Yeremia 16 – NEN & CCL

Kiswahili Contemporary Version (Neno: Bibilia Takatifu)

Yeremia 16:1-21

Siku Ya Maafa

1Kisha neno la Bwana likanijia: 216:2 Mwa 19:14; Mt 19:12; 1Kor 7:26-27“Kamwe usioe na kuwa na wana wala binti mahali hapa.” 316:3 Yer 6:21Kwa maana hili ndilo asemalo Bwana kuhusu wana na binti wazaliwao katika nchi hii, na kuhusu wale wanawake ambao ni mama zao, na wale wanaume ambao ni baba zao: 416:4 Yer 25:33; 9:22; Za 83:10; Kum 28:26; Za 79:1-3; Yer 14:15; 19:7“Watakufa kwa magonjwa ya kufisha. Hawataombolezewa wala kuzikwa, lakini watakuwa kama mavi yaliyosambaa juu ya ardhi. Watakufa kwa upanga na kwa njaa, nazo maiti zao zitakuwa chakula cha ndege wa angani, na cha wanyama wa nchi.”

5Kwa kuwa hili ndilo asemalo Bwana: “Usiingie katika nyumba ambayo kuna chakula cha matanga, usiende kuwaombolezea wala kuwahurumia, kwa sababu nimeziondoa baraka zangu, upendo wangu na huruma zangu kutoka kwa watu hawa,” asema Bwana. 616:6 Yer 9:21; Eze 9:5-6; Law 19:28; 21:5; Isa 22:12; 1:20“Wakubwa na wadogo watakufa katika nchi hii. Hawatazikwa wala kuombolezewa, na hakuna atakayejikatakata au kunyoa nywele za kichwa chake kwa ajili yao. 716:7 Mit 3:6; Eze 24:17; Hos 9:4; 2Sam 3:35; Yer 22:10; Mao 1:9, 16Hakuna yeyote atakayewapa chakula ili kuwafariji wale waombolezao kwa ajili ya wale waliokufa, hata akiwa amefiwa na baba au mama, wala hakuna yeyote atakayewapa kinywaji ili kuwafariji.

816:8 Kut 32:6; Mhu 7:2-4; Yer 15:17“Usiingie katika nyumba ambayo kuna karamu, na kuketi humo ili kula na kunywa. 916:9 Isa 51:3; Amo 6:4-7; Yer 7:34; Isa 22:12-14; Ufu 18:23; Eze 26:13Kwa kuwa hili ndilo asemalo Bwana Mwenye Nguvu Zote, aliye Mungu wa Israeli: ‘Mbele ya macho yako na katika siku zako, nitakomesha sauti zote za shangwe na za furaha, na pia sauti za bibi arusi na bwana arusi mahali hapa.’

1016:10 Kum 29:24; Yer 5:19“Utakapowaambia watu hawa mambo haya yote na wakakuuliza, ‘Kwa nini Bwana ameamuru maafa makubwa kama haya dhidi yetu? Tumefanya kosa gani? Tumetenda dhambi gani dhidi ya Bwana, Mungu wetu?’ 1116:11 Amu 2:12-13; Za 106:35-43; 1Fal 9:9; Neh 9:26-29; Ay 31:27; Kum 29:25-26Basi waambie, ‘Ni kwa sababu baba zenu waliniacha mimi, wakafuata miungu mingine ili kuitumikia na kuiabudu. Waliniacha mimi na hawakuishika sheria yangu,’ asema Bwana. 1216:12 Kut 32:8; Amo 2:4; Mhu 9:3; Yer 13:10; 2Tim 3:13; Yer 7:26; Eze 20:30‘Lakini ninyi mmetenda uovu zaidi kuliko baba zenu. Tazama jinsi ambavyo kila mmoja wenu anafuata ukaidi wa moyo wake mbaya, badala ya kunitii mimi. 1316:13 Kum 4:26-28; Yer 15:4-5; 2Nya 20:7; Yer 5:19; Kum 28:36Kwa hiyo nitawaondoa katika nchi hii na kuwatupa katika nchi ambayo ninyi wala baba zenu hamkuijua, nako huko mtaitumikia miungu mingine usiku na mchana, kwa maana sitawapa fadhili zangu huko.’

1416:14 Kum 15:15; Yer 23:7-8; 29:10; 31:27, 38; 30:3“Hata hivyo, siku zinakuja,” asema Bwana, “wakati ambapo watu hawatasema tena, ‘Hakika kama Bwana aishivyo, aliyewapandisha Waisraeli kutoka Misri,’ 1516:15 Isa 11:11-12; Za 53:6; Yer 3:18; 23:8; 30:3; Eze 38:14; Yoe 3:1; Kum 30:3bali watasema, ‘Hakika kama Bwana aishivyo, aliyewatoa wana wa Israeli kutoka nchi ya kaskazini na nchi zote alizokuwa amewafukuzia.’ Maana nitawarudisha katika nchi niliyowapa baba zao.

1616:16 Amo 4:2; Hab 1:14-15; Amo 9:3; Mik 7:2; 1Sam 26:20“Lakini sasa nitawaagiza wavuvi wengi,” asema Bwana, “nao watawavua. Baada ya hilo, nitawaagizia wawindaji wengi, nao watawawinda kwenye kila mlima na kilima, na katika nyufa za miamba. 1716:17 Mhu 12:14; Mk 4:22; Mit 5:21; Sef 1:12; Yer 32:19; Mwa 3:8; Ebr 4:13Macho yangu yanaziona njia zao zote, hazikufichika kwangu, wala dhambi yao haikusitirika. 1816:18 Hes 35:34; Isa 40:2; Eze 43:7; Ufu 18:6; Isa 65:6; Yer 12:3; Za 101:3Nitawalipiza maradufu kwa ajili ya uovu wao na dhambi yao, kwa sababu wameinajisi nchi yangu kwa maumbo yasiyo na uhai ya vinyago vyao vibaya, na kuujaza urithi wangu na sanamu za kuchukiza.”

1916:19 Yer 3:17; Za 4:2; Isa 2:2; Za 18:2; 2Sam 22:3; Yer 14:22; Isa 40:19; 1Sam 12:21Ee Bwana, nguvu zangu na ngome yangu,

kimbilio langu wakati wa taabu,

kwako mataifa yatakujia

kutoka miisho ya dunia na kusema,

“Baba zetu hawakuwa na chochote zaidi ya miungu ya uongo,

sanamu zisizofaa kitu

ambazo hazikuwafaidia lolote.

2016:20 Isa 37:19; Rum 1:23; Gal 4:8; Za 115:4-7; Yer 2:11Je, watu hujitengenezea miungu yao wenyewe?

Naam, lakini hao si miungu!”

2116:21 Kut 3:15“Kwa hiyo nitawafundisha:

wakati huu nitawafundisha

nguvu zangu na uwezo wangu.

Ndipo watakapojua

kuwa Jina langu ndimi Bwana.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 16:1-21

Tsiku la Masautso

1Kenaka Yehova anandiwuza kuti, 2“Usadzakwatire ndi kubereka ana aamuna kapena aakazi malo ano 3pakuti ana aamuna ndi ana aakazi obadwira mʼdziko muno, komanso amayi awo ndi abambo awo amene anabereka anawo mʼdziko muno, 4adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzawalira maliro kapena kuyikidwa mʼmanda koma adzakhala ngati ndowe zotayikira pansi. Ena adzaphedwa ku nkhondo ndipo ena adzafa ndi njala. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo.”

5Yehova akuti, “Usalowe mʼnyumba ya maliro; usapite kukalira maliro kapena kukapepesa, chifukwa Ine ndawachotsera madalitso anga, chikondi changa ndi chifundo changa.” 6Akuluakulu ndi angʼonoangʼono omwe adzafa mʼdziko muno. Sadzayikidwa mʼmanda kapena kuliridwa, ndipo palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi lake chifukwa cha iwo. 7Palibe amene adzapereka chakudya kutonthoza amene akulira maliro, ngakhale kuti womwalirayo ndi abambo ake kapena amayi ake.

8“Ndipo usalowe mʼnyumba mmene muli madyerero, nʼkukhala pansi ndi kudya ndi kumwa nawo. 9Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Pa nthawi yanu, inu mukuona ndidzathetsa mawu achimwemwe ndi achisangalalo ndiponso mawu a mkwati ndi mkwatibwi pa malo ano.’

10“Ukawawuza anthu awa zinthu zonsezi akakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wanena kuti tsoka lalikulu lotere lidzatigwere? Kodi talakwa chiyani? Kodi tamuchimwira tchimo lotani Yehova Mulungu wathu?’ 11Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa. 12Komanso inu munachimwa kwambiri kupambana makolo anu. Aliyense wa inu akutsatira zoyipa ndi mtima wake wokanikawo mʼmalo mondimvera Ine. 13Choncho Ine ndidzakubalalitsani mʼdziko muno ndi kukulowetsani mʼdziko limene inu ndi makolo anu simunalidziwe. Kumeneko mukatumikira milungu ina usana ndi usiku, ndipo sadzakuchitirani chifundo.’ ”

14Yehova akuti, “Komabe masiku akubwera pamene anthu polumbira sadzatinso, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto,’ 15koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku mayiko onse kumene anawabalalitsirako.’ Pakuti ndidzawabwezera ku dziko limene ndinalipereka kwa makolo awo.”

16Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe. 17Maso anga akuona makhalidwe awo onse; sanabisike pamaso panga. Palibe tchimo limene sindikulidziwa. 18Ndidzawalanga mowirikiza chifukwa cha kuyipa kwawo ndi tchimo lawo. Ndidzatero chifukwa ayipitsa dziko langa ndi mafano awo amene ali ngati mitembo, ndiponso adzaza cholowa changa ndi mafano awo onyansa.”

19Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga ndi linga langa,

pothawirapo panga nthawi ya masautso,

anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu

kuchokera ku mathero onse a dziko lapansi ndipo adzanena kuti,

“Makolo anthu anali ndi milungu yonama,

anali ndi mafano achabechabe amene sanawathandize.

20Kodi anthu nʼkudzipangira milungu?

Atati atero ndiye kuti imeneyo ikhala milungu yachabechabe.”

21“Choncho Ine ndidzawaphunzitsa,

kokha kano kuti adziwe

za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga.

Pamenepo adzadziwa kuti

dzina langa ndi Yehova.