Leviticus 18 – TCB & CCL

Tagalog Contemporary Bible

Leviticus 18:1-30

Ang mga Ipinagbabawal na Gawaing Mahahalay

1Inutusan ng Panginoon si Moises 2na sabihin ito sa mga taga-Israel:

Ako ang Panginoon na inyong Dios. 3Huwag nʼyong gawin ang mga ginagawa ng mga taga-Egipto, kung saan kayo tumira noon. Huwag din ninyong gayahin ang mga ginagawa ng mga taga-Canaan na pagdadalhan ko sa inyo. 4-5Dapat ninyong sundin ang aking mga utos at mga tuntunin dahil ang mga susunod dito ay mabubuhay. Ako ang Panginoon na inyong Dios.

6Huwag kayong sumiping sa malapit ninyong kamag-anak. Ako ang Panginoon.

7-8Huwag mong ilagay sa kahihiyan ang iyong ama sa pamamagitan ng pagsiping sa iyong ina o sa iba pa niyang asawa.

9Huwag kang sumiping sa iyong kapatid na babae, kahit na kapatid mo siya sa ama o sa ina, kahit na lumaki siya sa inyo o hindi.

10Huwag kang sumiping sa iyong apong babae dahil magbibigay ito sa iyo ng kahihiyan.

11Huwag kang sumiping sa anak na babae ng iyong ama sa iba niyang asawa, dahil kapatid mo rin siya.

12-13Huwag kang sumiping sa iyong tiyahin na kapatid ng iyong ama o ina.

14Huwag mong ilalagay sa kahihiyan ang iyong tiyuhin sa pamamagitan ng pagsiping sa kanyang asawa, dahil tiyahin mo rin siya.

15Huwag kang sumiping sa iyong manugang na babae dahil asawa siya ng iyong anak.

16Huwag kang sumiping sa iyong hipag na babae dahil itoʼy magbibigay ng kahihiyan sa iyong kapatid.

17Huwag kang sumiping sa anak o apo ng babaeng sinipingan mo noon, dahil baka anak o apo mo iyon at itoʼy nakakahiya.

18Huwag kang mag-asawa ng kapatid na babae ng iyong asawa habang buhay pa ang iyong asawa.

19Huwag kang sumiping sa babaeng may buwanang dalaw dahil itinuturing siyang marumi.

20Huwag kang sumiping sa asawa ng iba dahil kapag ginawa mo ito, ituturing kang marumi.

21Huwag mong ibibigay ang iyong anak para ihandog sa dios na si Molec, dahil iyan ay paglapastangan sa aking pangalan na iyong Dios. Ako ang Panginoon.

22Huwag kang sumiping sa kapwa mo lalaki o kapwa mo babae dahil kasuklam-suklam ito.

23Huwag kang sumiping sa hayop dahil ito ay napakasama at ikaw ay ituturing na marumi kapag ginawa mo iyon.

24Huwag ninyong dumihan ang inyong sarili sa pamamagitan ng paggawa ng ganitong mga gawain dahil ito ang nagparumi sa mga taong pinaalis ko sa lupaing ibinigay ko sa inyo. 25-28At kahit ang lupain ay nadungisan dahil sa ginawa nilang iyon. Pinadalhan ko ng mga salot ang lupaing iyon para silaʼy magsialis doon. Pero kayong mga katutubong Israelita at mga dayuhang naninirahang kasama ninyo, huwag ninyong gawin ang kasuklam-suklam na gawaing iyon, kundi sundin ninyo ang mga tuntunin at mga kautusan ko. Sapagkat kung dudungisan din ninyo ang lupaing iyon, sa pamamagitan ng paggawa ng mga gawaing iyon, paaalisin ko rin kayo sa lupaing iyon katulad ng mga taong unang tumira roon. 29Ang sinumang gumawa ng mga kasuklam-suklam na gawaing ito ay huwag na ninyong ituring na kababayan. 30Kaya sundin ninyo ang iniuutos ko sa inyo at huwag ninyong susundin ang mga kasuklam-suklam na ginawa ng mga taong nauna sa inyo, para hindi ninyo madungisan ang inyong sarili katulad nila. Ako ang Panginoon na inyong Dios.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 18:1-30

Kugonana Koletsedwa

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 3Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo. 4Inu muzimvera malamulo anga ndipo muzisamalitsa kutsatira malangizo anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 5Choncho sungani malangizo ndi malamulo anga, popeza munthu amene amvera zimenezi adzakhala ndi moyo. Ine ndine Yehova.

6“ ‘Munthu aliyense asagonane ndi wachibale wake. Ine ndine Yehova.

7“ ‘Usachititse manyazi abambo ako pogonana ndi amayi ako. Iwo ndi amayi ako. Usagonane nawo.

8“ ‘Usagonane ndi mkazi wa abambo ako (osakhala amayi okubala). Ukatero ukuchititsa manyazi abambo ako.

9“ ‘Usagonane ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa abambo ako, kapena mwana wamkazi wa amayi ako, kaya anabadwira mʼnyumba mwanu kapena kwina.

10“ ‘Usagonane ndi mdzukulu wako: mwana wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wa mwana wako wamkazi. Kutero nʼkudzichotsa ulemu.

11“ ‘Usagonane ndi mwana wamkazi wa mkazi wa abambo ako, amene abambo akowo anabereka; popeza ameneyo ndi mlongo wako.

12“ ‘Usagonane ndi mlongo wa abambo ako; popeza ameneyo ndi thupi limodzi ndi abambo ako.

13“ ‘Usagonane ndi mchemwali wa amayi ako chifukwa ameneyo ndi thupi limodzi ndi amayi ako.

14“ ‘Usachititse manyazi mchimwene wa abambo ako pogonana ndi mkazi wake popeza amenewo ndi azakhali ako.

15“ ‘Usagonane ndi mpongozi wako popeza ameneyo ndi mkazi wa mwana wako. Choncho usamuchititse manyazi.

16“ ‘Usagonane ndi mkazi wa mchimwene wako popeza potero ukuchititsa manyazi mʼbale wakoyo.

17“ ‘Usagonane ndi mkazi ndiponso mwana wake wamkazi. Usagonane ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi limodzi ndi mkaziyo. Kutero ndikuchita chinthu choyipa kwambiri.

18“ ‘Usakwatire mchemwali wa mkazi wako ndi kumagonana naye mkazi wakoyo ali moyo ngati wopikisana naye.

19“ ‘Usamuyandikire mkazi kuti ugonane naye pa nthawi yake yosamba.

20“ ‘Usagonane ndi mkazi wa mnzako ndi kudziyipitsa naye.

21“ ‘Usapereke mwana wako aliyense kuti akhale nsembe yamoto kwa Moleki ndi kuyipitsa dzina la Yehova. Ine ndine Yehova.

22“ ‘Usagonane ndi mwamuna ngati mkazi; chimenecho ndi chinthu chonyansa.

23“ ‘Usagonane ndi nyama ndi kudziyipitsa nayo. Mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agonane nayo. Chimenecho ndi chisokonezo.

24“ ‘Musadzidetse ndi zinthu zimenezi chifukwa umo ndi mmene mitundu ina imene ndikuyithamangitsa pamaso panu inadzidetsera. 25Choncho dziko linayipa ndipo ndinalilanga chifukwa cha tchimo lake. Motero dzikolo linasanza anthu ake okhalamo. 26Koma inu mukasunge malangizo ndi malamulo anga. Mbadwa ndiponso alendo amene akukhala pakati panu asakachite china chilichonse cha zinthu zonyansazi, 27pakuti zinthu zonsezi ndi zomwe ankachita anthu amene ankakhala mʼdzikomo inu musanafike, ndipo dziko linayipitsidwa. 28Koma inu musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mutaliyipitsa monga linasanzira mitundu imene imakhalamo inu musanafike.

29“ ‘Aliyense wochita zinthu zonyansa zimenezi achotsedwe pakati pa anthu anzake. 30Choncho mverani malangizo anga oletsa kuchita miyambo yonyansayi imene ankatsatira anthu amene analipo inu musanafike ndi kudziyipitsa nayo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”