Skutky 27 – SNC & CCL

Slovo na cestu

Skutky 27:1-44

Pavel se plaví do Říma

1Přišel čas transportu vězňů do Itálie. Byl do něho zařazen také Pavel a my s Makedoncem Aristarchem z Tesaloniky jako jeho průvodci. Transportu velel důstojník Julius z císařského oddílu. 2Najal loď, která obeplouvala pobřeží Malé Asie a na cestě k jejímu severnímu cípu měla udělat řadu zastávek. 3Když jsme druhý den přistáli v Sidónu, dovolil důstojník Julius, který zacházel s Pavlem skutečně lidsky, aby navštívil ve městě své přátele; ti ho vybavili na cestu vším potřebným. 4Kvůli nepříznivému větru jsme se dále plavili mezi Kyprem a pevninou; 5minuli jsme Kilikii a Pamfylii a přistáli nakonec v lykijské Myře. 6Tam velitel najal alexandrijskou loď, která měla namířeno do Itálie, a převedl nás na ni. 7-8Po několik dalších dní byla plavba obtížná a v Knidu jsme ani nemohli přistát, jak silný vítr vál od pevniny. Propluli jsme tedy mezi Krétou a ostrovem Salmonou a s námahou jsme se drželi jižního pobřeží Kréty až do „Dobrých přístavů“ u Lasaia.

9Měli jsme zpoždění, byl již konec září a plavba přes otevřené moře je v tomto období nebezpečná. Pavel jako zkušený cestovatel varoval: 10„Jestli teď vyplujete, dáváte v sázku nejen loď a její náklad, ale i životy nás všech.“ 11-12Důstojník však dal víc na kapitána a majitele lodi, kteří radili sledovat ještě dále krétské pobřeží až k jihozápadnímu přístavu Foiniku. Tvrdili, že je vhodnější k přezimování lodi než Lasaia. Zdálo se, že se to podaří, protože začal vát jižní vítr. Tak jsme tedy zvedli kotvy.

Bouře na moři

13Zanedlouho se však zvedl od Kréty silný severovýchodní vítr, kterému loď nemohla vzdorovat, a ten nás unášel dál a dál od krétského pobřeží. 14-16Přišel tak nenadále, že jsme ani nestačili naložit do lodi záchranný člun, obvykle vlečený vzadu. To se nám podařilo až v závětří ostrůvku Klauda. 17Námořníci stáhli lany trup lodi, aby lépe odolával, a spustili vlečnou kotvu, abychom snad v plné rychlosti nenajeli na nebezpečné mělčiny Syrtis u afrického pobřeží. 18Druhý den vlny už dosahovaly nebezpečné výše, takže jsme museli zmenšit ponor lodi: plavci vyházeli část nákladu 19a další den i část lodní výstroje. 20Po mnoho dní bylo zataženo, neviděli jsme slunce ani hvězdy, takže jsme ztratili orientaci a divoká bouře stále zmenšovala naši naději na záchranu.

21Po celou tu dobu nikdo na lodi ani nepomyslel na jídlo. Pavel vyšel na palubu a oslovil námořníky: „Přátelé, měli jste dát na mne a přezimovat na Krétě v ‚Dobrých přístavech‘. Byli byste si ušetřili spoustu těžkostí a škod. 22Ale neklesejte na mysli, není všechno ztraceno: nikdo z nás nezahyne, jen loď vezme za své. 23Dnes v noci se mi zjevil posel Boha, kterému náležím a sloužím, 24a řekl mi: ‚Neboj se, Pavle, máš ještě stát před císařem! Jako dar ti Bůh přidá životy všech, kteří se s tebou plaví.‘ 25Odvahu, přátelé! Já věřím svému Bohu, že se jeho vzkaz doslova splní. 26Máme se zachránit na nějakém ostrově.“

Ztroskotání

27Už čtrnáctou noc jsme byli unášeni Středozemním mořem do neznáma, když kolem půlnoci hlídka hlásila zemi na obzoru. 28Námořníci spustili olovnici a naměřili hloubku čtyřiceti metrů a po chvíli už jen třicet metrů. 29Dostali strach, že bychom mohli potmě najet na skaliska, a tak vyhodili přes záď čtyři kotvy a všichni jsme toužebně očekávali svítání. 30Ale námořníci chtěli zrádně opustit ohroženou loď. Spustili na moře záchranný člun, jako že roztáhnou ještě další kotvy z přídi. 31Pavel však postřehl jejich pravý úmysl a řekl důstojníkovi a vojákům: „Pozor na ně, bez nich se nezachráníte!“ 32Vojáci tedy přesekli lana člunu a nechali ho odplout prázdný.

33Ještě než se rozednilo, přesvědčoval Pavel posádku: „Čtrnáct dní tu zápolíte, hlídáte a přitom skoro nic nedáte do úst. 34Alespoň teď se pořádně najezte, ať máte sílu dostat se na břeh. Řekl jsem vám přece, že se nikomu nic nestane.“ 35Vzal chléb, přede všemi za něj Bohu nahlas poděkoval a začal jíst. 36Ostatní to povzbudilo a dali se také do jídla. 37Bylo nás tam všech dohromady dvě sta sedmdesát šest. 38Když jsme se najedli, vyhazovali námořníci do moře obilí, hlavní náklad, aby zmenšili ponor lodi.

39Konečně se rozednilo. Viděli jsme před sebou pás plochého pobřeží se zálivem, ale nikdo tu zemi neznal. Plavci se chtěli pokusit o přistání v zátoce. 40Kotvy nevytahovali, ale odsekli kotevní lana, odvázali upevněné kormidlo a s přední plachtou na stožáru se pustili ke břehu. 41Brzy jsme však najeli na písčinu a loď uvázla. Příď se zabořila pevně do dna a prudký příboj začal rozbíjet záď. 42Vojáci se už chystali podle římských pravidel pro takové situace pobít všechny vězně, aby některý z nich neodplaval na břeh a neutekl. 43Velitel však chtěl zachovat Pavla při životě, vzal na sebe odpovědnost a nedovolil jim to. Nařídil, aby nejprve skočili přes palubu ti, kdo umějí plavat, 44ostatní ať si opatří kusy dřeva z lodi a všichni ať se snaží dostat na břeh. Tak nikdo neutonul a všichni se v pořádku dostali na souš.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 27:1-44

Paulo Apita ku Roma

1Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa sitima ya pa madzi, anamupereka Paulo pamodzi ndi a mʼndende ena kwa msilikali wolamulira asilikali 100, dzina lake Yuliyo, amene anali wa gulu la asilikali lotchedwa, Gulu la Mfumu. 2Tinakwera sitima ya pamadzi yochokera ku Adramutiyo imene inali yokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tinanyamuka. Aristariko, wa ku Makedoniya wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe.

3Mmawa mwake tinafika ku Sidoni; ndipo Yuliyo, mokomera mtima Paulo, anamulola kupita kwa abwenzi ake kuti akamupatse zosowa zake. 4Kuchokera kumeneko tinayambanso ulendo pa nyanja ndipo tinadutsa kumpoto kwa chilumba cha Kupro chifukwa mphepo imawomba kuchokera kumene ife timapita. 5Titawoloka nyanja mbali ya gombe la Kilikiya ndi Pamfiliya, tinakafika ku Mura, mzinda wa ku Lukia. 6Kumeneko wolamulira asilikali 100 uja anapeza sitima ya pamadzi ya ku Alekisandriya imene imapita ku Italiya, ndipo anatikweza mʼmenemo. 7Tinayenda pangʼonopangʼono kwa masiku ambiri ndipo tinakafika kufupi ndi Knido movutikira. Pamene mphepo sinatilole kupitirira ulendo wathu molunjika, tinadzera kummwera kwa chilumba cha Krete, moyangʼanana ndi Salimoni. 8Timayenda movutikira mʼmbali mwa chilumbacho ndipo tinafika pa malo wotchedwa Madooko Okoma, pafupi ndi mzinda wa Laseya.

9Tinataya nthawi yayitali, ndipo kuyenda pa nyanja kunali koopsa chifukwa nʼkuti tsopano nthawi yosala kudya itapita kale. Choncho Paulo anawachenjeza kuti, 10“Anthu inu, ine ndikuona kuti ulendo wathuwu ukhala woopsa ndipo katundu ndi sitima ziwonongeka, ngakhalenso miyoyo yathu.” 11Koma wolamulira asilikali 100 uja, mʼmalo momvera zimene Paulo amanena, anatsatira malangizo a woyendetsa sitimayo ndiponso mwini wa sitimayo. 12Popeza kuti dookolo silinali labwino kukhalako nthawi yozizira anthu ambiri anaganiza kuti tichoke. Ife tinkayembekeza kukafika ku Foinikisi ndi kukhala kumeneko nthawi yachisanu. Ili linali dooko la ku Krete, limene limaloza kummwera cha kumadzulo ndiponso kumpoto cha kumadzulo.

Namondwe pa Nyanja

13Mphepo yochokera kummwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anthuwo anaganiza kuti apeza chimene amafuna; kotero analowetsa nangula ndipo anayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Krete. 14Pasanathe nthawi yayitali, mphepo yamkuntho yotchedwa Eurokulo, inayamba kuwomba kuchokera ku chilumbacho. 15Mphepo yamkunthoyo inawomba sitima ija ndipo sinathe kulimbana nayo, kotero ife tinayigonjera ndi kuyamba kutengedwa nayo. 16Tikudutsa mʼmbali mwa kachilumba kakangʼono kotchedwa Kawuda, tinavutika kuti tisunge bwato lopulumukiramo. 17Anthuwo atakweza bwatolo mʼsitima, anakulunga zingwe sitimayo kuti ayilimbitse. Poopa kuti angakagunde mchenga wa ku Surti, iwo anatsitsa nangula ndi kuyilola sitima kuti idzingoyenda ndi mphepo. 18Ife tinavutika kwambiri ndi namondwe kotero kuti mmawa mwake tinayamba kuponya katundu mʼmadzi. 19Pa tsiku lachitatu anaponya mʼnyanja zipangizo za mʼsitima ndi manja awo. 20Sitinaone dzuwa kapena nyenyezi kwa masiku ambiri ndipo namondwe anapitirira kuwomba kwambiri, pomaliza ife tonse tinalibenso chiyembekezo choti nʼkupulumuka.

21Anthu aja atakhala nthawi yayitali osadya, Paulo anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga oti tisachoke ku Krete: zonsezi sizikanawonongeka ndi kutayika. 22Koma tsopano ndikuti limbani mtima, chifukwa palibe aliyense wa inu amene adzataya moyo wake; koma sitima yokhayi idzawonongeka. 23Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine, 24ndipo iyeyu anati, ‘Usachite mantha, Paulo. Ukuyenera kukayima pamaso pa Kaisara; ndipo Mulungu mwa kukoma mtima kwake wakupatsa miyoyo ya anthu onse amene ukuyenda nawo.’ 25Tsono limbani mtima, anthu inu, pakuti ine ndili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu kuti zichitika monga momwe wandiwuzira. 26Komabe tiyenera kukatsakamira pa chilumba china chake.”

Kuwonongeka kwa Sitima

27Pakati pa usiku wa tsiku la khumi ndi chinayi tikukankhidwabe ndi mphepo mʼnyanja ya Adriya, oyendetsa sitimayo anazindikira kuti timayandikira ku mtunda. 28Iwo anatenga choyezera kuzama kwa nyanja ndi kupeza kuti kuzama kwake kunali mamita 36. Atayendanso pangʼono anatenganso choyezera chija napeza kuti kuzama kwake kunali 27. 29Poopa kuti tingagunde miyala, iwo anatsitsira anangula anayi mʼmadzi kumbuyo kwa sitimayo ndipo tinapemphera kuti kuche. 30Pofuna kuthawa mʼsitimayo, oyendetsa aja anatsitsira mʼnyanja bwato lopulumukiramo nʼkumachita ngati akufuna kutsitsira anangula mʼnyanjamo kutsogolo kwa sitimayo. 31Pamenepo Paulo anawuza wolamulira asilikali uja ndi asilikaliwo kuti, “Ngati anthu awa sakhala mʼsitima muno, inu simungapulumuke.” 32Pamenepo asilikaliwo anadula zingwe za bwatolo ndipo linagwera mʼmadzi.

33Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anawawumiriza anthu onse kuti adye. Iye anati, “Kwa masiku khumi ndi anayi mwakhala mukuda nkhawa ndipo simumadya kanthu kalikonse. 34Tsopano ine ndikukupemphani kuti mudye. Muyenera kudya kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe wa inu adzataye ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pake.” 35Paulo atanena zimenezi, anatenga buledi nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo ananyema bulediyo nayamba kudya. 36Onse analimba mtima nayamba kudyanso. 37Tonse pamodzi mʼsitimamo tinalipo anthu 276. 38Onse atadya, nakhuta anapeputsa sitimayo potaya tirigu mʼnyanja.

39Kutacha, anthu sanazindikire dzikolo, koma anaona pomwe sitima zimayimapo pamodzi ndi mchenga wa pa gombe. Iwo anaganiza zokocheza sitimayo kumeneko ngati zikanatheka kutero. 40Atadula anangula aja, nawasiya mʼnyanja, pa nthawi yomweyo anamasula zingwe zimene anamangira zowongolera sitimayo. Kenaka anayimika chinsalu chimene mphepo imakankha kuti sitima iyende, ndipo anayamba kupita ku gombe. 41Koma sitimayo inagunda mchenga wobisika ndipo inayima. Mbali ya kutsogolo ya sitimayo inakanirira ndipo sinathe kuyendanso, ndipo mbali yakumbuyo inasweka ndi kuwomba kwa mafunde.

42Asilikali anaganiza za kupha amʼndende onse, kuti angasambire kupita pa mtunda ndi kuthawa. 43Koma wolamulira asilikali uja anafuna kupulumutsa Paulo ndipo anawaletsa kuchita zimene anakonza. Iye analamulira asilikali kuti amene amatha kusambira kuti adziponye mʼmadzi ndi kuyamba kukafika pa mtunda. 44Otsalawo anayenera kugwira matabwa kapena tizidutswa ta sitimayo. Motero onse anapulumuka nakafika pa mtunda.