Tito 1 – NVI & CCL

Nueva Versión Internacional

Tito 1:1-16

1Pablo, siervo de Dios y apóstol de Jesucristo, llamado para que, mediante la fe, los elegidos de Dios lleguen a conocer la verdad que conduce a la devoción. 2Nuestra esperanza es la vida eterna, la cual Dios, que no miente, ya había prometido antes del comienzo del tiempo. 3Ahora, a su debido tiempo, él ha cumplido esta promesa mediante la predicación que se me ha confiado por orden de Dios nuestro Salvador.

4A Tito, mi verdadero hijo en esta fe que compartimos:

Que Dios el Padre y Cristo Jesús nuestro Salvador te concedan gracia y paz.

Tarea de Tito en Creta

5Te dejé en Creta para que pusieras en orden lo que quedaba por hacer y en cada pueblo nombraras1:5 nombraras. Alt. ordenaras. líderes de la iglesia, de acuerdo con las instrucciones que te di. 6El líder debe ser irreprensible, esposo de una sola mujer; sus hijos deben ser creyentes,1:6 creyentes. Alt. fieles. libres de sospecha de libertinaje o de desobediencia. 7El obispo tiene a su cargo la obra de Dios y por lo tanto, debe ser irreprensible: no arrogante, ni iracundo, ni borracho, ni violento, ni codicioso de ganancias mal habidas. 8Al contrario, debe ser hospitalario, amigo del bien, sensato, justo, santo y disciplinado. 9Debe apegarse a la palabra fiel, según la enseñanza que recibió, de modo que también pueda exhortar a otros con la sana doctrina y refutar a los que se opongan.

10Y es que hay muchos rebeldes, charlatanes y engañadores, especialmente los partidarios de la circuncisión. 11A esos hay que taparles la boca, ya que están arruinando familias enteras al enseñar lo que no se debe y lo hacen para obtener ganancias mal habidas. 12Fue precisamente uno de sus propios profetas el que dijo: «Los cretenses son siempre mentirosos, malas bestias, glotones perezosos». 13Y es la verdad. Por eso, repréndelos con severidad a fin de que sean sanos en la fe 14y no hagan caso de mitos judíos ni de lo que exigen esos que rechazan la verdad. 15Para los puros todo es puro, pero para los corruptos e incrédulos no hay nada puro. Al contrario, tienen corrompidas la mente y la conciencia. 16Profesan conocer a Dios, pero con sus acciones lo niegan; son abominables, desobedientes e incapaces de hacer algo bueno.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tito 1:1-16

1Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu 2ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe. 3Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu.

4Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse:

Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.

Ntchito ya Tito ku Krete

5Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira. 6Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera. 7Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo. 8Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo. 9Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.

Kudzudzula Olephera Kuchita Bwino

10Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. 11Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo. 12Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.” 13Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona, 14kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi. 15Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa. 16Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.