Êxodo 36 – OL & CCL

O Livro

Êxodo 36:1-38

1Todos os outros artistas, com capacidades dadas pelo Senhor, deverão prestar assistência a Bezalel e a Aoliabe na construção e no mobiliário do tabernáculo.”

2Moisés chamou Bezalel, Aoliabe e todos os homens capazes, que o Senhor dotou de sabedoria e que se tinham oferecido voluntariamente para ajudar neste trabalho, e mandou que começassem. 3Moisés entregou-lhes o material oferecido pelo povo, mas este ainda trazia em cada manhã mais ofertas voluntárias. 4Por fim, todos os que trabalhavam naquela tarefa vieram ter com Moisés 5e disseram-lhe: “Já temos muito mais do que é necessário para esta obra!” 6Moisés então enviou uma mensagem, através do campo, anunciando que não eram precisas mais ofertas. E o povo teve mesmo de ser impedido de trazer mais coisas, 7porque aquilo que eles já tinham era mais do que suficiente para realizar todo o serviço.

O tabernáculo

(Êx 26.1-37)

8Os artistas tecelãos fizeram primeiramente dez véus de linho fino retorcido, em azul, púrpura e vermelho, com querubins habilmente bordados. 9O comprimento de cada véu era de 14 metros e de largura, 2 metros. Eram todos da mesma medida. 10Cinco destes véus eram ligados entre si, lado a lado, e outros cinco também da mesma maneira, de forma a fazerem duas peças retangulares. 11-12Cinquenta laços azuis foram cosidos na bainha de cada uma dessas duas longas peças. 13Depois fizeram-se cinquenta colchetes de ouro para prender os laços, atando assim as duas peças de maneira a formarem um todo único.

14Por cima desse teto havia uma segunda coberta feita de onze mantas de pelo de cabra, 15cada uma delas uniformemente com 15 metros de comprimento por 2 de largura. 16Bezalel juntou cinco destas cobertas, formando uma peça retangular, e as outras seis também as uniu da mesma forma. 17Depois fez cinquenta laços na bainha dum dos lados de cada uma dessas peças, 18assim como cinquenta pequenos colchetes de bronze para poder atar os laços uns aos outros, a fim de que as duas peças ficassem bem unidas. 19A última camada deste telhado era feita de pele de carneiro tingida de vermelho e ainda de pele de couro fino.

20Para os lados do tabernáculo empregou tábuas de madeira de acácia, postas ao alto. 21A altura de cada tábua era de 5 metros, e a largura de 75 centímetros. 22Cada tábua tinha uma ranhura para poder encaixar na seguinte. 23Havia vinte tábuas do lado sul, 24com as extremidades enfiando, ao todo, em quarenta bases de prata. Cada tábua estava fixada à base por duas braçadeiras. 25Havia também vinte tábuas do lado norte do tabernáculo, 26com quarenta bases de prata, duas sob cada tábua. 27O lado ocidental, que era a parte de trás, tinha seis tábuas, 28-29mais uma para cada canto. Estas tábuas, incluindo as dos cantos, ligavam-se umas às outras em ambas as extremidades por meio de argolas. 30Assim, no lado ocidental, havia oito tábuas nos cantos da construção, com dezasseis bases de prata; duas bases para cada tábua.

31Depois fez cinco conjuntos de barras de madeira de acácia para prender as tábuas entre si; cinco barras para cada lado do tabernáculo. 32Cinco traves para cada lado do tabernáculo, mais cinco para a retaguarda, do lado do ocidente. 33A barra do meio, que ficará a meia altura das tábuas, atravessá-las-á de uma ponta à outra. 34Tanto as tábuas como as barras foram cobertas de ouro, mas as argolas eram de ouro puro.

35O véu interior, de azul, púrpura e vermelho, foi feito de linho, com querubins artisticamente bordados. 36Depois foi atado a quatro ganchos postos em quatro colunas de madeira de acácia, cobertas de ouro e assentes em quatro bases de prata.

37Seguidamente, fez o véu para a entrada da tenda sagrada, de linho fino retorcido, bordado a azul, púrpura e vermelho. 38Este véu estava suspenso por cinco postes ou colunas. Estes postes, os seus capitéis e hastes foram revestidos de ouro. As suas cinco bases foram moldadas em bronze.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 36:1-38

1Choncho Bezaleli, Oholiabu pamodzi ndi anthu aluso onse amene Yehova anawapatsa luso ndi nzeru zodziwira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Yehova analamulira.”

2Ndipo Mose anayitana Bezaleli ndi Oholiabu ndiponso munthu aliyense waluso amene Yehova anamupatsa luso ndiponso amene anali ndi mtima wofuna kugwira ntchito. 3Iwo analandira kuchokera kwa Mose zopereka zonse Aisraeli anabweretsa kuti agwirire ntchito yomanga malo wopatulika. Ndipo anthu anapitirira kupereka zopereka zaufulu mmawa uliwonse. 4Kotero amisiri onse amene amagwira ntchito yonse ya malo wopatulika anasiya ntchitoyo 5ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.”

6Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, 7chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse.

Chihema

8Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi. 9Nsalu zonse zinali zofanana. Mulitali mwake zinali mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. 10Iwo analumikiza nsalu zisanu, kuti ikhale nsalu imodzi ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. 11Kenaka anapanga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. 12Iwo anasokerera zokolowekamo makumi asanu pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Anapanga kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. 13Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi.

14Iwo anapanga nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zinalipo khumi ndi imodzi. 15Nsalu zonse khumi ndi imodzi zinali zofanana. Mulitali mwake munali mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake munali mamita awiri. 16Iwo analumikiza nsalu zisanu kukhala nsalu imodzi ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, analumikizanso kukhala nsalu imodzinso. 17Kenaka anasokerera zokolowekamo makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija ndiponso anapanga zokolowekamo zina makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. 18Iwo anapanga ngowe 50 zamkuwa zolowetsa mu zokolowekazo ndipo anaphatikiza nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. 19Ndipo anapanga chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake anapanganso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.

20Iwo anapanga maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. 21Feremu iliyonse inali yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake munali masentimita 69. 22Thabwa lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri. Iwo anapanga maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. 23Anapanga maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho, 24ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. 25Iwo anapanganso maferemu makumi awiri a mbali yakumpoto ya chihemacho, 26ndiponso matsinde makumi anayi asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. 27Anapanganso maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo, 28ndiponso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. 29Pa ngodya ziwirizi panali maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba atalumikizidwa pa ngowe imodzi. Maferemu onse anali ofanana. 30Choncho panali maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri anali pansi pa feremu iliyonse.

31Iwo anapanganso mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha. Mitanda isanu inali ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, 32mitanda isanu inanso inali ya maferemu a mbali inayo ndipo mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. 33Anapanga mtanda wapakati omwe umachokera pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. 34Iwo anakuta maferemuwo ndi golide ndiponso anapanga mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso anayikuta ndi golide.

35Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi. 36Iwo anapanga nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide. Anapanganso ngowe zagolide za nsanamirazo ndi matsinde asiliva anayi. 37Anapanga nsalu ya pa chipata cholowera mu chihema, yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira yomwe inali yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. 38Anapanga nsanamira zisanu ndi ngowe zake. Anakuta pamwamba pa nsanamirazo ndi zomangira zake ndi golide, ndipo anapanganso matsinde asanu amkuwa.