Exodus 5 – NIRV & CCL

New International Reader’s Version

Exodus 5:1-23

Bricks Without Straw

1Later on, Moses and Aaron went to Pharaoh. They said, “The Lord is the God of Israel. He says, ‘Let my people go. Then they will be able to hold a feast to honor me in the desert.’ ”

2Pharaoh said, “Who is the Lord? Why should I obey him? Why should I let Israel go? I don’t even know the Lord. And I won’t let Israel go.”

3Then Moses and Aaron said, “The God of the Hebrews has met with us. Now let us take a journey that lasts about three days. We want to go into the desert to offer sacrifices to the Lord our God. If we don’t, he might strike us with plagues. Or he might let us be killed by swords.”

4But the king of Egypt said, “Moses and Aaron, why are you taking the people away from their work? Get back to work!” 5Pharaoh continued, “There are large numbers of your people in the land. But you are stopping them from working.”

6That same day Pharaoh gave orders to the slave drivers and the overseers in charge of the people. 7He said, “Don’t give the people any more straw to make bricks. Let them go and get their own straw. 8But require them to make the same number of bricks as before. Don’t lower the number they have to make. They are lazy. That’s why they are crying out, ‘Let us go. We want to offer sacrifices to our God.’ 9Make them work harder. Then they will be too busy to pay attention to lies.”

10The slave drivers and the overseers left. They said to the people, “Pharaoh says, ‘I won’t give you any more straw. 11Go and get your own straw anywhere you can find it. But you still have to make the same number of bricks.’ ” 12So the people scattered all over Egypt. They went to gather any pieces of straw left in the fields. 13Pharaoh’s slave drivers kept making the people work hard. They said, “Finish the work you are required to do each day. Make the same number of bricks you made when you had straw.” 14The slave drivers whipped the Israelite overseers they had appointed. The slave drivers asked, “Why haven’t you made the same number of bricks yesterday or today, just as before?”

15Then the Israelite overseers appealed to Pharaoh. They asked, “Why have you treated us like this? 16You didn’t give us any straw. But you told us, ‘Make bricks!’ We are being whipped. But it’s the fault of your own people.”

17Pharaoh said, “You are lazy! That’s why you keep saying, ‘Let us go. We want to offer sacrifices to the Lord.’ 18Now get to work. We won’t give you any straw. But you still have to make the same number of bricks.”

19The Israelite overseers realized they were in trouble. They knew it when they were told, “Don’t reduce the number of bricks you are required to make each day.” 20When they left Pharaoh, they found Moses and Aaron waiting to meet them. 21They said to Moses and Aaron, “We want the Lord to look at what you have done! We want him to judge you for it! We are like a very bad smell to Pharaoh and his officials. You have given them an excuse to kill us with their swords.”

The Lord Promises to Save the Israelites

22Moses returned to talk to the Lord. He said to him, “Why, Lord? Why have you brought trouble on these people? Is this why you sent me? 23I went to Pharaoh to speak to him in your name. Ever since then, he has brought nothing but trouble on these people. And you haven’t saved your people at all.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 5:1-23

Mose Akumana ndi Farao

1Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”

2Koma Farao anati, “Yehova ndani kuti ine ndimumvere ndi kulola Aisraeli kuti apite? Ine Yehova sindikumudziwa ndipo sindilola kuti Aisraeli apite.”

3Ndipo iwo anati, “Mulungu wa Ahebri anakumana nafe. Chonde tiloleni tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, ngati sititero iye adzatipweteka ndi miliri kapena lupanga.”

4Koma mfumu ya Igupto inati, “Mose ndi Aaroni, chifukwa chiyani mukuchititsa anthuwa kuti asagwire ntchito zawo? Bwererani ku ntchito zanu!” 5Ndiponso Farao anati, “Taonani, anthuwa mʼdziko muno alipo ochuluka, ndipo inu mukuwaletsa kugwira ntchito.”

Njerwa Zopanda Udzu

6Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti 7“Inu musawapatsenso udzu wopangira njerwa monga mumachitira kale, iwo azipita ndi kukatenga udzu wawo. 8Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’ 9Muwakhawulitse ndi ntchito anthu amenewa kuti azitanganidwa, asakhale ndi mpata omvera zabodza.”

10Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu. 11Mʼmalo mwake mupite mukadzimwetere udzu kulikonse kumene mungawupeze. Komabe ntchito yanu sichepetsedwa.’ ” 12Kotero anthuwo anamwazikana mʼdziko lonse la Igupto kukamweta udzu. 13Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.” 14Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?”

15Pamenepo oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja anapita kukadandaula kwa Farao kuti, “Chifukwa chiyani mwachitira antchito anu zotere? 16Antchito anu sakupatsidwa udzu, komabe akutiwuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ Antchito anu akumenyedwa, koma cholakwa sichili ndi anthu anu.”

17Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’ 18Pitani tsopano kuntchito. Simudzapatsidwanso udzu komabe muyenera kuwumba muyeso wanu wovomerezeka wa njerwa.”

19Oyangʼanira anzawo a Chiisraeli anazindikira kuti ali pa mavuto pamene anawuzidwa kuti, “Musachepetse chiwerengero cha njerwa chimene muyenera kuwumba tsiku lililonse.” 20Atachoka pamaso pa Farao, anakumana ndi Mose ndi Aaroni akuwadikira, 21ndipo iwo anati, “Yehova akupenyeni ndi kukuweruzani popeza mwachititsa Farao ndi nduna zake kuti anyansidwe nafe ndipo mwayika lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.”

Mulungu Alonjeza Chipulumutso

22Mose anabwerera kwa Yehova ndipo anati, “Chonde Ambuye, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Kodi munanditumira zimenezi? 23Chipitireni changa kwa Farao kukamuyankhula mʼdzina lanu, iye wakhala akuzunza anthuwa, ndipo inu simunawapulumutse konse anthu anu.”