Miyambo 15:31-33, Miyambo 16:1-7 CCL

Miyambo 15:31-33

Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo

adzakhala pakati pa anthu anzeru.

Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha,

koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.

Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru,

ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.

Read More of Miyambo 15

Miyambo 16:1-7

Zolinga za mu mtima ndi za munthu,

koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.

Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake,

koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.

Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova,

ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Yehova amachita zonse ndi cholinga chake,

ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.

Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova.

Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.

Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake;

chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.

Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova,

ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.

Read More of Miyambo 16