New International Version

Titus 3:1-15

Saved in Order to Do Good

1Remind the people to be subject to rulers and authorities, to be obedient, to be ready to do whatever is good, 2to slander no one, to be peaceable and considerate, and always to be gentle toward everyone.

3At one time we too were foolish, disobedient, deceived and enslaved by all kinds of passions and pleasures. We lived in malice and envy, being hated and hating one another. 4But when the kindness and love of God our Savior appeared, 5he saved us, not because of righteous things we had done, but because of his mercy. He saved us through the washing of rebirth and renewal by the Holy Spirit, 6whom he poured out on us generously through Jesus Christ our Savior, 7so that, having been justified by his grace, we might become heirs having the hope of eternal life. 8This is a trustworthy saying. And I want you to stress these things, so that those who have trusted in God may be careful to devote themselves to doing what is good. These things are excellent and profitable for everyone.

9But avoid foolish controversies and genealogies and arguments and quarrels about the law, because these are unprofitable and useless. 10Warn a divisive person once, and then warn them a second time. After that, have nothing to do with them. 11You may be sure that such people are warped and sinful; they are self-condemned.

Final Remarks

12As soon as I send Artemas or Tychicus to you, do your best to come to me at Nicopolis, because I have decided to winter there. 13Do everything you can to help Zenas the lawyer and Apollos on their way and see that they have everything they need. 14Our people must learn to devote themselves to doing what is good, in order to provide for urgent needs and not live unproductive lives.

15Everyone with me sends you greetings. Greet those who love us in the faith.

Grace be with you all.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tito 3:1-15

Kuchita Ntchito Zabwino

1Uwakumbutse anthu kuti azigonjera oweruza ndi olamulira, aziwamvera ndi kukhala okonzeka kuchita chilichonse chabwino. 2Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.

3Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake. 4Koma kukoma mtima ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chitaonekera, 5Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera 6amene anatipatsa mowolowamanja kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu, 7kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. 8Mawuwa ndi okhulupirika ndipo ine ndikufuna kuti iwe utsindike zinthu izi, kuti amene akhulupirira Mulungu adzipereke kuchita ntchito zabwino. Zinthu izi ndi zabwino kwambiri ndi zopindulitsa kwa aliyense.

9Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kuwerengawerenga mndandanda wa mibado ya makolo, mikangano ndi mitsutso pa za Malamulo, chifukwa zimenezi ndi zosapindulitsa ndi zopanda pake. 10Munthu woyambitsa mipatuko umuchenjeze koyamba, ndiponso umuchenjeze kachiwiri. Kenaka umupewe. 11Iwe udziwe kuti munthu wotero ngosokoneza ndi wochimwa, ndipo akudzitsutsa yekha.

Mawu Otsiriza

12Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira. 13Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu. 14Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.

15Onse amene ali ndi ine akupereka moni. Upereke moni kwa amene amatikonda ife mʼchikhulupiriro.

Chisomo chikhale ndi inu nonse.