Miyambo 19:23-29, Miyambo 20:1-4 CCL

Miyambo 19:23-29

Kuopa Yehova kumabweretsa moyo;

wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.

Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale;

koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.

Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo;

dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.

Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,

ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.

Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo,

udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.

Mboni yopanda pake imanyoza cholungama,

ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.

Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa,

ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.

Read More of Miyambo 19

Miyambo 20:1-4

Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola;

aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.

Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango;

amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.

Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano,

koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.

Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera;

kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.

Read More of Miyambo 20