Matthew 28 – NIV & CCL

New International Version

Matthew 28:1-20

Jesus Has Risen

1After the Sabbath, at dawn on the first day of the week, Mary Magdalene and the other Mary went to look at the tomb.

2There was a violent earthquake, for an angel of the Lord came down from heaven and, going to the tomb, rolled back the stone and sat on it. 3His appearance was like lightning, and his clothes were white as snow. 4The guards were so afraid of him that they shook and became like dead men.

5The angel said to the women, “Do not be afraid, for I know that you are looking for Jesus, who was crucified. 6He is not here; he has risen, just as he said. Come and see the place where he lay. 7Then go quickly and tell his disciples: ‘He has risen from the dead and is going ahead of you into Galilee. There you will see him.’ Now I have told you.”

8So the women hurried away from the tomb, afraid yet filled with joy, and ran to tell his disciples. 9Suddenly Jesus met them. “Greetings,” he said. They came to him, clasped his feet and worshiped him. 10Then Jesus said to them, “Do not be afraid. Go and tell my brothers to go to Galilee; there they will see me.”

The Guards’ Report

11While the women were on their way, some of the guards went into the city and reported to the chief priests everything that had happened. 12When the chief priests had met with the elders and devised a plan, they gave the soldiers a large sum of money, 13telling them, “You are to say, ‘His disciples came during the night and stole him away while we were asleep.’ 14If this report gets to the governor, we will satisfy him and keep you out of trouble.” 15So the soldiers took the money and did as they were instructed. And this story has been widely circulated among the Jews to this very day.

The Great Commission

16Then the eleven disciples went to Galilee, to the mountain where Jesus had told them to go. 17When they saw him, they worshiped him; but some doubted. 18Then Jesus came to them and said, “All authority in heaven and on earth has been given to me. 19Therefore go and make disciples of all nations, baptizing them in the name of the Father and of the Son and of the Holy Spirit, 20and teaching them to obey everything I have commanded you. And surely I am with you always, to the very end of the age.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 28:1-20

Yesu Auka kwa Akufa

1Litapita tsiku la Sabata, mmawa wa tsiku loyamba la Sabata, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anapita kukaona manda.

2Kunachitika chivomerezi chachikulu, pakuti mngelo wa Ambuye anabwera kuchokera kumwamba ndipo anapita ku manda, nakagubuduza mwala nawukhalira. 3Maonekedwe ake anali ngati mphenzi ndipo zovala zake zinali mbuu ngati matalala. 4Alondawo anachita naye mantha kwambiri kotero kuti ananjenjemera ndi kuwuma ngati akufa.

5Mngelo anati kwa amayiwo, “Musachite mantha popeza ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa. 6Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona. 7Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.”

8Pamenepo amayiwo anachoka mofulumira ku mandako ali ndi mantha komabe atadzaza ndi chimwemwe, ndipo anathamanga kukawuza ophunzira ake. 9Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nati, “Moni.” Iwo anabwera kwa Iye, nagwira mapazi ake namulambira. 10Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Musachite mantha, pitani kawuzeni abale anga kuti apite ku Galileya ndipo kumeneko akandiona Ine.”

Uthenga wa Alonda

11Amayi aja akupita, ena mwa alonda aja anapita ku mzinda nafotokozera akulu a ansembe zonse zimene zinachitika. 12Akulu a ansembe atakumana ndi akuluakulu anapangana zochita. Anapatsa alonda aja ndalama zambiri, 13nawawuza kuti, “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku ndipo amuba ife tili mtulo.’ 14Ngati nkhani iyi imupeze bwanamkubwa, ife tidzamukhazika mtima pansi ndipo simudzakhala mʼmavuto.” 15Pamenepo alondawo anatenga ndalamazo nachita monga mmene anawuzidwira. Ndipo mbiri iyi inawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino.

Yesu Atuma Ophunzira Ake

16Ndipo ophunzira khumi ndi mmodzi aja anapita ku Galileya, ku phiri limene Yesu anawawuza kuti apite. 17Atamuona Iye, anamulambira; koma ena anakayika. 18Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine. 19Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, 20ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”