2 Samuel 13 – OL & CCL

O Livro

2 Samuel 13:1-39

Amnom e Tamar

1O príncipe Absalão, filho de David, tinha uma irmã muito bonita chamada Tamar. E o príncipe Amnom, que era meio-irmão dela, apaixonou-se perdidamente pela rapariga. 2Amnom estava tão enamorado que ficou doente. E não tinha maneira de lhe falar, pois os rapazes e as meninas eram mantidos separados.

3Amnom tinha um amigo muito esperto, o seu primo Jonadabe, filho de um irmão de David chamado Simeia. 4Um dia, Jonadabe perguntou a Amnom: “O que é que se passa contigo? Porque é que o filho de um rei há de andar definhando de dia para dia?” Respondeu-lhe: “Estou apaixonado por Tamar, minha meia-irmã.”

5“Pois bem, vou dizer-te o que hás de fazer. Vai para a cama e finge que estás muito doente. Quando o teu pai vier ver-te, pede-lhe que Tamar venha preparar-te alguma comida; diz-lhe que te sentirás melhor se ela te vier trazer o alimento.”

6Amnom assim fez. Quando o rei veio vê-lo, Amnom pediu-lhe, por favor, que a sua irmã Tamar fosse autorizada a preparar-lhe algum alimento para ele comer. 7David concordou e mandou dizer a Tamar que fosse aos aposentos de Amnom preparar-lhe alguma coisa para comer.

8Ela obedeceu e foi ao quarto dele; começou a amassar farinha e preparou-lhe um bolo especial. 9Mas quando lho levou ele recusou comer: “Quero que toda a gente saia daqui”, disse aos criados. E as pessoas saíram todas. 10Depois disse a Tamar: “Traz-me tu a comida aqui à cama e então hei de comer.” A moça assim fez. 11Quando ela estava ali em frente dele, prendeu-a e pediu-lhe: “Vem, deita-te aqui comigo, minha irmã.”

12“Oh! Não, meu irmão!”, gritou ela. “Não faças uma loucura dessas. Não me forces! Sabes bem o crime tremendo que isso seria em Israel. 13Eu nem saberia onde esconder-me de vergonha! Tu serias considerado o maior louco da nação! Por favor, fala ao rei no assunto e ele certamente deixará que me case contigo.”

14Ele não quis ouvi-la e, como tinha mais força, violentou-a. 15Logo a seguir a sua paixão tornou-se ódio e acabou por odiá-la ainda mais do que a tinha amado. “Sai daqui!”, rosnou ele.

16“Não! Rejeitares-me agora seria um crime ainda maior do que aquilo que me fizeste.” Mas ele não lhe deu ouvidos. 17Chamou por um criado e ordenou-lhe: “Tira esta rapariga daqui e fecha a porta atrás dela.”

18Assim a expulsou. Ela trazia vestida uma túnica até aos pés, às cores e com mangas, segundo o traje das princesas ainda virgens, naqueles dias. 19Então rasgou a túnica, colocou cinza sobre si, cruzou as mãos na cabeça e foi andando e chorando.

20Seu irmão Absalão veio ter com ela: “Então sempre é verdade que Amnom esteve contigo! Não te angusties, visto que tudo se passou em família. Não é caso para ficares assim!” E Tamar foi morar com o seu irmão Absalão como uma mulher solitária.

21Ao ouvir o que acontecera, o rei David ficou extremamente irado. 22Absalão não disse nada a Amnom, porque lhe tinha um ódio profundo pelo que fizera à irmã.

Absalão mata Amnom

23Dois anos mais tarde, quando as ovelhas de Absalão estavam a ser tosquiadas em Baal-Hazor em Efraim, Absalão convidou o pai e todos os irmãos para um banquete, a fim de festejarem a ocasião. 24Foi ter com o rei e disse-lhe: “Chegou o tempo da tosquia do meu rebanho. Peço que o rei e os seus oficiais venham à festa deste seu servo.”

25O rei respondeu-lhe: “Não, meu rapaz. Se fôssemos todos, seria um encargo enorme para ti.” Absalão insistiu, mas David não aceitou e mandou-lhe felicitações.

26“Bom”, disse Absalão, “já que não vens, manda em teu lugar o meu irmão Amnom.” O rei perguntou: “Porquê Amnom?”

27Absalão insistiu muito, até que o rei concordou e permitiu que todos os filhos lá fossem, incluindo Amnom. Absalão preparou um grande banquete como se fosse um rei.13.27 Absalão preparou um grande banquete como se fosse um rei. Esta frase aparece na tradução grega (LXX) e na versão 4QSam, encontrada em Qumran.

28Absalão avisou os seus homens: “Esperem até que Amnom esteja embriagado e quando eu der o sinal matem-no! Não tenham receio. Aqui sou eu quem dá as ordens e é isto que estou a ordenar-vos. Vamos em frente e nada de ter medo!” 29Foi dessa maneira que mataram Amnom. Os outros príncipes, seus irmãos, montaram nas suas mulas e fugiram.

30Vinham ainda a caminho de Jerusalém, quando chegou aos ouvidos de David o seguinte rumor: “Absalão matou todos os irmãos; nem um ficou em vida!” 31O rei levantou-se, rasgou a roupa que tinha vestida e prostrou-se no chão. Os seus conselheiros rasgaram igualmente as roupas em sinal de amargura.

32Nessa altura, chegou Jonadabe, sobrinho de David, filho de Simeia, que explicou: “Não morreram todos! Só Amnom foi morto! Absalão tinha isto preparado desde que Tamar fora violentada por Amnom. 33Os teus filhos não foram todos mortos! Só foi Amnom.”

34Entretanto, Absalão fugiu. O guarda que estava de vigia na muralha de Jerusalém deu o aviso de que via gente a chegar, na direção da cidade, ao longo da estrada que corre junto da colina.

35“Pronto”, disse Jonadabe ao rei. “Aqui estão eles. Os teus filhos estão a chegar, tal como te disse.” 36Em breve os outros apareceram, a chorar e a lamentarem-se. O rei e os conselheiros também choraram com eles.

37-39Absalão fugiu para junto do rei Talmai de Gesur, filho de Amiude, e ali ficou durante três anos. Entretanto, David já conformado com a morte de Amnom, andava cheio de saudades do seu filho Absalão.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 13:1-39

Amnoni ndi Tamara

1Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola.

2Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye.

3Koma Amnoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu mwana wamwamuna wa Simea, mʼbale wake wa Davide. Yonadabu anali munthu wochenjera kwambiri. 4Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?”

Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.”

5Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.”

6Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.”

7Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.” 8Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo. 9Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana.

Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka. 10Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake. 11Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.”

12Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere. 13Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.” 14Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira.

15Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!”

16Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.”

Koma anakana kumumvera. 17Amnoni anayitana wantchito wake ndipo anati, “Mutulutse mkazi uyu muno ndipo utseke chitseko akatuluka.” 18Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala. 19Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita.

20Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa.

21Mfumu Davide itamva zimenezi, inakwiya kwambiri. 22Abisalomu sananene mawu aliwonse kwa Amnoni; abwino kapena oyipa. Iye anamuda Amunoniyo chifukwa anachititsa manyazi mlongo wake Tamara.

Abisalomu Apha Amnoni

23Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko. 24Abisalomu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Ometa nkhosa za mtumiki wanu anabwera. Chonde mfumu ndi akuluakulu anu mubwere kudzakhala nane?”

25Mfumu inayankha kuti, “Ayi mwana wanga, tisapite tonsefe. Tidzakhala cholemetsa kwa iwe.” Ngakhale Abisalomu anayesetsa kuwumiriza mfumuyo, inakana kupita. Mʼmalo mwake inangomudalitsa Abisalomuyo.

26Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.”

Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?” 27Koma Abisalomu anamuwumiriza, kotero analola kuti Amnoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye.

28Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.” 29Kotero antchito a Abisalomu anachita kwa Amnoni zimene Abisalomu anawalamula. Kenaka ana onse a mfumu anayimirira ndipo anakwera pa abulu awo nathawa.

30Ali mʼnjira, Davide anamva mphekesera yakuti, “Abisalomu wakantha ana onse a mfumu ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala.” 31Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo.

32Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara. 33Mbuye wanga mfumu musavutike ndi maganizo ndi nkhani yoti ana onse a mfumu afa. Wafa ndi Amnoni yekha.”

34Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa.

Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.”

35Yehonadabu anati kwa mfumu, “Taonani ana a mfumu afika. Zachitika monga momwe mtumiki wanu ananenera.”

36Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa.

37Abisalomu anathawa, napita kwa Talimai mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Koma mfumu Davide inalira mwana wake tsiku ndi tsiku.

38Abisalomu atathawa ndi kupita ku Gesuri, anakhala kumeneko zaka zitatu. 39Ndipo Davide anagwidwa ndi chifundo chofuna kumulondola Abisalomu pakuti anali atatonthozedwa pa imfa ya Amnoni.