi a ansembe mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo Mperisi. 23Zidzukulu za Levi, makamaka atsogoleri a mabanja awo analembedwa mʼbuku la mbiri mpaka pa nthawi ya Yohanani mwana wa Eliyasibu. 24Ndipo atsogoleri a Alevi awa, Hasabiya, Serebiya, Yesuwa mwana wa Kadimieli ndi abale awo, ankayimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza molandizana. Gulu limodzi linkavomerezana ndi linzake monga mmene Davide munthu wa Mulungu analamulira.
25Mataniya, Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu anali olonda nyumba zosungiramo chuma pa zipata za ku Nyumba ya Mulungu. 26Iwo ndiwo ankatumikira pa nthawi ya Yowakimu mwana wa Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndiponso pa nthawi ya bwanamkubwa Nehemiya ndi wansembe Ezara amene analinso mlembi.
Mwambo Wopereka Khoma la Yerusalemu
27Pa mwambo wopereka khoma la Yerusalemu anayitana Alevi kulikonse kumene ankakhala kuti abwere ku Yerusalemu ku mwambo wopereka khoma kwa Mulungu, mwachimwemwe ndi mothokoza poyimba nyimbo pamodzi ndi ziwiya za malipenga, azeze ndi apangwe. 28Tsono anthu a mabanja a Alevi oyimba nyimbo aja anasonkhana pamodzi kuchokera ku madera onse ozungulira Yerusalemu ndiponso ku midzi ya Anetofati, 29Beti-Giligala ndi ku madera a ku Geba ndi Azimaveti, pakuti oyimbawo anali atamanga midzi yawo mozungulira Yerusalemu. 30Tsono ansembe ndi Alevi anachita mwambo wodziyeretsa. Pambuyo pake anachita mwambo woyeretsa anthu onse ndi khoma la Yerusalemu.
31Ine ndinabwera nawo atsogoleri a dziko la Yuda ndi kukwera nawo pa khoma. Ndipo ndinasankha magulu awiri akuluakulu oyimba nyimbo za matamando. Gulu limodzi linadzera mbali ya ku dzanja lamanja pa khoma mpaka ku Chipata cha Kudzala. 32Pambuyo pawo panali Hosayia, theka la atsogoleri a Yuda aja 33pamodzi ndi Azariya, Ezara, Mesulamu, 34Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya. 35Ena mwa ana a ansembe amene ankayimba malipenga awo anali awa: Zekariya mwana wa Yonatani mwana wa Semaya mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu, 36pamodzi ndi abale awo awa: Semaya, Azareli, Milalai, Gilalayi, Maayi, Netaneli, Yuda ndi Hanani. Onse ankagwiritsa ntchito zida zoyimbira za Davide, munthu wa Mulungu. Tsono Ezara mlembi uja ankawatsogolera. 37Kuchokera ku Chipata cha Kasupe anayenda nakakwera makwerero opita ku mzinda wa Davide pa njira yotsatira khoma, chakumtundu kwa nyumba ya Davide mpaka ku Chipata cha Madzi, mbali ya kummawa.
38Gulu loyimba lachiwiri linadzera mbali ya kumanzere kwa khomalo. Tsono ine ndi theka lina la atsogoleri aja tinkalitsata pambuyo tikuyenda pamwamba pa khomalo. Tinapitirira Nsanja ya Ngʼanjo mpaka ku Khoma Lotambasuka. 39Tinadutsanso Chipata cha Efereimu, Chipata cha Yesana, Chipata cha Nsomba, Nsanja ya Hananeli, Nsanja ya Zana mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo mdipiti uwu unakayima pa Chipata cha Mlonda.
40Choncho magulu onse awiri oyimba nyimbo zothokoza aja anakayima pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. Pamodzi ndi ine ndi theka la atsogoleri aja, 41panalinso ansembe awa akuyimba malipenga: Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya ndi Hananiya. 42Panalinso ansembe awa: Maaseya, Semaya, Eliezara, Uzi, Yehohanani, Milikiya, Elamu ndi Ezeri. Gulu loyimba linkatsogozedwa ndi Yezirahayiya. 43Pa tsiku limenelo anthu anapereka nsembe zambiri ndipo anakondwera chifukwa Mulungu anawapatsa chimwemwe chachikulu. Nawonso akazi ndi ana anakondwera ndipo kukondwa kwa anthu a mu mzinda wa Yerusalemu kunamveka kutali.
44Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi. 45Iwowa ankagwira ntchito ya Mulungu wawo, makamaka mwambo woyeretsa zinthu. Nawonso oyimba nyimbo ndi olonda ku Nyumba ya Mulungu anagwira ntchito zawo monga Davide ndi mwana wake Solomoni analamula. 46Pakuti kalekale, pa nthawi ya Davide ndi Asafu, panali atsogoleri a anthu oyimba nyimbo za matamando ndi nyimbo zoyamika Mulungu. 47Choncho mu nthawi ya Zerubabeli ndi Nehemiya, Aisraeli onse anakapereka mphatso tsiku ndi tsiku kwa anthu oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankayikanso padera chigawo cha zopereka cha Alevi. Nawonso Alevi ankayika padera chigawo cha zopereka cha ansembe, zidzukulu za Aaroni.