Exodus 14 – NIRV & CCL

New International Reader’s Version

Exodus 14:1-31

1Then the Lord spoke to Moses. 2He said, “Tell the people of Israel to turn back. Have them camp near Pi Hahiroth between Migdol and the Red Sea. They must camp by the sea, right across from Baal Zephon. 3Pharaoh will think, ‘The Israelites are wandering around the land. They don’t know which way to go. The desert is all around them.’ 4I will make Pharaoh stubborn. He will chase them. But I will gain glory for myself because of what will happen to Pharaoh and his whole army. And the Egyptians will know that I am the Lord.” So the Israelites camped by the Red Sea.

5The king of Egypt was told that the people had escaped. Then Pharaoh and his officials changed their minds about them. They said, “What have we done? We’ve let the people of Israel go! We’ve lost our slaves and all the work they used to do for us!” 6So he had his chariot made ready. He took his army with him. 7He took 600 of the best chariots in Egypt. He also took along all the other chariots. Officers were in charge of all of them. 8The Lord made Pharaoh, the king of Egypt, stubborn. So he chased the Israelites as they were marching out boldly. 9The Egyptians went after the Israelites. All Pharaoh’s horses and chariots and horsemen and troops chased them. They caught up with the Israelites as they camped by the sea. The Israelites were near Pi Hahiroth, across from Baal Zephon.

10As Pharaoh approached, the Israelites looked back. There were the Egyptians marching after them! The Israelites were terrified. They cried out to the Lord. 11They said to Moses, “Why did you bring us to the desert to die? Weren’t there any graves in Egypt? What have you done to us by bringing us out of Egypt? 12We told you in Egypt, ‘Leave us alone. Let us serve the Egyptians.’ It would have been better for us to serve the Egyptians than to die here in the desert!”

13Moses answered the people. He said, “Don’t be afraid. Stand firm. You will see how the Lord will save you today. Do you see those Egyptians? You will never see them again. 14The Lord will fight for you. Just be still.”

15Then the Lord spoke to Moses. He said, “Why are you crying out to me? Tell the people of Israel to move on. 16Hold out your walking stick. Reach out your hand over the Red Sea to divide the water. Then the people can go through the sea on dry ground. 17I will make the Egyptians stubborn. They will go in after the Israelites. I will gain glory for myself because of what will happen to Pharaoh, his army, chariots and horsemen. 18The Egyptians will know that I am the Lord. I will gain glory because of what will happen to Pharaoh, his chariots and his horsemen.”

19The angel of God had been traveling in front of Israel’s army. Now he moved back and went behind them. The pillar of cloud also moved away from in front of them. Now it stood behind them. 20It came between the armies of Egypt and Israel. All through the night the cloud brought darkness to one side and light to the other. Neither army went near the other all night long.

21Then Moses reached out his hand over the Red Sea. All that night the Lord pushed the sea back with a strong east wind. He turned the sea into dry land. The waters were divided. 22The people of Israel went through the sea on dry ground. There was a wall of water on their right side and on their left.

23The Egyptians chased them. All Pharaoh’s horses and chariots and horsemen followed them into the sea. 24Near the end of the night the Lord looked down from the pillar of fire and cloud. He saw the Egyptian army and threw it into a panic. 25He jammed the wheels of their chariots. That made the chariots hard to drive. The Egyptians said, “Let’s get away from the Israelites! The Lord is fighting for Israel against Egypt.”

26Then the Lord spoke to Moses. He said, “Reach out your hand over the sea. The waters will flow back over the Egyptians and their chariots and horsemen.” 27So Moses reached out his hand over the sea. At sunrise the sea went back to its place. The Egyptians tried to run away from the sea. But the Lord swept them into it. 28The water flowed back and covered the chariots and horsemen. It covered the entire army of Pharaoh that had followed the people of Israel into the sea. Not one of the Egyptians was left.

29But the Israelites went through the sea on dry ground. There was a wall of water on their right side and on their left. 30That day the Lord saved Israel from the power of Egypt. The Israelites saw the Egyptians lying dead on the shore. 31The Israelites saw the amazing power the Lord showed against the Egyptians. So the Israelites had great respect for the Lord and put their trust in him. They also put their trust in his servant Moses.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 14:1-31

1Kenaka Yehova anati kwa Mose, 2“Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. 3Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’ 4Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.

5Farao, mfumu ya Igupto atamva kuti anthu aja athawa, iye pamodzi ndi nduna zake anasintha maganizo awo pa Israeli ndipo anati, “Ife tachita chiyani? Tawalola Aisraeli kuti apite ndi kuleka kutitumikira?” 6Choncho anakonzetsa galeta lake ndipo ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake. 7Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo. 8Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika. 9Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.

10Tsono Farao anayandikira. Ndipo Aisraeli ataona kuti Aigupto akuwatsatira, anachita mantha aakulu ndipo anafuwula kwa Yehova. 11Iwo anafunsa Mose kuti, “Kodi nʼchifukwa chakuti kunalibe manda ku dziko la Igupto kuti iwe utibweretse muno mʼchipululu kuti tidzafe? Chimene watichitachi nʼchiyani, kutitulutsa mʼdziko la Igupto? 12Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, ‘Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.”

13Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso. 14Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete.”

15Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Chifukwa chiyani ukufuwulira kwa ine? Uwuze Aisraeli aziyenda. 16Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma. 17Ine ndidzawumitsa mitima ya Aigupto kotero kuti adzatsatirabe Aisraeli. Ndipo ine ndikadzagonjetsa Farao ndi asilikali ake onse ankhondo, okwera magaleta ndi akavalo, ndidzapeza ulemerero. 18Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova akadzaona mmene ndipambanire Farao ndi magaleta ndi owayendetsa ake.”

19Ndipo mngelo wa Mulungu amene amayenda patsogolo pa gulu lankhondo la Israeli anachoka ndi kupita kumbuyo kwawo. Chipilala cha mtambo chinasunthanso kuchoka kutsogolo ndi kupita kumbuyo kwawo. 20Choncho mtambowo unakhala pakati pa asilikali ankhondo a dziko la Igupto ndi a dziko la Israeli. Choncho panali mdima motero kuti magulu awiri ankhondowa sanathe kuyandikizana usiku wonse.

21Kenaka Mose anatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo Yehova pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kummawa imene inawomba usiku wonse anabweza madzi ndi kuwumitsa nyanja ija. Choncho nyanja ija inagawanika. 22Ndipo Aisraeli anawoloka pakati pa nyanja powuma, madzi atasanduka khoma kumanja ndi kumanzere kwawo.

23Aigupto onse, Farao, ndi onse okwera pa magaleta ndi akavalo anawalondola ndipo analowa mʼmadzi. 24Kutatsala pangʼono kucha, Yehova ali mu chipilala chamoto ndi chamtambo, anayangʼana asilikali ankhondo a Igupto ndipo anabweretsa chisokonezo pakati pawo. 25Yehova anamanga matayala a magaleta kotero kuti ankavutika kuyenda. Ndipo Aigupto anati, “Tiyeni tiwathawe Aisraeli! Yehova akuwamenyera nkhondo kulimbana nafe.”

26Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasula dzanja lako pa nyanja kuti madzi amize Aigupto ndi magaleta awo ndi okwera pa akavalo.” 27Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo. 28Madzi anabwerera ndi kumiza magaleta ndi okwera akavalo, asilikali ankhondo onse amene anatsatira Aisraeli mʼnyanja, palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka.

29Koma Aisraeli aja anawoloka nyanja pansi pali powuma, madzi atachita khoma kumanja ndi kumanzere kwawo. 30Tsiku limeneli Yehova anapulumutsa Israeli mʼmanja mwa Aigupto ndipo Israeli anaona Aigupto ali lambalamba mʼmbali mwa nyanja atafa 31Choncho Aisraeli anaona dzanja lamphamvu la Yehova limene linagonjetsa Aigupto aja, ndipo iwo anaopa Yehova ndi kumukhulupirira pamodzi ndi mtumiki wake Mose.