1 Chronicles 11 – NIRV & CCL

New International Reader’s Version

1 Chronicles 11:1-47

David Becomes King Over Israel

1The whole community of Israel came together to see David at Hebron. They said, “We are your own flesh and blood. 2In the past, Saul was our king. But you led the men of Israel in battle. The Lord your God said to you, ‘You will be the shepherd over my people Israel. You will become their ruler.’ ”

3All the elders of Israel came to see King David at Hebron. There he made a covenant with them in front of the Lord. They anointed David as king over Israel. It happened just as the Lord had promised through Samuel.

David Captures Jerusalem

4David and all the men of Israel marched to Jerusalem. Jerusalem was also called Jebus. The Jebusites who lived there 5said to David, “You won’t get in here.” But David captured the fort of Zion. It became known as the City of David.

6David had said, “Anyone who leads the attack against the Jebusites will become the commander of Israel’s army.” Joab went up first. So he became the commander of the army. He was the son of Zeruiah.

7David moved into the fort. So it was called the City of David. 8He built up the city around the fort. He filled in the low places. He built a wall around it. During that time, Joab built up the rest of the city. 9David became more and more powerful. That’s because the Lord who rules over all was with him.

David’s Mighty Warriors

10The chiefs of David’s mighty warriors and the whole community of Israel helped David greatly. They helped him become king over the entire land. That’s exactly what the Lord had promised him. 11Here is a list of David’s mighty warriors.

Jashobeam was chief of the officers. He was a Hakmonite. He used his spear against 300 men. He killed all of them at one time.

12Next to him was Eleazar. He was one of the three mighty warriors. He was the son of Dodai, the Ahohite. 13Jashobeam was with David at Pas Dammim. The Philistines had gathered there for battle. Israel’s troops ran away from the Philistines. At the place where that happened, there was a field full of barley. 14The three mighty warriors took their stand in the middle of the field. They didn’t let the Philistines capture it. They struck them down. The Lord helped them win a great battle.

15David was near the rock at the cave of Adullam. Three of the 30 chiefs came down to him there. A group of Philistines was camped in the Valley of Rephaim. 16At that time David was in his usual place of safety. Some Philistine troops were stationed at Bethlehem. 17David really wanted some water. He said, “I wish someone would get me a drink of water from the well near the gate of Bethlehem!” 18So the three mighty warriors fought their way past the Philistine guards. They got some water from the well near the gate of Bethlehem. They took the water back to David. But David refused to drink it. Instead, he poured it out as a drink offering to the Lord. 19“I would never drink that water!” David said. “It would be like drinking the blood of these men. They put their lives in danger by going to Bethlehem.” The men had put their lives in danger by bringing the water back. So David wouldn’t drink it.

Those were some of the brave things the three mighty warriors did.

20Abishai was chief over the three mighty warriors. He was the brother of Joab. Abishai used his spear against 300 men. He killed all of them. So he became as famous as the three mighty warriors. 21He was honored twice as much as the three mighty warriors. He became their commander. But he wasn’t included among them.

22Benaiah was a great hero from Kabzeel. He was the son of Jehoiada. Benaiah did many brave things. He struck down two of Moab’s best fighting men. He also went down into a pit on a snowy day. He killed a lion there. 23And Benaiah struck down an Egyptian who was seven and a half feet tall. The Egyptian was holding a spear as big as a weaver’s rod. Benaiah went out to fight against him with a club. He grabbed the spear out of the Egyptian’s hand. Then he killed him with it. 24Those were some of the brave things Benaiah, the son of Jehoiada, did. He too was as famous as the three mighty warriors. 25He was honored more than any of the 30 chiefs. But he wasn’t included among the three mighty warriors. And David put him in charge of his own personal guards.

26Here is a list of David’s mighty warriors.

Asahel, the brother of Joab

Elhanan, the son of Dodo, from Bethlehem

27Shammoth, the Harorite

Helez, the Pelonite

28Ira, the son of Ikkesh, from Tekoa

Abiezer from Anathoth

29Sibbekai, the Hushathite

Ilai, the Ahohite

30Maharai from Netophah

Heled, the son of Baanah, from Netophah

31Ithai, the son of Ribai, from Gibeah in Benjamin

Benaiah from Pirathon

32Hurai from the valleys of Gaash

Abiel, the Arbathite

33Azmaveth, the Baharumite

Eliahba, the Shaalbonite

34the sons of Hashem, the Gizonite

Jonathan, the son of Shagee, the Hararite

35Ahiam, the son of Sakar, the Hararite

Eliphal, the son of Ur

36Hepher, the Mekerathite

Ahijah, the Pelonite

37Hezro from Carmel

Naarai, the son of Ezbai

38Joel, the brother of Nathan

Mibhar, the son of Hagri

39Zelek from Ammon

Naharai, from Beeroth, who carried the armor of Joab, the son of Zeruiah

40Ira, the Ithrite

Gareb, the Ithrite

41Uriah, the Hittite

Zabad, the son of Ahlai

42Adina, the son of Shiza, the Reubenite, who was chief of the Reubenites and the 30 men with him

43Hanan, the son of Maakah

Joshaphat, the Mithnite

44Uzzia, the Ashterathite

Shama and Jeiel, the sons of Hotham from Aroer

45Jediael, the son of Shimri

his brother Joha, the Tizite

46Eliel, the Mahavite

Jeribai and Joshaviah, the sons of Elnaam

Ithmah from Moab

47Eliel

Obed

Jaasiel, the Mezobaite

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 11:1-47

Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli

1Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife abale anu. 2Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”

3Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.

Davide Agonjetsa Yerusalemu

4Davide ndi Aisraeli onse anapita ku Yerusalemu (ku Yebusi). Ayebusi amene ankakhala kumeneko 5anamuwuza Davide kuti, “Simulowa muno.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.

6Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali.

7Tsono Davide anakhazikika mu lingamo, ndipo mzindawu anawutcha Mzinda wa Davide. 8Iye anamanga malo onse ozungulira, kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Ndipo Yowabu anakonzanso mbali ina ya mzindawu. 9Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Asilikali Otchuka a Davide

10Awa ndiye anali atsogoleri amphamvu a Davide. Iwo pamodzi ndi Aisraeli onse, anathandiza kulimbikitsa ufumu wake kuti ukwanire madera onse, monga momwe Yehova analonjezera. 11Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide:

Yasobeamu Mhakimoni anali mkulu wa atsogoleri. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300 nthawi imodzi.

12Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi, mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu. 13Iye anali ndi Davide ku Pasi-Damimu pamene Afilisti anasonkhana kudzachita nkhondo. Ankhondo anathawa Afilistiwo pamalo pamene panali munda wodzaza ndi barele. 14Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.

15Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu. 16Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. 17Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!” 18Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. 19Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe.

Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.

20Abisai mʼbale wa Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300. Choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja. 21Iye analandira ulemu woposa atatuwo. Kotero anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti iyeyo sanali mʼgulu la anthu atatu aja.

22Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango. 23Ndipo iye anakanthanso Mwigupto amene anali wotalika mamita awiri ndi theka. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo wofanana ndi ndodo yowombera nsalu mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe. 24Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja. 25Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.

26Ankhondo amphamvuwa anali:

Asaheli mʼbale wa Yowabu,

Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

27Samoti Mharori,

Helezi Mpeloni.

28Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,

Abiezeri wa ku Anatoti,

29Sibekai Mhusati,

Ilai Mwahohi,

30Maharai Mnetofa,

Heledi mwana wa Baana Mnetofa,

31Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini,

Benaya Mpiratoni,

32Hurai wa ku zigwa za Gaasi,

Abieli Mwaribati,

33Azimaveti Mbaharumi,

Eliyahiba Msaaliboni,

34ana a Hasemu Mgizoni,

Yonatani mwana wa Sage Mharari,

35Ahiamu mwana wa Sakari Mharari,

Elifali mwana wa Uri,

36Heferi Mmekerati,

Ahiya Mpeloni,

37Heziro wa ku Karimeli

Naara mwana wa Ezibai,

38Yoweli mʼbale wa Natani,

Mibihari mwana wa Hagiri,

39Zeleki Mwamoni,

Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya.

40Ira Mwitiri,

Garebu Mwitiri,

41Uriya Mhiti,

Zabadi mwana wa Ahilai,

42Adina mwana wa Siza Mrubeni, amene anali mtsogoleri wa Arubeni ndi anthu makumi atatu pamodzi naye,

43Hanani mwana wa Maaka,

Yehosafati Mmitini,

44Uziya Mwasiterati,

Sama ndi Yeiyeli ana a Hotamu Mwaroeri,

45Yediaeli mwana wa Simiri,

ndi Yoha Mtizi mʼbale wake,

46Elieli Mhavati,

Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu,

Itima Mmowabu,

47Elieli, Obedi ndi Yaasieli Mmeobai.