Proverbs 12 – NIV & CCL

New International Version

Proverbs 12:1-28

1Whoever loves discipline loves knowledge,

but whoever hates correction is stupid.

2Good people obtain favor from the Lord,

but he condemns those who devise wicked schemes.

3No one can be established through wickedness,

but the righteous cannot be uprooted.

4A wife of noble character is her husband’s crown,

but a disgraceful wife is like decay in his bones.

5The plans of the righteous are just,

but the advice of the wicked is deceitful.

6The words of the wicked lie in wait for blood,

but the speech of the upright rescues them.

7The wicked are overthrown and are no more,

but the house of the righteous stands firm.

8A person is praised according to their prudence,

and one with a warped mind is despised.

9Better to be a nobody and yet have a servant

than pretend to be somebody and have no food.

10The righteous care for the needs of their animals,

but the kindest acts of the wicked are cruel.

11Those who work their land will have abundant food,

but those who chase fantasies have no sense.

12The wicked desire the stronghold of evildoers,

but the root of the righteous endures.

13Evildoers are trapped by their sinful talk,

and so the innocent escape trouble.

14From the fruit of their lips people are filled with good things,

and the work of their hands brings them reward.

15The way of fools seems right to them,

but the wise listen to advice.

16Fools show their annoyance at once,

but the prudent overlook an insult.

17An honest witness tells the truth,

but a false witness tells lies.

18The words of the reckless pierce like swords,

but the tongue of the wise brings healing.

19Truthful lips endure forever,

but a lying tongue lasts only a moment.

20Deceit is in the hearts of those who plot evil,

but those who promote peace have joy.

21No harm overtakes the righteous,

but the wicked have their fill of trouble.

22The Lord detests lying lips,

but he delights in people who are trustworthy.

23The prudent keep their knowledge to themselves,

but a fool’s heart blurts out folly.

24Diligent hands will rule,

but laziness ends in forced labor.

25Anxiety weighs down the heart,

but a kind word cheers it up.

26The righteous choose their friends carefully,

but the way of the wicked leads them astray.

27The lazy do not roast12:27 The meaning of the Hebrew for this word is uncertain. any game,

but the diligent feed on the riches of the hunt.

28In the way of righteousness there is life;

along that path is immortality.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 12:1-28

1Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu,

koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.

2Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova,

koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.

3Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa,

koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.

4Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake,

koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.

5Maganizo a anthu olungama ndi owongoka,

koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.

6Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa,

koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.

7Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika,

koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.

8Munthu amatamandidwa malinga ndi nzeru zake,

koma anthu amitima yokhota amanyozedwa.

9Nʼkwabwino kukhala munthu wonyozeka koma wodzigwirira ntchito nʼkukhala ndi zonse zofunika,

kuposa kukhala wodzikuza koma ulibe ndi chakudya chomwe.

10Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake,

koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.

11Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka,

koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.

12Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa,

koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.

13Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa;

koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.

14Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake

ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.

15Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino,

koma munthu wanzeru amamvera malangizo.

16Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo,

koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.

17Woyankhula zoona amapereka umboni woona,

koma mboni yabodza imafotokoza zonama.

18Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga,

koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.

19Mawu woona amakhala mpaka muyaya

koma mawu abodza sakhalitsa.

20Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo;

koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.

21Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama,

koma munthu woyipa mavuto samuthera.

22Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova,

koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.

23Munthu wochenjera amabisa nzeru zake,

koma munthu wopusa amaonetsa uchitsiru wake poyera.

24Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira,

koma aulesi adzakhala ngati kapolo.

25Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu,

koma mawu abwino amamusangalatsa.

26Munthu wolungama amatsogolera mnansi wake,

koma ntchito za anthu oyipa zimawasocheretsa.

27Munthu waulesi sapeza chimene akufuna,

koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengo wapatali.

28Mʼnjira yachilungamo muli moyo;

koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.