1 Corintios 10 – NVI & CCL

Nueva Versión Internacional

1 Corintios 10:1-33

Advertencias basadas en la historia de Israel

1No quiero que desconozcan, hermanos, que nuestros antepasados estuvieron todos bajo la nube y que todos atravesaron el mar. 2Todos ellos fueron bautizados en la nube y en el mar para unirse a Moisés. 3Todos también comieron el mismo alimento espiritual 4y tomaron la misma bebida espiritual, pues bebían de la roca espiritual que los acompañaba, y la roca era Cristo. 5Sin embargo, la mayoría de ellos no agradaron a Dios y sus cuerpos quedaron tendidos en el desierto.

6Todo eso sucedió para servirnos de ejemplo, a fin de que no nos apasionemos por lo malo, como lo hicieron ellos. 7No sean idólatras como lo fueron algunos de ellos, según está escrito: «Se sentó el pueblo a comer y a beber, y se levantó para entregarse al desenfreno».10:7 Éx 32:6. 8No cometamos inmoralidad sexual como algunos lo hicieron, por lo que en un solo día perecieron veintitrés mil. 9Tampoco pongamos a prueba a Cristo como lo hicieron algunos y murieron víctimas de las serpientes. 10Tampoco murmuren contra Dios como lo hicieron algunos y sucumbieron a manos del exterminador.

11Todo eso les sucedió para servir de ejemplo y quedó escrito para advertencia nuestra, pues a nosotros nos ha llegado el fin de los tiempos. 12Por lo tanto, si alguien piensa que está firme, tenga cuidado de no caer. 13Ustedes no han sufrido ninguna tentación que no sea común al género humano. Pero Dios es fiel y no permitirá que ustedes sean tentados más allá de lo que puedan aguantar. Más bien, cuando llegue la tentación, él les dará también una salida a fin de que puedan resistir.

Las fiestas idólatras y la Cena del Señor

14Por tanto, mis queridos hermanos, huyan de la idolatría. 15Me dirijo a personas sensatas; juzguen ustedes mismos lo que digo. 16Esa copa de bendición por la cual damos gracias,10:16 por la cual damos gracias. Lit. que bendecimos. ¿no significa que entramos en comunión con la sangre de Cristo? Ese pan que partimos, ¿no significa que entramos en comunión con el cuerpo de Cristo? 17Hay un solo pan del cual todos participamos; por eso, aunque somos muchos, formamos un solo cuerpo.

18Consideren al pueblo de Israel: ¿No entran en comunión con el altar los que comen de lo sacrificado? 19¿Qué quiero decir con esta comparación? ¿Que el sacrificio que los no judíos ofrecen a los ídolos sea algo o que el ídolo mismo sea algo? 20No, sino que cuando ellos ofrecen sacrificios, lo hacen para los demonios, no para Dios; y no quiero que ustedes entren en comunión con los demonios. 21No pueden beber de la copa del Señor y también de la copa de los demonios; no pueden participar de la mesa del Señor y también de la mesa de los demonios. 22¿O vamos a provocar celos al Señor? ¿Somos acaso más fuertes que él?

La libertad del creyente

23«Todo está permitido», pero no todo es provechoso. «Todo está permitido», pero no todo es constructivo. 24Que nadie busque sus propios intereses, sino los del prójimo.

25Coman de todo lo que se vende en la carnicería, sin preguntar nada por motivos de conciencia, 26porque «del Señor es la tierra y todo cuanto hay en ella».10:26 Sal 24:1.

27Si algún incrédulo los invita a comer y ustedes aceptan la invitación, coman de todo lo que sirvan sin preguntar nada por motivos de conciencia. 28Ahora bien, si alguien les dice: «Esto ha sido ofrecido en sacrificio a los ídolos», entonces no lo coman, por consideración al que se lo mencionó y por motivos de conciencia.10:28 conciencia. Var. conciencia, porque «del Señor es la tierra y todo cuanto hay en ella». 29Me refiero a la conciencia del otro, no a la de ustedes. ¿Por qué se ha de juzgar mi libertad de acuerdo con la conciencia ajena? 30Si con gratitud participo de la comida, ¿me van a condenar por comer algo por lo cual doy gracias a Dios?

31En conclusión, ya sea que coman o beban o hagan cualquier otra cosa, háganlo todo para la gloria de Dios. 32No hagan tropezar a nadie, ni a judíos, ni a los que no son judíos, ni a la iglesia de Dios. 33Hagan como yo, que procuro agradar a todos en todo. No busco mis propios intereses, sino los de los demás, para que sean salvos.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 10:1-33

Chenjezo Kuchokera Mʼmbiri ya Israeli

1Pakuti sindikufuna kuti inu mukhale osadziwa zenizeni, abale, kuti makolo athu anatsogozedwa ndi mtambo ndikuti onse anawoloka nyanja. 2Ndipo onse anabatizidwa mwa Mose mu mtambo ndi mʼnyanja. 3Onse anadya chakudya chimodzi chauzimu 4ndipo anamwa chakumwa chimodzi chauzimu; popeza anamwa kuchokera mʼthanthwe lomwe anayenda nalo, ndipo thanthwe limeneli linali Khristu. 5Ngakhale zinali choncho, Mulungu sanakondwere ndi ambiri a iwo, motero ambiri mwa iwo anafera mʼchipululu.

6Tsono zinthu izi zinachitika kuti zikhale chitsanzo, kuti ife tisayike mitima yathu pa zinthu zoyipa monga anachitira makolo athuwo. 7Musakhale anthu opembedza mafano, monga analili ena mwa iwo. Pakuti zalembedwa kuti, “Anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.” 8Tisachite chigololo monga ena mwa iwo anachitira ndipo tsiku limodzi anafapo anthu 23,000. 9Tisamuyese Khristu, monga ena mwa iwo anachitira ndipo anaphedwa ndi njoka. 10Ndipo osamawiringula, monga ena mwa iwo anachitira naphedwa ndi mngelo wowononga.

11Zinthu izi zinawachitikira kuti zikhale chitsanzo ndipo zinalembedwa kuti zikhale chenjezo kwa ife, amene tiyandikira nthawi ya kutha kwa zonse. 12Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe! 13Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.

Maphwando a Mafano ndi Mgonero wa Ambuye

14Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano. 15Ndikuyankhula kwa a anthu anzeru zawo, nokha muweruze pa zimene ndikunenazi. 16Pamene tidalitsa chikho cha Mgonero wa Ambuye, mothokoza Mulungu, kodi sitikugawana magazi a Khristu? Nanga buledi amene timanyemayo, kodi sitikugawana thupi la Khristu? 17Pakuti buledi ndi mmodzi yekha, ifenso ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, popeza tonse timagawana buledi mmodzi yemweyo.

18Taganizirani zimene amachita Aisraeli. Kodi onse amene amadya zoperekedwa nsembe, samachita nawo miyambo ya pa guwapo? 19Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse? 20Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. 21Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. 22Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?

Ufulu wa Munthu Wokhulupirira

23Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza. 24Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.

25Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 26Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”

27Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 28Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima. 29Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina? 30Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?

31Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. 33Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.