New International Reader's Version

Leviticus 9

The Priests Offer Sacrifices

1On the eighth day Moses sent for Aaron, his sons and the elders of Israel. He said to Aaron, “Bring a bull calf for your sin offering. Bring a ram for your burnt offering. They must not have any flaws. Offer them to the Lord. Then speak to the Israelites. Tell them, ‘Bring a male goat for a sin offering. Bring a calf and a lamb for a burnt offering. Both of them must be a year old. They must not have any flaws. Bring an ox and a ram for a friendship offering. Sacrifice all of them to the Lord. Also bring a grain offering. Mix it with olive oil. Today the Lord will appear to you.’ ”

The people got the things Moses commanded them to get. They took them to the front of the tent of meeting. The whole community came up close to the tent. They stood there in front of the Lord. Then Moses said, “You have done what the Lord has commanded. So the glory of the Lord will appear to you.”

Moses said to Aaron, “Come to the altar. Sacrifice your sin offering and your burnt offering. Pay for your sin and the sin of the people. Sacrifice the people’s offering. Pay for their sin. Do just as the Lord has commanded.”

So Aaron came to the altar. He killed the calf as a sin offering for himself. His sons brought its blood to him. He dipped his finger into the blood. He put some on the horns that stick out from the upper four corners of the altar. He poured out the rest of the blood at the bottom of the altar. 10 He burned the fat and the kidneys on the altar. He also burned the long part of the liver. All these parts were from the sin offering. Aaron did just as the Lord had commanded Moses. 11 He burned up the meat and the hide outside the camp.

12 Then he killed the animal for the burnt offering. His sons handed him its blood. He splashed it against the sides of the altar. 13 They handed him the burnt offering piece by piece. It included the animal’s head. Aaron burned everything on the altar. 14 He washed the inside parts and the legs. He burned them on top of the burnt offering on the altar.

15 Then Aaron brought the people’s offering. He took the goat for their sin offering and killed it. He offered it for a sin offering. He did just as he had done with his own sin offering.

16 He brought the animal for the burnt offering. He offered it in the way the law requires. 17 He also brought the grain offering. He took a handful of it and burned it on the altar. It was in addition to that morning’s burnt offering.

18 Aaron killed the ox and the ram as the friendship offering for the people. His sons handed him the blood. He splashed it against the sides of the altar. 19 His sons also brought the fat parts of the ox and the ram. They included the fat tail and the layer of fat. They also included the kidneys and the long part of the liver. 20 Aaron’s sons placed everything on the breasts of the animals. Aaron burned the fat on the altar. 21 He lifted up the breasts and the right thigh and waved them in front of the Lord as a wave offering. He did it just as Moses had commanded.

22 Then Aaron lifted up his hands toward the people. He gave them a blessing. He had already sacrificed the sin offering, the burnt offering and the friendship offering. So he stepped down from the altar.

23 Moses and Aaron went into the tent of meeting. When they came out, they gave the people a blessing. The glory of the Lord appeared to all the people. 24 The Lord sent fire on the altar. The fire burned up the burnt offering along with the fat parts. All the people saw it. Then they shouted for joy. They fell with their faces to the ground.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 9

Ansembe Ayamba Kutumikira

1Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Mose anayitana Aaroni, ana ake ndi akuluakulu a Aisraeli. Ndipo anawuza Aaroni kuti, “Tenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yako yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke pamaso pa Yehova. Kenaka uwawuze Aisraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwana wangʼombe ndi mwana wankhosa. Zonsezi zikhale za chaka chimodzi ndi zopanda chilema kuti zikhale nsembe yopsereza. Mutengenso ngʼombe yayimuna ndi nkhosa yayimuna kuti zikhale nsembe yachiyanjano zoti ziperekedwe pamaso pa Yehova. Pamodzi ndi izi mubwerenso ndi nsembe yachakudya yosakaniza ndi mafuta pakuti lero Yehova akuonekerani.’ ”

Anthu anatenga zonse zimene Mose analamula nabwera nazo pa khomo la tenti ya msonkhano. Gululo linasendera pafupi ndi kuyima pamaso pa Yehova. Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.”

Pambuyo pake Mose anawuza Aaroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa ndipo upereka nsembe yako yopepesera machimo ndi nsembe yako yopsereza ndikuchita mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a anthu. Anthuwa apereke nsembe zawo zopepesera machimo monga momwe Yehova walamulira.”

Choncho Aaroni anasendera pafupi ndi guwa, napha mwana wangʼombe uja kukhala nsembe yake yopepesera machimo. Ana a Aaroni anabwera ndi magazi kwa Aaroni ndipo iye anaviyika chala chake mʼmagaziwo, nawapaka pa nyanga za guwa. Magazi wotsalawo anawathira pa tsinde la guwalo. 10 Kenaka anatentha paguwapo, mafuta, impsyo pamodzi ndi mafuta amene amakuta chiwindi ngati nsembe yopepesera machimoyo, monga momwe Yehova analamulira Mose. 11 Koma nyama ndi chikopa anazitenthera kunja kwa msasa.

12 Kenaka anapha nsembe yopsereza. Ana a Aaroni atabwera ndi magazi kwa iye, Aaroniyo anawawaza mbali zonse za guwa. 13 Ana akewo anamupatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza ija pamodzi ndi mutu ndipo anazitentha pa guwa. 14 Aaroni anatsuka matumbo ndi miyendo nazitentha pa guwa pamodzi ndi nsembe yopsereza ija.

15 Kenaka Aaroni anapereka zopereka za anthuwo. Anatenga mbuzi yopepesera machimo a anthuwo, yopereka chifukwa cha tchimo, nayipha ndi kuyipereka kuti ikhale yopepesera machimo monga anachitira ndi nsembe yoyamba ija.

16 Anabwera ndi nsembe yopsereza, nayipereka potsata mwambo wake. 17 Anabweranso ndi chopereka cha chakudya. Anatapa ufa dzanja limodzi ndi kutentha pa guwa, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa ija.

18 Tsono Aaroni anapha ngʼombe ndi nkhosa yayimuna monga nsembe yachiyanjano ya anthu. Ana ake anamupatsira magazi ndipo anawawaza mbali zonse za guwa. 19 Anamupatsiranso mafuta a ngʼombeyo ndi nkhosa yayimunayo: mchira wamafuta, mafuta wokuta matumbo, impsyo ndi mafuta wokuta chiwindi. 20 Ana a Aaroni anayika mafutawo pa zidale. Pambuyo pake Aaroni anatentha mafutawo pa guwa lansembe. 21 Koma zidale ndi ntchafu ya kumanja Aaroni anaziweyula ngati chopereka choweyula pamaso pa Yehova.

22 Kenaka Aaroni anakweza manja ake pa anthuwo nawadalitsa. Ndipo atatha kupereka nsembe yopepesera machimo, nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano, anatsika pa guwapo.

23 Ndipo Mose pamodzi ndi Aaroni analowa mu tenti ya msonkhano. Atatulukamo anadalitsa anthuwo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse. 24 Pomwepo moto unatuluka pamaso pa Yehova niwutentha nsembe zopsereza ndi mafuta zimene zinali pa guwa. Anthu onse ataona zimenezi anafuwula mwachimwemwe ndipo anaweramitsa nkhope zawo pansi.