Marcos 4 – OL & CCL

O Livro

Marcos 4:1-41

A parábola do semeador

(Mt 13.1-9; Lc 8.4-8)

1Uma vez mais, logo se juntou uma multidão imensa, pelo que entrou num barco e se sentou nele. O barco estava na água, enquanto a multidão ficava à beira-mar, mas em terra.

2E ensinava as pessoas por meio de parábolas. Numa delas, deu-lhes este ensino: 3“Ouçam bem: certo homem foi semear. 4Enquanto semeava, algumas sementes caíram à beira do caminho, vieram as aves e comeram-nas. 5Outras caíram em solo pedregoso com pouca terra; como o solo não tinha profundidade cresceram logo. 6Mas quando o sol rompeu, murcharam; e como não ganharam raízes, acabaram por secar. 7Outras caíram entre espinhos que em pouco tempo sufocaram os rebentos, pelo que não deram grão. 8Outras, porém, outras caíram em bom solo, cresceram, desenvolveram-se e deram trinta, sessenta ou cem vezes mais. 9Quem tem ouvidos, ouça!”

Razão das parábolas

(Mt 13.10-23; Lc 8.9-15)

10E logo que se achou a sós, os que o acompanhavam, juntamente com os doze discípulos, pediram-lhe a explicação das parábolas. 11Ele respondeu-lhes: “É-vos concedido conhecer o mistério do reino de Deus; mas àqueles que estão fora, tudo se expõe por parábolas.

12‘De modo que, ainda que vejam e vejam,

não percebam,

e ainda que ouçam e ouçam, não entendem.

Não estou empenhado em que se arrependam,

nem em perdoá-los.’ ”4.12 Is 6.9-10.

13E acrescenta: “Se não entenderem esta parábola, como compreenderão todas as outras? 14O homem vai semear a palavra. 15As sementes que ficam à beira do caminho são aqueles que receberam a palavra; mal a ouvem, logo vem Satanás tirar-lhes a palavra que neles tinha sido semeada. 16As semeadas em solo pedregoso são os que ouvem a palavra e a recebem com alegria. 17Todavia, não deitam raízes, antes duram pouco; depois, aparecem dificuldades ou perseguições por causa da palavra, e logo essa pessoa se escandaliza. 18As semeadas entre os espinhos são os que ouvem a palavra, 19mas as preocupações desta vida, a ambição da riqueza e os outros desejos surgem e abafam a palavra, pelo que fica sem fruto. 20Mas as sementes plantadas em solo bom são aqueles que ouvem a palavra e a recebem, e produzem uma colheita trinta, sessenta ou até cem vezes maior!”

A luz do candeeiro

(Lc 8.16-18)

21Jesus perguntou-lhes: “Quando alguém acende uma lâmpada, será que a coloca debaixo duma caixa ou da cama? Não a coloca antes num candeeiro?

22Pois nada há oculto que não venha a mostrar-se, nem nada encoberto que não venha a manifestar-se. 23Quem tem ouvidos, ouça! 24Cuidado com o que ouvem! A medida que usarem para medir será usada também para vos medir e ainda vos será aumentada. 25Quem tiver receberá; mas a quem não tem até o que tiver lhe será tirado.

A parábola da semente

26Vou explicar-vos de outra maneira o reino de Deus: Um lavrador semeou o seu campo e foi embora. 27Com o passar dos dias, as sementes foram crescendo sem a sua ajuda, 28pois era a terra que fazia as sementes crescerem. Primeiro, apareceu uma folha, mais tarde, formaram-se as espigas de trigo, até que por fim o grão amadureceu. 29O lavrador veio logo com a foice e tratou de colhê-lo.

A semente de mostarda

(Mt 13.31-32; Lc 13.18-19)

30A que compararei o reino de Deus? Que parábola contarei para o explicar? 31É como uma semente de mostarda; ao ser plantada na terra, embora seja a menor de todas as sementes que existem, 32cresce e transforma-se na maior de todas as plantas, e dá grandes ramos, em cuja sombra as aves do céu podem fazer os seus ninhos.”

33Por meio de muitas parábolas como esta anunciava a palavra ao povo, até onde este podia entendê-la. 34Aliás, nunca o fazia sem lhes contar uma parábola; mas quando estava a sós com os discípulos, explicava-lhes o que queria dizer.

Jesus acalma a tempestade

(Mt 8.18, 23-27; Lc 8.22-25)

35Ao cair da tarde desse dia, Jesus disse aos discípulos: “Vamos atravessar para a outra margem do lago.” 36Deixando a multidão para trás, entraram no barco onde ele já estava e começaram a travessia, embora outros barcos os seguissem. 37Mas logo se levantou um tão grande temporal, com vendaval e ondas rebentando contra o barco, que este já estava cheio de água.

38Entretanto, Jesus dormia deitado na popa, com a cabeça numa almofada. Inquietos, acordaram-no, gritando: “Mestre, não te preocupa que estejamos quase a morrer?” 39Ele, levantando-se, repreendeu o vento e disse ao mar: “Aquieta-te!” O vento parou e fez-se uma grande calma. 40E disse-lhes: “Porque estavam com tanto medo? Ainda não têm fé?”

41E tomados de grande espanto, perguntavam uns aos outros: “Mas quem é este, a quem o próprio vento e o mar obedecem?”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 4:1-41

Fanizo la Wofesa Mbewu

1Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi. 2Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati: 3“Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. 4Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. 5Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. 6Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. 7Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. 8Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”

9Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”

10Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo. 11Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo: 12kotero kuti,

“ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu,

kumva mudzamva koma osamvetsetsa,

kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”

13Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse? 14Wofesa amafesa mawu. 15Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo. 16Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. 17Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira. 18Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; 19koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. 20Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”

Fanizo la Nyale

21Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake? 22Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera. 23Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”

24Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri. 25Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”

Fanizo la Mbewu Imene Ikukula

26Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. 27Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira. 28Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo. 29Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”

Fanizo la Mbewu ya Mpiru

30Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? 31Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. 32Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”

33Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa. 34Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.

Yesu Aletsa Namondwe

35Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.” 36Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. 37Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. 38Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”

39Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.

40Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”

41Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”