Књига пророка Исаије 43 – NSP & CCL

New Serbian Translation

Књига пророка Исаије 43:1-28

Ослобођење јеврејског народа

1Сада говори Господ,

који те је створио, Јакове,

који те је начинио, Израиљу:

„Не бој се, јер ја сам те откупио,

по имену те позвао: ти си мој.

2Кад преко воде прелазиш,

ја сам с тобом;

преко река,

неће те преплавити.

Прођеш ли кроз ватру,

нећеш изгорети,

и пламен те опалити неће,

3јер ја сам Господ, Бог твој,

Израиљев Светитељ, твој Спаситељ.

Да тебе откупим, дајем Египат;

уместо тебе дајем Куш и Севу.

4Јер ти си драгоцен у мојим очима,

цењен си и ја те волим.

Зато и дајем човека уместо тебе,

и народе трампим за живот твој.

5Не бој се, јер ја сам с тобом.

Са истока ћу потомство твоје довести,

и са запада ћу те сакупити.

6Рећи ћу северу: ’Дај ми!’

и југу: ’Не задржавај га!’

Синове моје доведи издалека,

и ћерке моје с краја земље,

7сваког ко се именом мојим зове,

и кога сам на славу своју створио,

замислио га, па га начинио.

Господ је једини Бог

8Изведи народ слеп, премда има очи,

и глув, премда има уши.

9Нека се заједно саберу сва племена,

и нека се сакупе народи.

Је ли ко од њих ово најавио,

и од давнина нам предсказао?

Нек доведу своје сведоке и оправдају се.

Нека се чује, па нек кажу: ’Истина је!’

10Ви сте сведоци моји – говори Господ –

и слуге моје које сам изабрао,

да бисте знали и мени веровали,

и схватили да сам то ја.

Пре мене ниједан бог саздан не би,

а неће ни после мене бити.

11Ја, ја сам Господ,

осим мене спаситеља нема.

12Ја сам најавио и спасао и предсказао,

и међу вама туђинаца нема!

А ви сте сведоци моји – говори Господ –

и ја сам Бог.

13Од вечности ја то јесам,

и нико из моје руке избавити неће.

Учинићу, а ко ће изменити?“

Бог ће уништити Вавилон

14Говори Господ,

ваш Откупитељ, Израиљев Светитељ:

„Вас ради послао сам према Вавилону,

и оборићу бегунце, све њих;

а Халдејци ће клицати у лађама.

15Ја сам Господ, ваш Светитељ,

Израиљев створитељ, ваш цар!“

Нови излазак

16Говори Господ,

који начини пут по мору,

и по водама силним пролаз,

17који је извео бојна кола и коње,

војску и јунаке заједно,

и они падоше да више не устану,

згаснуше, као фитиљ утрнуше:

18„Не спомињите оно што је давнашње,

не мислите на оно што је застарело.

19Ево, чиним нешто ново;

већ настаје, зар не опажате?

Да, направићу пут у пустињи,

и реке у пустоши.

20Славиће ме звери пољске,

шакали и нојеви млади,

јер сам дао воду у пустињи,

реке у пустари,

да напојим свој народ,

изабраника својега.

21Овај народ што сам га себи саздао,

казиваће мени похвалу.

Незахвалност Божијег народа

22Али ти мене ниси призивао, Јакове;

досадио сам ти, Израиљу!

23Ниси ми приносио овцу на свеспалницу,

ниси ме прослављао приносећи жртве;

а ја те нисам терао да приносиш приносе,

нити сам ти досађивао да ми кадиш;

24ниси ми за новац куповао мирисни штапић;

ниси ме ситио салом својих жртава;

него си ме оптерећивао својим гресима,

досађивао си ми својом кривицом.

25А ја, ја сам тај,

себе ради бришем твоје преступе,

и не спомињем твоје грехе.

26Подсети ме,

спорићемо се заједно,

сабери се да се оправдаш.

27Прво је сагрешио отац твој,

а од мене су се одметнули посредници твоји.

28И ја ћу оскрнавити главаре Светилишта,

те Јакова изручити проклетству,

а Израиља порузи.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 43:1-28

Yehova Yekha Mpulumutsi wa Israeli

1Koma tsopano, Yehova

amene anakulenga, iwe Yakobo,

amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,

“Usaope, pakuti ndakuwombola;

Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.

2Pamene ukuwoloka nyanja,

ndidzakhala nawe;

ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,

sidzakukokolola.

Pamene ukudutsa pa moto,

sudzapsa;

lawi la moto silidzakutentha.

3Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,

Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.

Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,

ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.

4Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,

ndipo chifukwa ndimakukonda,

ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,

ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.

5Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;

ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,

ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.

6Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’

ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’

Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali,

ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;

7onsewo amadziwika ndi dzina langa;

ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga,

ndinawawumba, inde ndinawapanga.”

8Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya,

anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.

9Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi,

anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu.

Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi?

Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale?

Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona,

kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”

10Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga,

ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha,

kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha.

Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina,

ngakhale pambuyo panga

sipadzakhalaponso wina.”

11Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova,

ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.

12Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa;

ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu.

Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.

13“Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse.

Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga,

ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”

Chifundo cha Mulungu ndi Kusakhulupirika kwa Israeli

14Yehova akuti,

Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti,

“Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni

ndi kukupulumutsani.

Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.

15Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja,

Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”

16Yehova

anapanga njira pa nyanja,

anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.

17Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo,

gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu,

ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso

anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,

18“Iwalani zinthu zakale;

ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.

19Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano!

Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona?

Ine ndikulambula msewu mʼchipululu

ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.

20Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi

zinandilemekeza.

Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma

kuti ndiwapatse madzi anthu anga

osankhidwa.

21Anthu amene ndinadziwumbira ndekha

kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.

22“Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo,

munatopa nane, Inu Aisraeli.

23Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza,

kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu.

Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya

kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.

24Simunandigulire bango lonunkhira

kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu.

Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu

ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.

25“Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza

zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini,

ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.

26Mundikumbutse zakale,

ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi;

fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.

27Kholo lanu loyamba linachimwa;

ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.

28Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero,

ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe

ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”