The Message

Joshua 1

11-9 After the death of Moses the servant of God, God spoke to Joshua, Moses’ assistant:

“Moses my servant is dead. Get going. Cross this Jordan River, you and all the people. Cross to the country I’m giving to the People of Israel. I’m giving you every square inch of the land you set your foot on—just as I promised Moses. From the wilderness and this Lebanon east to the Great River, the Euphrates River—all the Hittite country—and then west to the Great Sea. It’s all yours. All your life, no one will be able to hold out against you. In the same way I was with Moses, I’ll be with you. I won’t give up on you; I won’t leave you. Strength! Courage! You are going to lead this people to inherit the land that I promised to give their ancestors. Give it everything you have, heart and soul. Make sure you carry out The Revelation that Moses commanded you, every bit of it. Don’t get off track, either left or right, so as to make sure you get to where you’re going. And don’t for a minute let this Book of The Revelation be out of mind. Ponder and meditate on it day and night, making sure you practice everything written in it. Then you’ll get where you’re going; then you’ll succeed. Haven’t I commanded you? Strength! Courage! Don’t be timid; don’t get discouraged. God, your God, is with you every step you take.”

The Taking of the Land

10-11 Then Joshua gave orders to the people’s leaders: “Go through the camp and give this order to the people: ‘Pack your bags. In three days you will cross this Jordan River to enter and take the land God, your God, is giving you to possess.’”

12-15 Then Joshua addressed the Reubenites, the Gadites, and the half-tribe of Manasseh. He said, “Remember what Moses the servant of God commanded you: God, your God, gives you rest and he gives you this land. Your wives, your children, and your livestock can stay here east of the Jordan, the country Moses gave you; but you, tough soldiers all, must cross the River in battle formation, leading your brothers, helping them until God, your God, gives your brothers a place of rest just as he has done for you. They also will take possession of the land that God, your God, is giving them. Then you will be free to return to your possession, given to you by Moses the servant of God, across the Jordan to the east.”

16-18 They answered Joshua: “Everything you commanded us, we’ll do. Wherever you send us, we’ll go. We obeyed Moses to the letter; we’ll also obey you—we just pray that God, your God, will be with you as he was with Moses. Anyone who questions what you say and refuses to obey whatever you command him will be put to death. Strength! Courage!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 1

Yehova Asankha Yoswa Kukhala Mtsogoleri

1Atamwalira Mose mtumiki wa Mulungu, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mthandizi wa Mose: “Mose mtumiki wanga wamwalira. Ndipo iwe ndi anthu onsewa, tsopano konzekani kuwoloka mtsinje wa Yorodani kupita ku dziko limene ndiwapatse Aisraeli onse. Paliponse pamene phazi lanu liponde, ndikupatsani monga momwe ndinalonjezera Mose. Dziko lanu lidzayambira ku chipululu kummwera mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kummawa, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yayikulu ya kumadzulo. Palibe munthu amene adzatha kukugonjetsa masiku onse a moyo wako. Monga Ine ndinakhalira ndi Mose, chomwechonso ndidzakhala nawe. Sindidzakusiya kapena kukataya.

“Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima, chifukwa iwe udzatsogolera anthu awa kukalandira dziko limene Ine ndinalonjeza makolo awo kuti ndidzawapatsa. Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti umvere malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakupatsa. Usachoke pa malamulo anga ndipo kulikonse kumene udzapite udzapambana. Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana. Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

10 Tsono Yoswa analamula atsogoleri a Aisraeli nawawuza kuti, 11 “Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’ ”

12 Koma Yoswa anawuza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti, 13 “Kumbukirani zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani kuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndi dziko ili kuti likhale lanu.’ 14 Tsono akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu zitsale mʼdziko lino limene Mose anakupatsani kummawa kwa Yorodani. Koma ankhondo anu okha ndiwo awoloke atatenga zida zawo ndi kupita patsogolo pa abale anu kukawathandiza. 15 Abale anuwo akadzalandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa monga inu mwachitira, inu mudzabwerera kudzakhazikika mʼdziko lanu limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya la kummawa kwa Yorodani.”

16 Kenaka iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife tidzachita chilichonse chimene mwatilamula, ndipo kulikonse kumene mudzatitume tidzapita. 17 Monga momwe tinamvera Mose kwathunthu, chomwechonso tidzakumvera iwe. Yehova Mulungu wanu akhale nanu monga momwe anachitira ndi Mose. 18 Aliyense wotsutsana ndi inu kapena wosamvera zimene mutilamula adzaphedwa. Inu mukhale wamphamvu ndi wolimba mtima!”