Mateyu 26:69-75, Mateyu 27:1-10 CCL

Mateyu 26:69-75

Petro Amukana Yesu

Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”

Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”

Kenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.”

Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”

Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”

Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!”

Nthawi yomweyo tambala analira. Ndipo Petro anakumbukira mawu amene Yesu anayankhula kuti, “Tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.” Ndipo anatuluka panja nakalira kwambiri.

Read More of Mateyu 26

Mateyu 27:1-10

Yudasi Adzimangirira

Mmamawa, akulu a ansembe onse ndi akuluakulu anavomerezana kuti aphe Yesu. Anamumanga, napita naye kukamupereka kwa bwanamkubwa Pilato.

Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu. Iye anati, “Ndachimwa pakuti ndapereka munthu wosalakwa.”

Iwo anayankha nati, “Ife tilibe nazo kanthu izo ndi zako.”

Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira.

Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.” Choncho anagwirizana kuti ndalamazo azigwiritse ntchito pogulira munda wa wowumba mbiya kuti ukhale manda alendo. Ndi chifukwa chake umatchedwa munda wamagazi mpaka lero lino. Pamenepo zimene anayankhula mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa kuti, “Anatenga ndalama zamasiliva makumi atatu mtengo umene anamuyikira Iye anthu a Israeli. Ndipo anazigwiritsa ntchito kugula munda wa wowumba mbiya monga mmene Ambuye anandilamulira ine.”

Read More of Mateyu 27