耶和华命令百姓重建圣殿
1大流士王执政第二年六月一日,耶和华借着先知哈该对撒拉铁的儿子犹大省长所罗巴伯和约撒答的儿子大祭司约书亚说:
2“万军之耶和华说,‘这些百姓说,重建耶和华殿的时候还没到。’” 3因此,耶和华对先知哈该说: 4“这殿还是一片废墟,你们却住在华丽的房子里。 5万军之耶和华说,你们要认真反省自己的行为。 6你们种多收少,吃不饱,喝不足,穿不暖,挣来的工钱却放在漏口袋中。”
7万军之耶和华说:“你们要认真反省自己的行为。 8你们要上山伐木,重建这殿,好让我欢喜并得到尊崇。这是耶和华说的。 9你们盼望丰收,结果收的很少;你们把收成带回家,我却把它们吹走。这是什么缘故?万军之耶和华告诉你们,‘因为你们都忙于建自家的房子,任由我的殿一片废墟。 10所以,天不降雨露,地无出产。 11我让旱灾临到大地、群山、五谷、葡萄、橄榄等地里的出产以及人畜,使你们一切的劳碌付诸东流。’”
12撒拉铁的儿子犹大省长所罗巴伯、约撒答的儿子大祭司约书亚和所有的余民1:12 “余民”指“从流亡之地归回的人”。听到他们的上帝耶和华借先知哈该所讲的话,都顺服耶和华的话。百姓都敬畏耶和华。 13耶和华的使者哈该向百姓传达耶和华的话,说:“耶和华说,‘我与你们同在。’” 14耶和华感动撒拉铁的儿子犹大省长所罗巴伯、约撒答的儿子大祭司约书亚和所有的余民,他们就动工建造他们的上帝万军之耶和华的殿, 15时值大流士王执政第二年六月二十四日。
Za Kumanga Nyumba ya Yehova
1Chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Yehova anapatsa mneneri Hagai uthenga wopita kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, ndiponso kwa mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki:
2Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu awa amanena kuti, ‘Nthawi sinafike yoti nʼkumanga Nyumba ya Yehova.’ ”
3Tsono Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti, 4“Kodi ino ndi nthawi yoti inuyo muzikhala mʼnyumba zomanga bwino, pamene Nyumba yangayi ikanali bwinja?”
5Tsono zimene Yehova Wamphamvuzonse akunena ndi izi, “Ganizirani bwino njira zanu. 6Mwadzala zambiri, koma mwakolola zochepa. Mumadya, koma simukhuta. Mumamwa, koma ludzu lanu silitha. Mumavala, koma simumva kutentha. Mumalandira malipiro, koma ndalama zanu zimatha ngati mwaziyika mʼthumba lobowoka.”
7Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ganizirani bwino njira zanu. 8Pitani ku mapiri ndipo mukatenge matabwa oti mudzamangire Nyumba yanga, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiramo ulemu,” akutero Yehova. 9“Mumayembekezera zambiri, koma taonani mwapeza pangʼono pokha. Zimene munazibweretsa ku nyumba, Ine ndinazimwaza. Nʼchifukwa chiyani?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Chifukwa Nyumba yanga ikanali bwinja, pamene aliyense wa inu watanganidwa kumanga nyumba yake. 10Choncho, chifukwa cha inu, mitambo yaleka kugwetsa mvula ndipo dziko lapansi laleka kutulutsa zomera. 11Ndabweretsa chilala pa minda ndi pa mapiri, chilala chawumitsa tirigu, mphesa, mafuta a olivi ndi chilichonse chimene chimamera pa nthaka, pa anthu ndi pa ngʼombe, ndi pa ntchito zonse za manja anu.”
12Pamenepo Zerubabeli mwana wa Sealatieli, mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndi anthu onse otsala anamvera mawu a Yehova Mulungu wawo ndi uthenga wa Hagai, chifukwa anatumidwa ndi Yehova Mulungu wawo. Ndipo anthuwo anaopa Yehova.
13Tsono Hagai, mthenga wa Yehova, anapereka kwa anthuwo uthenga uwu wa Yehova: “Ine ndili nanu,” akutero Yehova. 14Kotero Yehova anakhudza mtima wa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, mtima wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso mitima ya anthu onse otsala. Iwo anabwera ndi kuyamba ntchito yomanga Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wawo, 15pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chimodzi, wa chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo.