The Message

1 John 1

11-2 From the very first day, we were there, taking it all in—we heard it with our own ears, saw it with our own eyes, verified it with our own hands. The Word of Life appeared right before our eyes; we saw it happen! And now we’re telling you in most sober prose that what we witnessed was, incredibly, this: The infinite Life of God himself took shape before us.

3-4 We saw it, we heard it, and now we’re telling you so you can experience it along with us, this experience of communion with the Father and his Son, Jesus Christ. Our motive for writing is simply this: We want you to enjoy this, too. Your joy will double our joy!

Walk in the Light

This, in essence, is the message we heard from Christ and are passing on to you: God is light, pure light; there’s not a trace of darkness in him.

6-7 If we claim that we experience a shared life with him and continue to stumble around in the dark, we’re obviously lying through our teeth—we’re not living what we claim. But if we walk in the light, God himself being the light, we also experience a shared life with one another, as the sacrificed blood of Jesus, God’s Son, purges all our sin.

8-10 If we claim that we’re free of sin, we’re only fooling ourselves. A claim like that is errant nonsense. On the other hand, if we admit our sins—make a clean breast of them—he won’t let us down; he’ll be true to himself. He’ll forgive our sins and purge us of all wrongdoing. If we claim that we’ve never sinned, we out-and-out contradict God—make a liar out of him. A claim like that only shows off our ignorance of God.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yohane 1

Mawu a Moyo

1Tikukulalikirani za Mawu a moyo amene analipo kuyambira pachiyambi, amene tinawamva, amene tinawaona ndi maso athu, amene tinawapenyetsetsa, ndipo tinawakhudza ndi manja athu. Moyowo unaoneka, tinawuona ndipo tikuchitira umboni. Tikukulalikirani za moyo wosatha umene unali ndi Atate ndipo unaonekera kwa ife. Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu. Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu.

Kuyenda mu Kuwunika

Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse. Tikanena kuti timayanjana naye, koma nʼkumayendabe mu mdima, tikunama ndipo sitikuchita choonadi. Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

Kuwulula Machimo ndi Kukhululukidwa

Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi. Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse. 10 Ife tikanena kuti sitinachimwe, tikumutenga Mulungu kukhala wonama, ndipo Mawu ake sali mwa ife.