ปัญญาจารย์ 10 – TNCV & CCL

Thai New Contemporary Bible

ปัญญาจารย์ 10:1-20

1แมลงวันตายทำให้น้ำหอมเหม็นคลุ้งฉันใด

ความโง่เขลานิดหน่อยก็อาจบั่นทอนสติปัญญาและเกียรติฉันนั้น

2ใจของคนฉลาดไขว่คว้าหาความถูกต้อง

ส่วนใจของคนโง่เอียงไปสู่ความชั่วร้าย

3คนโง่แม้เดินไปตามถนนหนทาง

ก็ยังไม่มีสำนึก

และทำให้คนดูออกว่าเขาโง่แค่ไหน

4หากเจ้านายโกรธเคืองท่าน

อย่าเพิ่งทิ้งหน้าที่ไป

ความสงบสยบความผิดพลาดใหญ่หลวงได้

5ข้าพเจ้าได้เห็นความชั่วร้ายอีกอย่างหนึ่งภายใต้ดวงอาทิตย์

เป็นความผิดที่เกิดขึ้นจากผู้ครอบครอง

6คือให้คนโง่ได้ตำแหน่งสูง

ขณะที่คนร่ำรวยอยู่ในตำแหน่งต่ำต้อย

7ข้าพเจ้าเห็นทาสนั่งบนหลังม้า

ขณะที่เจ้านายเดินเท้าไปเหมือนทาส

8คนที่ขุดหลุมอาจจะตกลงไปในหลุม

คนที่รื้อกำแพงอาจจะถูกงูกัด

9คนที่สกัดหินอาจได้รับบาดเจ็บเพราะหิน

คนที่เลื่อยซุงอาจได้รับอันตรายจากซุง

10หากขวานทื่อ

และไม่ได้ลับให้คม

เวลาใช้ก็ต้องออกแรงมากขึ้น

แต่ความเชี่ยวชาญจะนำความสำเร็จมาให้

11หมองูก็ไม่มีประโยชน์

หากเขาถูกกัดก่อนที่จะสะกดมันได้

12ถ้อยคำของคนฉลาดนั้นน่าฟัง

แต่คนโง่ย่อยยับเพราะลมปากของตัวเอง

13พอเริ่มพูดก็แสดงความโง่

พูดจบก็ยิ่งบ้าเลวทราม

14และต่อความยาวสาวความยืดไม่รู้จบ

ไม่มีใครรู้ว่าจะเกิดอะไรขึ้น

ใครเล่าจะบอกเขาได้ว่าจะเกิดอะไรขึ้นในภายหลัง?

15งานของคนโง่ทำให้เขาอ่อนระโหย

เขาไม่รู้จักทางเข้าเมือง

16วิบัติแก่เจ้า ดินแดนซึ่งมีคนรับใช้10:16 หรือเด็กเป็นกษัตริย์

และบรรดาเจ้านายกินเลี้ยงเฮฮากันตั้งแต่เช้า

17ความสุขมีแก่เจ้า ดินแดนที่กษัตริย์ของเจ้ามีคุณธรรมสูง

และเจ้านายรู้จักกินดื่มในเวลาอันควร

เพื่อให้มีกำลังวังชา ไม่ใช่เพื่อเมามาย

18หากผู้ใดเกียจคร้าน จันทัน10:18 หรือคานค้ำหลังคาก็ผุพัง

หากงอมืองอเท้า เรือนก็รั่ว

19งานเลี้ยงสังสรรค์ให้เสียงหัวเราะ

เหล้าองุ่นให้ชีวิตรื่นเริง

แต่เงินคือคำตอบสำหรับทุกสิ่ง

20อย่าแช่งด่ากษัตริย์ แม้แต่ในความคิดคำนึง

หรือแช่งด่าคนรวยในห้องนอนของท่าน

เพราะนกในอากาศอาจจะคาบวาจาของท่านไป

และนกที่โบยบินอาจจะรายงานสิ่งที่ท่านพูด

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 10:1-20

1Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira,

choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.

2Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino,

koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa.

3Chitsiru ngakhale chikamayenda mu msewu,

zochita zake ndi zopanda nzeru

ndipo chimaonetsa aliyense kuti icho ndi chitsirudi.

4Ngati wolamulira akukwiyira,

usachoke pa ntchito yako;

kufatsa kumakonza zolakwa zazikulu.

5Pali choyipa chimene ndinachiona pansi pano,

kulakwitsa kumene kumachokera kwa wolamulira:

6Zitsiru amazipatsa ntchito zambiri zapamwamba,

pamene anthu olemera amawapatsa ntchito zotsika.

7Ndaona akapolo atakwera pa akavalo,

pamene akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.

8Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha;

amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.

9Amene amaphwanya miyala adzapwetekedwa ndi miyalayo;

amene amawaza nkhuni adzapwetekedwa nazo.

10Ngati nkhwangwa ili yobuntha

yosanoledwa,

pamafunika mphamvu zambiri potema,

koma luso limabweretsa chipambano.

11Nʼkopanda phindu kudziwa kuseweretsa njoka

ngati njokayo yakuluma kale.

12Mawu a pakamwa pa munthu wanzeru ndi okondweretsa,

koma chitsiru chidzawonongedwa ndi milomo yake yomwe.

13Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa;

potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala

14ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu.

Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo,

ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?

15Chitsiru chimatopa msanga ndi ntchito yochepa;

ndipo sichikhala ndi mphamvu zobwererera ku mudzi.

16Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana,

ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.

17Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka

ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake,

kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.

18Ngati munthu ndi waulesi, denga lake limaloshoka;

ngati manja ake ndi alobodo nyumba yake imadontha.

19Phwando ndi lokondweretsa anthu,

ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo,

koma ndalama ndi yankho la chilichonse.

20Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako,

kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako,

pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako

nʼkukafotokoza zomwe wanena.