ማቴዎስ 7 – NASV & CCL

New Amharic Standard Version

ማቴዎስ 7:1-29

በሌሎች ላይ አለመፍረድ

7፥3-5 ተጓ ምብ – ሉቃ 6፥4142

1“እንዳይፈረድባችሁ በማንም ሰው ላይ አትፍረዱ፤ 2በምትፈርዱበትም ዐይነት ይፈረድባችኋል፤ በምትሰፍሩበትም መስፈሪያ ይሰፈርላችኋል።

3“በዐይንህ ውስጥ ያለውን ግንድ ሳትመለከት፣ በወንድምህ ዐይን ያለውን ጕድፍ ለምን ታያለህ? 4በዐይንህ ውስጥ ግንድ እያለ ወንድምህን፣ ‘ዐይንህ ውስጥ ያለውን ጕድፍ ላውጣልህ’ ማለት እንዴት ትችላለህ? 5አንተ ግብዝ፤ አስቀድመህ በዐይንህ ውስጥ ያለውን ግንድ አውጣ፤ ከዚያም በወንድምህ ዐይን ውስጥ ያለውን ጕድፍ ለማውጣት አጥርተህ ታያለህ።

6“በእግራቸው እንዳይረግጡት፣ ተመልሰውም ነክሰው እንዳይቦጫጭቋችሁ፣ የተቀደሰ ነገር ለውሾች አትስጡ፤ ዕንቈቻችሁንም በዕሪያ ፊት አትጣሉ።

ለምኑ፤ ፈልጉ፤ አንኳኩ

7፥7-11 ተጓ ምብ – ሉቃ 11፥9-13

7“ለምኑ፣ ይሰጣችኋል፤ ፈልጉ፣ ታገኛላችሁ፤ አንኳኩ፣ በሩም ይከፈትላችኋል። 8የሚለምን ሁሉ ይሰጠዋል፤ የሚፈልግም ያገኛል፤ ለሚያንኳኳም በሩ ይከፈትለታል።

9“ከእናንተ መካከል ልጁ ዳቦ ቢለምነው፣ ድንጋይ የሚሰጥ አባት አለ? 10ወይም ዓሣ ቢለምነው እባብ የሚሰጥ ይኖራልን? 11ታዲያ እናንት ክፉዎች ሳላችሁ ለልጆቻችሁ መልካም ስጦታ መስጠት ካወቃችሁ፣ የሰማዩ አባታችሁማ ለሚለምኑት መልካም ስጦታን እንዴት አብልጦ አይሰጣቸውም? 12ሌሎች እንዲያደርጉላችሁ የምትፈልጉትን ነገር እናንተም አድርጉላቸው፤ ኦሪትም፣ ነቢያትም በዚህ ይጠቃለላሉና።

ጠባቡና ሰፊው በር

13“በጠባቡ በር ግቡ፤ ወደ ጥፋት የሚወስደው መንገድ ትልቅ፣ በሩም ሰፊ ነውና፤ ብዙዎችም በዚያ ይገባሉ። 14ወደ ሕይወት የሚያደርሰው ግን መንገዱ ቀጭን፣ በሩም ጠባብ ነው፤ የሚገቡበትም ጥቂቶች ብቻ ናቸው።

ሐሰተኛ ነቢያት

15“በውስጣቸው ነጣቂ ተኵላዎች ሆነው ሳሉ የበግ ለምድ ለብሰው መካከላችሁ በመግባት ከሚያሸምቁ ሐሰተኛ ነቢያት ተጠንቀቁ። 16ከፍሬያቸው ታውቋቸዋላችሁ፤ ከእሾኽ ቍጥቋጦ ወይን፣ ከኵርንችትስ በለስ ይለቀማልን? 17እንዲሁም ጥሩ ዛፍ ሁሉ ጥሩ ፍሬ፣ መጥፎ ዛፍ ግን መጥፎ ፍሬ ያፈራል። 18ጥሩ ዛፍ መጥፎ ፍሬ፣ መጥፎም ዛፍ ጥሩ ፍሬ ማፍራት አይችልም። 19ጥሩ ፍሬ የማያፈራ ዛፍ ሁሉ ይቈረጣል፤ ወደ እሳትም ይጣላል። 20ስለዚህ በፍሬአቸው ታውቋቸዋላችሁ።

21“በሰማይ ያለውን የአባቴን ፈቃድ ሳይፈጽም ‘ጌታ ሆይ፤ ጌታ ሆይ፤’ የሚለኝ ሁሉ ወደ መንግሥተ ሰማይ አይገባም። 22በዚያ ቀን ብዙዎች፣ ‘ጌታ ሆይ፤ ጌታ ሆይ፤ በስምህ ትንቢት አልተናገርንምን? በስምህ አጋንንት አላወጣንምን? በስምህስ ብዙ ታምራት አላደረግንምን?’ ይሉኛል። 23በዚያ ጊዜ፣ ‘ከቶ አላወቅኋችሁም፤ እናንት ክፉዎች፤ ከእኔ ራቁ’ ብዬ በግልጽ እነግራቸዋለሁ።

ብልኁና ሞኙ ቤት ሠሪ

7፥24-27 ተጓ ምብ – ሉቃ 6፥47-49

24“እንግዲህ ይህን ቃሌን ሰምቶ በተግባር የሚያውል፣ ቤቱን በዐለት ላይ የሠራን ብልኅ ሰው ይመስላል። 25ዶፍ ወረደ፤ ጐርፍም ጐረፈ፤ ነፋስም ነፈሰ፤ ያንን ቤት መታው፤ በዐለትም ላይ ስለ ተመሠረተ አልወደቀም። 26ይህን ቃሌን ሰምቶ በተግባር የማያውለው ግን ቤቱን በአሸዋ ላይ የሠራን ሞኝ ሰው ይመስላል። 27ዶፍ ወረደ፤ ጐርፍም ጐረፈ፤ ነፋስም ነፈሰ፤ ያንን ቤት መታው፤ ቤቱም ወደቀ፤ አወዳደቁም የከፋ ነበር።”

28ኢየሱስ ማስተማሩን በፈጸመ ጊዜ፣ ሕዝቡ በትምህርቱ ተደነቁ። 29ምክንያቱም እንደ አይሁድ ሃይማኖት መምህራናቸው ሳይሆን እንደ ባለ ሥልጣን አስተምሯቸው ስለ ነበር ነው።

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 7:1-29

Za Kuweruza Ena

1“Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe. 2Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo.

3“Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako? 4Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, ‘Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako? 5Wachiphamaso iwe! Yamba wachotsa chimtengo chili mʼdiso mwako ndipo pamenepo udzatha kuona bwino ndi kuchotsa kachitsotso kali mʼdiso mwa mʼbale wako.

6“Musapatse agalu zinthu zopatulika; kapena musaponyere nkhumba ngale zanu. Pakuti ngati mutero, zidzaziponda ndipo pomwepo zidzakutembenukirani ndi kukudulani nthulinthuli.

Pemphani, Funafunani, Gogodani

7“Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. 8Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.

9“Ndani mwa inu, mwana wake akamupempha buledi amamupatsa mwala? 10Kapena ngati mwana apempha nsomba, kodi amamupatsa njoka? 11Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha? 12Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.

Zipata Ziwiri ndi Njira Ziwiri

13“Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. 14Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.

Aneneri Owona ndi Onyenga

15“Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa. 16Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula? 17Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa. 18Mtengo wabwino sungabale chipatso choyipa, ndi mtengo woyipa sungabale chipatso chabwino. 19Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto. 20Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira.

Ophunzira Owona ndi Onyenga

21“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. 22Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ 23Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’

Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa

24“Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga. 27Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”

28Yesu atamaliza kunena zonsezi, magulu a anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, 29chifukwa anaphunzitsa ngati amene anali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo.