The Message

Hosea 1

1This is God’s Message to Hosea son of Beeri. It came to him during the royal reigns of Judah’s kings Uzziah, Jotham, Ahaz, and Hezekiah. This was also the time that Jeroboam son of Joash was king over Israel.

This Whole Country Has Become a Whorehouse

The first time God spoke to Hosea he said:

“Find a whore and marry her.
    Make this whore the mother of your children.
And here’s why: This whole country
    has become a whorehouse, unfaithful to me, God.”

Hosea did it. He picked Gomer daughter of Diblaim. She got pregnant and gave him a son.

4-5 Then God told him:

“Name him Jezreel. It won’t be long now before
    I’ll make the people of Israel pay for the massacre at Jezreel.
    I’m calling it quits on the kingdom of Israel.
Payday is coming! I’m going to chop Israel’s bows and arrows
    into kindling in the valley of Jezreel.”

6-7 Gomer got pregnant again. This time she had a daughter. God told Hosea:

“Name this one No-Mercy. I’m fed up with Israel.
    I’ve run out of mercy. There’s no more forgiveness.
Judah’s another story. I’ll continue having mercy on them.
    I’ll save them. It will be their God who saves them,
Not their armaments and armies,
    not their horsepower and manpower.”

8-9 After Gomer had weaned No-Mercy, she got pregnant yet again and had a son. God said:

“Name him Nobody. You’ve become nobodies to me,
    and I, God, am a nobody to you.

10-11 “But down the road the population of Israel is going to explode past counting, like sand on the ocean beaches. In the very place where they were once named Nobody, they will be named God’s Somebody. Everybody in Judah and everybody in Israel will be assembled as one people. They’ll choose a single leader. There’ll be no stopping them—a great day in Jezreel!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 1

1Awa ndi mawu amene Yehova anayankhula kwa Hoseya mwana wa Beeri pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda ndiponso pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Yowasi mfumu ya ku Israeli.

Mkazi wa Hoseya ndi Ana Ake

Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.” Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna.

Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli. Tsiku limenelo ndidzathyola uta wa Israeli mʼchigwa cha Yezireeli.”

Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse. Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”

Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri anabereka mwana wina wamwamuna. Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.

10 “Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ 11 Anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Israeli adzasonkhananso pamodzi ndipo adzasankha mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka mʼdzikomo, pakuti tsiku la Yezireeli lidzakhala lalikulu kwambiri.”