Miyambo 20:25-30, Miyambo 21:1-4 CCL

Miyambo 20:25-30

Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,”

popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.

Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu

anthu oyipa.

Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova;

imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.

Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu;

chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.

Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,

imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.

Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa,

ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.

Read More of Miyambo 20

Miyambo 21:1-4

Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova;

Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.

Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo,

koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.

Za chilungamo ndi zolondola

ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.

Maso odzikuza ndi mtima wonyada,

zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.

Read More of Miyambo 21