Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以斯帖记 5:1-14

以斯帖为王和哈曼设宴

1第三天,以斯帖身穿朝服进入王宫内院,面对大殿站立,王在殿里正面朝宫门坐在宝座上。 2王见以斯帖王后站在院内,就施恩给她,向她伸出手中的金杖,以斯帖便上前摸杖头。 3王问道:“以斯帖王后啊,你有什么事?你有何要求?就是半壁江山,也必赐给你!” 4以斯帖回答说:“王若愿意,就请王今天带哈曼来赴我预备的宴席。” 5王说:“快召哈曼来,我们好照以斯帖的话做。”于是王带着哈曼以斯帖预备的宴席。 6席间,王对以斯帖说:“你要什么?我必赐给你。你有何要求?就是半壁江山,也必为你成就。” 7以斯帖回答说:“王啊,我所要、我所求的就是, 8我若得到王的恩宠,王若愿意赐我所要所求的,就请王明天带哈曼再来赴我预备的宴席,到时我一定向王禀明。”

哈曼图谋杀末底改

9那天哈曼出来,心中欢喜快乐。但他看见末底改在宫门前既不起身,也不对他表示畏惧,心中十分恼火。 10哈曼忍怒回到家中,把朋友和妻子细利斯叫来, 11向他们夸耀自己的荣华富贵和儿孙满堂,以及王怎样擢升他,使他位极人臣。 12哈曼又说:“还有,以斯帖王后只请了我随王赴她预备的宴席。她还请我明天随王赴宴。 13但只要我看见犹太末底改坐在宫门口,这一切对我都毫无意义。” 14他妻子细利斯和他所有的朋友对他说:“你可以叫人做一个二十三米高的木架,明天早上求王将末底改吊在上面,然后你可以快乐地随王去赴宴。”哈曼喜欢这个提议,就叫人做了木架。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Estere 5:1-14

Pempho la Estere kwa Mfumu

1Tsiku lachitatu Estere anavala zovala zake zaufumu ndipo anayima mʼbwalo la mʼkati la nyumba yaufumu choyangʼana ku chipinda chachikulu cha mfumu. Mfumu inakhala pa mpando waufumu mʼchipinda chachikulu moyangʼana ku chipata cholowera mʼnyumba yaufumu. 2Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo.

3Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.”

4Ndipo Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni, mfumu, mubwere lero pamodzi ndi Hamani kuphwando limene ndakonzera inu mfumu.”

5Mfumu inati, “Muwuzeni abwere Hamani msanga, kotero kuti tichite monga Estere wapempha.”

Choncho mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Estere anakonza. 6Akumwa vinyo, mfumu inamufunsano Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani tsopano? Chimene uti upemphe ndikupatsa. Chopempha chako ndi chiti? Ngakhale utafuna mpaka theka la ufumu, ndidzakupatsa.”

7Estere anayankha kuti, “Pempho langa ndi chofuna changa ndi ichi: 8Ngati mwandikomera mtima mfumu ndiponso ngati chingakukondweretseni mfumu kundipatsa chimene ndapempha ndi kuchita zimene ndifuna, mubwere mawa inu mfumu ndi Hamani ku phwando limene ndidzakukonzerani. Ndipo ndidzakuyankhani mfumu funso lanu.”

Mkwiyo wa Hamani Ukulabe pa Mordekai

9Tsiku limenelo Hamani anatuluka wokondwa ndi wosangalala kwambiri. Koma ataona Mordekai pa chipata cha mfumu ndi kuti sanayimirire kapena kumupatsa ulemu pamene iye amadutsa, Hamani anamukwiyira kwambiri, 10komabe Hamani anadziletsa ndipo anapita ku nyumba kwake.

Anayitana abwenzi ake pamodzi ndi mkazi wake Zeresi. 11Hamani anawawuza za kuchuluka kwa chuma chake ndi kuti anali ndi ana aamuna ambiri. Anawawuzanso za mmene mfumu inamukwezera ndi kumuyika kukhala woposa nduna ndi olemekezeka onse. 12Hamani anawonjeza kuti, “Ndipotu si zokhazi. Ndine ndekha amene ndayitanidwa pamodzi ndi mfumu kuphwando limene mfumukazi Estere anatikonzera. Ndipo mawa wandiyitananso pamodzi ndi mfumu. 13Koma zonsezi sindikhutira nazo ndikamaona nthawi zonse Myuda uja Mordekai atakhala pa chipata cha mfumu.”

14Mkazi wake Zeresi ndi abwenzi ake onse aja anamuwuza kuti, “Anthu apange mtanda wotalika mamita 23 ndipo mmawa upemphe mfumu kuti anthu akhomerepo Mordekai. Kenaka upite ndi mfumu kuphwando mokondwa.” Hamani anakondwera ndi uphungu umenewu ndipo mtanda unapangidwa.