2 Timothy 3 – NIV & CCL

New International Version

2 Timothy 3:1-17

1But mark this: There will be terrible times in the last days. 2People will be lovers of themselves, lovers of money, boastful, proud, abusive, disobedient to their parents, ungrateful, unholy, 3without love, unforgiving, slanderous, without self-control, brutal, not lovers of the good, 4treacherous, rash, conceited, lovers of pleasure rather than lovers of God— 5having a form of godliness but denying its power. Have nothing to do with such people.

6They are the kind who worm their way into homes and gain control over gullible women, who are loaded down with sins and are swayed by all kinds of evil desires, 7always learning but never able to come to a knowledge of the truth. 8Just as Jannes and Jambres opposed Moses, so also these teachers oppose the truth. They are men of depraved minds, who, as far as the faith is concerned, are rejected. 9But they will not get very far because, as in the case of those men, their folly will be clear to everyone.

A Final Charge to Timothy

10You, however, know all about my teaching, my way of life, my purpose, faith, patience, love, endurance, 11persecutions, sufferings—what kinds of things happened to me in Antioch, Iconium and Lystra, the persecutions I endured. Yet the Lord rescued me from all of them. 12In fact, everyone who wants to live a godly life in Christ Jesus will be persecuted, 13while evildoers and impostors will go from bad to worse, deceiving and being deceived. 14But as for you, continue in what you have learned and have become convinced of, because you know those from whom you learned it, 15and how from infancy you have known the Holy Scriptures, which are able to make you wise for salvation through faith in Christ Jesus. 16All Scripture is God-breathed and is useful for teaching, rebuking, correcting and training in righteousness, 17so that the servant of God3:17 Or that you, a man of God, may be thoroughly equipped for every good work.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Timoteyo 3:1-17

Zoopsa za Mʼmasiku Otsiriza

1Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri. 2Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. 3Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, 4opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. 5Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.

6Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu, 7amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi. 8Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa. 9Koma sadzapita nazo patali kwambiri zimenezi, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwawo monga anachitira Yanesi ndi Yambere.

Paulo Alimbikitsa Timoteyo

10Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga, 11mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi. 12Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, 13pomwe anthu oyipa ndi onyenga adzanka nayipirayipira, kunamiza ena, iwo nʼkumanamizidwanso. 14Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi. 15Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. 16Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo 17kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.