2พงศาวดาร 3 – TNCV & CCL

Thai New Contemporary Bible

2พงศาวดาร 3:1-17

โซโลมอนทรงสร้างพระวิหาร

(1พกษ.6:1-29)

1จากนั้นโซโลมอนทรงเริ่มสร้างพระวิหารขององค์พระผู้เป็นเจ้าบนภูเขาโมริยาห์ในกรุงเยรูซาเล็ม ที่ซึ่งองค์พระผู้เป็นเจ้าทรงปรากฏแก่ดาวิดราชบิดาของโซโลมอน เดิมเป็นลานนวดข้าวของอาราวนาห์3:1 ภาษาฮีบรูว่าโอรนันเป็นอีกรูปหนึ่งของอาราวนาห์ชาวเยบุสที่ดาวิดทรงเตรียมไว้ 2พระองค์ทรงเริ่มการก่อสร้างในวันที่สองเดือนที่สองของปีที่สี่ในรัชกาลของพระองค์

3ฐานรากของพระวิหารของพระเจ้าที่โซโลมอนได้วางนั้นยาว 60 ศอก3:3 คือ ประมาณ 27 เมตร กว้าง 20 ศอก3:3 คือ ประมาณ 9 เมตร เช่นเดียวกับข้อ 4,8,11 และ 13 (โดยใช้หน่วยศอกตามมาตรฐานเดิม) 4มุขที่ด้านหน้าของพระวิหารยาว 20 ศอกตลอดความกว้างของพระวิหาร และสูง 20 ศอก3:4 ภาษาฮีบรูว่าและสูง 120

พระองค์ทรงบุภายในด้วยทองคำบริสุทธิ์ 5ห้องโถงกรุด้วยไม้สนบุด้วยทองคำบริสุทธิ์ ตกแต่งด้วยลวดลายต้นอินทผลัมและโซ่ 6พระองค์ทรงตกแต่งพระวิหารด้วยอัญมณีล้ำค่า และทองคำที่ทรงใช้นั้นมาจากเมืองพารวายิม 7คาน เพดาน วงกบประตู ผนัง และประตูพระวิหาร ล้วนบุด้วยทองคำ และที่ผนังสลักลวดลายเครูบ

8ส่วนที่เป็นอภิสุทธิสถาน ความกว้างได้ขนาดกับความกว้างของพระวิหารคือ 20 ศอก ภายในบุด้วยทองคำเนื้อดีหนักประมาณ 21 ตัน3:8 ภาษาฮีบรูว่า 600 ตะลันต์ 9หมุดทองคำมีน้ำหนักประมาณ 600 กรัม3:9 ภาษาฮีบรูว่า 50 เชเขล ส่วนต่างๆ ของชั้นบนก็บุทองคำเช่นกัน

10ในอภิสุทธิสถาน พระองค์ทรงสร้างเครูบจำลองสองตนหุ้มด้วยทองคำ 11ช่วงกว้างทั้งหมดของปีกเครูบทั้งสองตนรวม 20 ศอก ปีกข้างหนึ่งของเครูบตัวแรกยาว 5 ศอก3:11 คือ ประมาณ 2.3 เมตร เช่นเดียวกับข้อ 12 และ 15 จรดกับด้านหนึ่งของผนังห้อง ปีกอีกข้างหนึ่งซึ่งยาว 5 ศอกเช่นกันจรดกับปีกของเครูบอีกตนหนึ่ง 12ในทำนองเดียวกัน ปีกข้างหนึ่งของเครูบตนที่สองยาว 5 ศอกจรดกับผนังอีกด้านหนึ่ง และปีกอีกข้างหนึ่งซึ่งยาว 5 ศอกเช่นกันจรดกับปีกของเครูบตนแรก 13ปีกของเครูบเหล่านี้กางออกยาว 20 ศอก ทั้งสองตนยืนหันหน้าไปทางห้องโถง3:13 หรือหันหน้าเข้าด้านใน

14มีม่านทำด้วยผ้าลินินเนื้อดี ปักลวดลายเครูบ ด้วยด้ายสีน้ำเงิน ม่วง และแดง

15ที่ด้านหน้าของพระวิหาร มีเสาหานสองต้นสูง 35 ศอก3:15 คือ ประมาณ 16 เมตร มีหัวเสาขนาด 5 ศอก 16โซโลมอนทรงให้ทำโซ่ระย้า3:16 หรืออาจจะเป็นทำโซ่ในสถานนมัสการชั้นในในภาษาฮีบรูวลีนี้มีความหมายไม่ชัดเจนทองคำติดไว้บนหัวเสา และมีทับทิมหนึ่งร้อยผลห้อยติดกับตาข่าย 17พระองค์ตั้งเสาไว้ด้านหน้าของพระวิหาร เสาทางใต้ชื่อยาคีน3:17 คงจะมีหมายความว่า พระองค์ทรงสถาปนาไว้ ส่วนเสาทางเหนือชื่อโบอาส3:17 คงจะมีหมายความว่า ในพระองค์คือกำลัง

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 3:1-17

Solomoni Amanga Nyumba ya Mulungu

1Pamenepo Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu pa Phiri la Moriya, pamene Yehova anaonekera Davide abambo ake. Panali pabwalo lopunthirapo tirigu la Arauna Myebusi, malo amene anapereka Davide. 2Iye anayamba kumanga pa tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake.

3Maziko amene Solomoni anayika pomanga Nyumba ya Mulungu ndi awa: Mulitali munali mamita 27, mulifupi munali mamita asanu ndi anayi (potsata miyeso yakale). 4Chipinda cha polowera mulitali mwake chinali mamita asanu ndi anayi ofanana ndi mulifupi mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali mamita 54.

Iye anakuta nyumbayo mʼkati mwake ndi golide woyengeka bwino. 5Chipinda chachikulu, khoma lake anakhomera matabwa a payini ndipo analikutira ndi golide wabwino ndi kulikongoletsa ndi zithunzi za kanjedza ndi maunyolo. 6Iye anakongoletsa Nyumba ya Mulunguyo ndi miyala yokongola. Ndipo golide amene anagwiritsa ntchito anali golide wa ku Paravaimu. 7Iye anakutira ndi golide mitanda ya ku denga, maferemu a zitseko, makoma ndi zitseko za Nyumba ya Mulungu, ndipo anajambula Akerubi mʼmakoma mwake.

8Iye anamanga Malo Opatulika Kwambiri ndipo mulitali mwake munali mofanana ndi mulifupi mwa Nyumba mamita asanu ndi anayi. Anakuta mʼkati mwake ndi golide wosalala wolemera matani makumi awiri. 9Misomali yagolide imalemera magalamu 570. Anakutanso ndi golide zipinda zapamwamba.

10Ku Malo Opatulika Kwambiri iye anapangako Akerubi awiri achitsulo ndipo anawakuta ndi golide. 11Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo. 12Chimodzimodzinso phiko la Kerubi wachiwiri linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza mbali ina ya khoma la Nyumba ya Mulungu, ndipo linalo limene linalinso loposera mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi woyamba uja. 13Mapiko a Akerubiwa akawatambasula amatalika mamita asanu ndi anayi. Akerubiwa anayimirira pa mapazi awo, kuyangʼana chipinda chachikulu.

14Solomoni anapanga nsalu zotchingira zobiriwira, zapepo ndi zofiira ndi nsalu zofewa zosalala, atajambulapo Akerubi.

15Kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu anamangako zipilala ziwiri, zimene zonse pamodzi zinali zotalika mamita khumi ndi asanu ndi theka; chipilala chilichonse chinali ndi mutu woposera mamita awiri. 16Iye anapanga maunyolo olumikizanalumikizana ndipo anawayika pamwamba pa zipilalazo. Anapanganso makangadza 100 ndipo anawalumikiza ku maunyolo aja. 17Solomoni anayimika nsanamirazo kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu, imodzi mbali ya kummwera ndi inayo mbali ya kumpoto. Nsanamira ya kummwera anayitcha Yakini ndipo ya kumpoto anayitcha Bowazi.