เยเรมีย์ 34 – TNCV & CCL

Thai New Contemporary Bible

เยเรมีย์ 34:1-22

พระดำรัสเตือนเศเดคียาห์

1ขณะที่กษัตริย์เนบูคัดเนสซาร์แห่งบาบิโลนและกองทัพของพระองค์กับมวลอาณาจักรและประชาชนในจักรวรรดิที่ทรงปกครองกำลังสู้รบกับเยรูซาเล็มและหัวเมืองต่างๆ โดยรอบ ก็มีพระดำรัสจากองค์พระผู้เป็นเจ้ามาถึงเยเรมีย์ความว่า 2“พระยาห์เวห์พระเจ้าแห่งอิสราเอลตรัสดังนี้ว่า จงไปบอกกษัตริย์เศเดคียาห์แห่งยูดาห์ว่า ‘องค์พระผู้เป็นเจ้าตรัสดังนี้ เรากำลังจะยกเมืองนี้ให้กษัตริย์บาบิโลน และเขาจะเผามันเสีย 3เจ้าจะหนีไม่พ้นมือเขา แต่จะถูกจับกุมตัวไปให้เขาอย่างแน่นอน เจ้าจะเห็นกษัตริย์บาบิโลนกับตา และเขาจะพูดกับเจ้าซึ่งๆ หน้าและเจ้าจะไปยังบาบิโลน

4“ ‘แต่จงฟังพระสัญญาขององค์พระผู้เป็นเจ้าเถิด กษัตริย์เศเดคียาห์แห่งยูดาห์เอ๋ย องค์พระผู้เป็นเจ้าตรัสเกี่ยวกับเจ้าดังนี้ว่า เจ้าจะไม่ตายเพราะสงคราม 5เจ้าจะตายอย่างสงบสุข และประชาชนจะเผาเครื่องหอมเป็นเกียรติแก่เจ้าเหมือนที่ได้ทำแก่บรรพบุรุษของเจ้าซึ่งเป็นกษัตริย์ที่ครองราชย์ก่อนเจ้า เขาจะร่ำไห้อาลัยเจ้าว่า “โอ้ อนิจจา กษัตริย์ของเรา!” เราเองได้สัญญาไว้ องค์พระผู้เป็นเจ้าประกาศดังนั้น’ ”

6แล้วผู้เผยพระวจนะเยเรมีย์จึงทูลทุกอย่างต่อกษัตริย์เศเดคียาห์แห่งยูดาห์ในเยรูซาเล็ม 7ขณะที่กองทัพบาบิโลนกำลังสู้รบกับเยรูซาเล็มและสู้รบกับลาคิชและอาเซคาห์ซึ่งเป็นหัวเมืองป้อมปราการที่ยังคงต่อสู้อยู่ในยูดาห์

เสรีภาพสำหรับทาส

8พระดำรัสขององค์พระผู้เป็นเจ้ามาถึงเยเรมีย์หลังจากที่กษัตริย์เศเดคียาห์ทรงทำสัญญากับประชาชนในเยรูซาเล็มว่าจะประกาศให้เสรีภาพแก่ทาสทั้งปวง 9ให้ทุกคนปล่อยทาสฮีบรู ไม่ว่าชายหรือหญิง อย่าให้ผู้ใดทำให้ชาวยิวซึ่งเป็นพี่น้องร่วมชาติตกเป็นทาส 10ดังนั้นบรรดาข้าราชบริพารและประชาชนทั้งปวงที่เข้าร่วมในพันธสัญญานี้จึงเห็นพ้องต้องกันที่จะปลดปล่อยทาสชายหญิงของตนให้พ้นจากข้อผูกมัดทุกประการ 11แต่หลังจากนั้นพวกเขาก็เปลี่ยนใจ และจับทาสที่ปล่อยเป็นไทแล้วกลับมาเป็นทาสอีก

12ฉะนั้นจึงมีพระดำรัสจากองค์พระผู้เป็นเจ้ามาถึงเยเรมีย์ว่า 13“พระยาห์เวห์พระเจ้าแห่งอิสราเอลตรัสดังนี้ว่า เราได้ทำพันธสัญญากับบรรพบุรุษของพวกเจ้าเมื่อเรานำคนเหล่านั้นออกมาจากอียิปต์ซึ่งเป็นดินแดนทาส เราสั่งไว้ว่า 14‘ทุกปีที่เจ็ดพวกเจ้าทุกคนต้องปลดปล่อยพี่น้องชาวฮีบรูซึ่งขายตัวเองเป็นทาสของเจ้า หลังจากที่เขารับใช้เจ้ามาตลอดหกปีแล้ว พวกเจ้าต้องปล่อยเขาเป็นไท’34:14 ฉธบ.15:12 แต่บรรพบุรุษของเจ้าทั้งหลายไม่ยอมใส่ใจ ไม่ยอมฟังคำของเรา 15เมื่อเร็วๆ นี้ เจ้าสำนึกผิดและทำสิ่งที่ถูกต้องในสายตาของเรา เจ้าแต่ละคนประกาศให้เสรีภาพแก่พี่น้องร่วมชาติของตน เจ้าถึงกับทำสัญญาต่อหน้าเราในวิหารซึ่งใช้นามของเรา 16แต่บัดนี้เจ้ากลับคำและลบหลู่นามของเรา พวกเจ้าแต่ละคนบังคับทาสชายหญิงซึ่งเจ้าได้ปลดปล่อยให้เป็นอิสระและให้ไปไหนมาไหนได้ตามใจชอบนั้น กลับมาเป็นทาสของเจ้าอีก

17“ดังนั้นองค์พระผู้เป็นเจ้าตรัสดังนี้ว่า เจ้าไม่ได้เชื่อฟังเรา ไม่ได้ประกาศให้อิสรภาพแก่พี่น้องร่วมชาติของเจ้า ดังนั้นเราขอประกาศให้ ‘เสรีภาพ’ แก่เจ้า องค์พระผู้เป็นเจ้าตรัสดังนี้ ‘เสรีภาพ’ที่จะล้มตายด้วยสงคราม โรคระบาด และการกันดารอาหาร เราจะทำให้เจ้าเป็นที่รังเกียจเดียดฉันท์แก่มวลอาณาจักรในโลกนี้ 18ผู้ที่ละเมิดพันธสัญญาของเรา และไม่ทำตามข้อกำหนดของพันธสัญญาซึ่งให้ไว้ต่อหน้าเรา เราจะปฏิบัติต่อพวกเขาเหมือนวัวที่ถูกผ่าออกเป็นสองท่อนและเดินผ่ากลาง 19บรรดาผู้นำของยูดาห์และเยรูซาเล็ม ข้าราชสำนัก ปุโรหิต และประชากรทั้งปวง ที่เดินผ่ากลางสองท่อนของวัวนั้น 20เราจะมอบพวกเขาให้แก่ศัตรูผู้หมายเอาชีวิตของพวกเขา ซากศพของพวกเขาจะตกเป็นเหยื่อของสัตว์ป่าและนกในอากาศ

21“เราจะมอบกษัตริย์เศเดคียาห์แห่งยูดาห์และข้าราชบริพารของเขาแก่ศัตรูผู้ที่มุ่งเอาชีวิตเขาแก่กองทัพกษัตริย์บาบิโลน ซึ่งได้ถอนทัพไปจากพวกเจ้า 22องค์พระผู้เป็นเจ้าประกาศว่าเราจะออกคำสั่งและเราจะนำพวกเขากลับมากรุงนี้อีก พวกเขาจะมาต่อสู้ เอาชนะและเผาเมืองเสีย เราจะทำให้หัวเมืองต่างๆ ของยูดาห์ถูกทิ้งร้าง ไม่มีใครอาศัยอยู่”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 34:1-22

Chenjezo kwa Zedekiya

1Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi gulu lake lonse lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankawalamulira ndiponso anthu a mitundu yonse ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yonse yozungulira Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2“Yehova, Mulungu wa Israeli akuti: Pita kwa Zedekiya mfumu ya Yuda ndipo ukamuwuze kuti Yehova akuti mzinda uno ndidzawupereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni ndipo adzawutentha ndi moto. 3Iweyo sudzapulumuka mʼmanja mwake koma udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka mʼmanja mwake. Udzayiona mfumu ya ku Babuloni maso ndi maso ako ndipo udzayankhula nayo pakamwa ndi pakamwa. Ndipo udzapita ku Babuloni.

4“Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda, imva lonjezo ili la Yehova. Izi ndi zimene Yehova akunena za iwe: Sudzaphedwa pa nkhondo; 5udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.”

6Ndipo mneneri Yeremiya anawuza zonsezi Zedekiya mfumu ya Yuda, mu Yerusalemu. 7Nthawi imeneyi nʼkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda ina yotsala ya Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiye inali mizinda yotetezedwa yotsala ya ku Yuda.

Kumasulidwa kwa Akapolo

8Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya. Nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Zedekiya atachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo awo adzawamasule. 9Aliyense amene anali ndi akapolo a Chihebri, aamuna kapena aakazi awamasule; palibe amene ayenera kusunga mu ukapolo Myuda mnzake. 10Choncho akuluakulu pamodzi ndi anthu onse amene anachita pangano ili anagwirizana kuti amasule akapolo awo aamuna ndi aakazi ndi kuti asawasungenso mu ukapolo. Iwo anachitadi zimenezi ndipo anawamasuladi. 11Koma pambuyo pake anasintha maganizo awo ndi kuwatenganso amuna ndi akazi amene anawamasula aja ndipo anawasandutsanso akapolo.

12Tsono Yehova anawuza Yeremiya kuti: 13“Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Ine ndinachita pangano ndi makolo anu pamene ndinawatulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. Ine ndinati, 14‘Chaka chachisanu ndi chiwiri chilichonse aliyense wa inu ayenera kumasula mʼbale wake wa Chihebri amene anadzigulitsa yekha kwa inuyo. Iyeyo amasulidwe akagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, mumulole apite mwaufulu.’ Komatu makolo anu sanandimvere kapena kusamala konse. 15Posachedwa pomwepa inu munalapa ndi kuchita zinthu zabwino pamaso panga: Aliyense wa inu anamasula mʼbale wake. Ndipo munachita pangano pamaso panga mʼNyumba imene imadziwika ndi dzina langa kuti mudzachitadi zimenezi. 16Koma tsopano mwasintha maganizo anu ndipo mwayipitsa dzina langa. Mwatenganso ukapolo aamuna ndi aakazi amene munawamasula aja kuti apite kumene akufuna. Mwawakakamiza kuti akhalebe akapolo anu.

17“Nʼchifukwa chake Yehova akuti: Inu simunandimvere Ine; simunalengeze kuti abale anu amasulidwe. Chabwino! Ine ndidzakupatsani ufulu; ufulu wake ukhala wophedwa ndi nkhondo, mliri ndi njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. 18Inu simunasunge pangano limene munachita ndi Ine. Simunasamale lonjezo limene munachita pamaso panga. Choncho ndidzakusandutsani ngati mwana wangʼombe uja amene ankamudula pawiri napita pakati pa zigawozo. 19Amene ankadutsa pakati pa zigawozo anali atsogoleri a Yuda ndi Yerusalemu, akuluakulu a bwalo, ansembe ndi anthu onse a mʼdzikomo. 20Onsewa ndidzawapereka kwa adani awo amene akufuna kuwapha. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo za dziko lapansi.

21“Ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda ndi nduna zake kwa adani awo amene akufuna kuwapha, kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni limene nthawi ino layamba kubwerera mʼmbuyo. 22Taonani, Ine ndidzawalamula, akutero Yehova, ndipo ndidzawabweretsanso ku mzinda uno. Adzathira nkhondo mzindawu, kuwulanda ndi kuwutentha. Ndipo Ine ndidzasandutsa chipululu mizinda ya Yuda kotero kuti palibe amene adzakhalemo.”